1 Samueli 18:1-30

  • Ubwenzi wa Davide ndi Yonatani (1-4)

  • Sauli anayamba kuchitira nsanje Davide (5-9)

  • Sauli ankafuna kupha Davide (10-19)

  • Davide anakwatira Mikala mwana wa Sauli (20-30)

18  Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula ndi Sauli, Yonatani+ ndi Davide anayamba kugwirizana kwambiri* moti Yonatani anayamba kukonda Davide ngati mmene ankadzikondera.*+  Kuyambira tsiku limenelo, Sauli sanalolenso kuti Davide abwerere kunyumba kwa bambo ake.+  Yonatani ndi Davide anachita pangano,+ chifukwa Yonatani ankakonda Davide ngati mmene ankadzikondera.*+  Ndiyeno Yonatani anavula mkanjo wake wodula manja nʼkumupatsa Davide. Anamupatsanso zovala zake zankhondo, lupanga, uta ndi lamba.  Davide anayamba kupita kunkhondo ndipo kulikonse kumene Sauli wamutumiza, zinthu zinkamuyendera bwino.+ Choncho Sauli anamuika kuti akhale mkulu wa asilikali+ ndipo zimenezi zinasangalatsa anthu onse komanso atumiki a Sauli.  Davide ndi asilikali ena akamabwera kuchokera kokapha Afilisiti, azimayi ankatuluka mʼmizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ komanso kuvina. Iwo ankapita kukachingamira Mfumu Sauli mosangalala, akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu.  Azimayi amene ankasangalalawo ankaimba kuti: “Sauli wapha adani ake masauzande,Ndipo Davide wapha masauzande ambirimbiri.”+  Sauli anakwiya kwambiri+ ndipo nyimbo imeneyi inkamunyasa, moti anayamba kuganiza kuti: “Akutamanda Davide ponena kuti wapha masauzande ambirimbiri, koma ine akunena kuti ndapha masauzande okha. Ndiye kuti kwatsala nʼkumupatsa ufumuwutu basi!”+  Kuyambira tsiku limenelo, Sauli anayamba kuyangʼana Davide ndi diso loipa. 10  Tsiku lotsatira, Sauli anagwidwa ndi mzimu woipa wochokera kwa Mulungu+ moti anayamba kuchita zinthu zachilendo* mʼnyumba mwake. Pa nthawiyi nʼkuti Davide akuimba nyimbo ndi zeze+ ngati mmene ankachitira ndipo Sauli anali ndi mkondo mʼmanja mwake.+ 11  Kenako Sauli anaponya mkondowo+ ndipo mumtima mwake ankati: ‘Ndibaya Davide nʼkumukhomerera kukhoma!’ Koma Davide anazinda nʼkuthawa ndipo zimenezi zinachitika kawiri konse. 12  Ndiyeno Sauli anachita mantha ndi Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo,+ koma Sauliyo anali atamʼchokera.+ 13  Choncho Sauli anachotsa Davide kuti asamakhalenso naye pafupi, ndipo anamuika kukhala mtsogoleri wa gulu la asilikali 1,000, moti Davide ankatsogolera asilikali kunkhondo.+ 14  Zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino Davide+ pa zonse zomwe ankachita ndipo Yehova anali naye.+ 15  Sauli ataona kuti Davide zinthu zikumuyendera bwino kwambiri, anachita naye mantha. 16  Koma anthu onse a mu Isiraeli ndi Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera kunkhondo. 17  Kenako Sauli anauza Davide kuti: “Paja ndili ndi mwana wamkazi wamkulu, Merabu,+ ndipo ndidzakupatsa kuti akhale mkazi wako.+ Koma iweyo upitirize kumenya nkhondo za Yehova+ ndiponso kundisonyeza kuti ndiwe wolimba mtima.” Mumtima mwake ankati: ‘Ndisamuphe ndine koma amuphe ndi Afilisiti.’+ 18  Koma Davide anayankha Sauli kuti: “Ndine ndani ine ndipo abale anga ndi anthu a mʼbanja la bambo anga ndi ndani mu Isiraeli, kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?”+ 19  Ndiyeno itafika nthawi yopereka Merabu mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, anali ataperekedwa kale kwa Adiriyeli+ Mmeholati kuti akhale mkazi wake. 20  Ndiyeno Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli ankakonda Davide. Anthu anauza Sauli za nkhaniyi ndipo Sauli atamva anasangalala. 21  Choncho Sauli anati: “Ndimʼpatsa Mikala kuti akhale msampha kwa iye, kuti Afilisiti amuphe.”+ Zitatero Sauli anauzanso Davide kachiwiri kuti: “Lero uchita nane mgwirizano wa ukwati.”* 22  Kuwonjezera pamenepo, Sauli analamula atumiki ake kuti: “Mukalankhule ndi Davide mwachinsinsi ndipo mukamuuze kuti, ‘Mfumutu ikusangalala nawe, ndipo atumiki ake onse akukukonda kwambiri. Ndiye chita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu.’” 23  Atumiki a Sauli atauza Davide mawu amenewa, Davide anawayankha kuti: “Kodi mukuona ngati ndi nkhani yaingʼono kuti munthu wosauka ndi wonyozeka ngati ine ndichite mgwirizano wa ukwati ndi mfumu?”+ 24  Ndiyeno atumikiwo anauza Sauli kuti: “Zimenezi nʼzimene Davide watiyankha.” 25  Sauli anati: “Mukauze Davide kuti, ‘Sikuti mfumu ikufuna malowolo,+ koma ikungofuna makungu amene amachotsa pochita mdulidwe a Afilisiti okwana 100,+ kuti ibwezere adani ake.’” Koma pamenepa Sauli ankakonza chiwembu kuti Davide aphedwe ndi Afilisiti. 26  Choncho atumiki a Sauli anauza Davide uthengawu. Davide anasangalala nazo ndipo anavomera kuti achite mgwirizano wa ukwati ndi mfumu.+ Nthawi imene anagwirizana isanakwane, 27  Davide ndi asilikali ake anapita nʼkukapha Afilisiti 200. Ndiyeno Davide anabweretsa makungu awo akunsonga ndipo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Choncho Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+ 28  Sauli anazindikira kuti Yehova ali ndi Davide.+ Anazindikiranso kuti mwana wake Mikala, ankamukonda kwambiri Davideyo.+ 29  Zimenezi zinangochititsanso kuti Sauli azimuopa kwambiri Davide ndipo Sauli anakhala mdani wa Davide moyo wake wonse.+ 30  Pa nthawi iliyonse imene akalonga a Afilisiti apita kukamenya nkhondo, zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri Davide kuposa atumiki onse a Sauli,+ moti dzina la Davide linatchuka kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ankakondera moyo wake.”
Kapena kuti, “mtima wa Yonatani unalumikizana ndi mtima wa Davide.”
Kapena kuti, “ankakondera moyo wake.”
Kapena kuti, “ngati mneneri.”
Kapena kuti, “ukhala mkamwini wanga.”