1 Samueli 2:1-36

  • Pemphero la Hana (1-11)

  • Machimo a ana awiri a Eli (12-26)

  • Yehova anaweruza banja la Eli (27-36)

2  Kenako Hana anapemphera kuti: “Mtima wanga ukukondwera chifukwa cha Yehova,+Yehova wakweza nyanga* yanga. Ndikutsutsa adani anga molimba mtimaChifukwa ndikukondwera ndi chipulumutso chanu.   Palibe woyera ngati Yehova,Palibenso wina koma inu nokha,+Ndipo palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.+   Musamalankhule modzikweza,Pakamwa panu pasatuluke mawu odzikuza,Chifukwa Yehova ndi Mulungu wodziwa zonse,+Ndipo zochita za anthu, iye amaziyeza molondola.   Mauta a anthu amphamvu awonongedwa,Koma ofooka apatsidwa mphamvu.+   Odya bwino ayenera kugwira ganyu kuti apeze chakudya,Koma anjala alibenso njala.+ Wosabereka wabereka ana 7,+Koma amene anali ndi ana aamuna ambiri, ali yekhayekha.*   Yehova amapha komanso amasunga moyo,*Iye amatsitsira Kumanda* komanso amaukitsa.+   Yehova amasaukitsa ndiponso amalemeretsa,+Iye amatsitsa komanso amakweza.+   Amadzutsa wonyozeka kumuchotsa pafumbi,Amachotsa osauka paphulusa,*+Kuti akhale ndi ana a mafumu,Ndipo amawapatsa mpando wolemekezeka. Chifukwa zolimbitsira dziko lapansi ndi za Yehova,+Ndipo anakhazika dziko lapansi pa zolimbitsirazo.   Amateteza mapazi a okhulupirika ake,+Koma anthu oipa adzawakhalitsa chete mumdima,+Popeza munthu sapambana chifukwa cha mphamvu zake.+ 10  Yehova adzawononga onse olimbana naye,*+Akadzawakwiyira, kumwamba kudzagunda mabingu.+ Yehova adzaweruza dziko lonse lapansi,+Iye adzapereka mphamvu kwa mfumu yake,+Ndipo adzakweza nyanga* ya wodzozedwa wake.”+ 11  Kenako Elikana anapita kunyumba kwake ku Rama, koma mwanayo anatsala nʼkumatumikira Yehova+ moyangʼaniridwa ndi wansembe Eli. 12  Ana a Eli anali oipa+ ndipo sankalemekeza Yehova. 13  Munthu aliyense akamapereka nsembe ankayeneranso kupereka gawo la nyamayo kwa wansembe.+ Ndiyeno zimene zinkachitika nʼzakuti nyamayo ikamawira, mtumiki wa wansembe ankabwera foloko ya mano atatu ili mʼmanja. 14  Akatero ankapisa folokoyo mʼbeseni, mʼpoto wa zogwirira ziwiri, mumphika kapena mʼpoto wa chogwirira chimodzi. Ndiyeno wansembe ankatenga chilichonse chimene folokoyo yatulutsa. Zimenezi ndi zimene ankachitira Aisiraeli onse opita ku Silo. 15  Komanso munthu wopereka nsembe asanapsereze mafuta,+ mtumiki wa wansembe ankabwera nʼkumuuza kuti: “Ndipatse nyama yosaphika ndikawotchere wansembe. Wansembe sakufuna nyama yophika koma yosaphika.” 16  Munthuyo akanena kuti: “Yembekeza kaye apsereze mafutawo+ kenako utenge chilichonse chimene ukufuna,” iye ankayankha kuti: “Ayi, ndipatse pompano, apo ayi ndichita kulanda!” 17  Atumikiwa ankachimwira Yehova kwambiri,+ chifukwa sankalemekeza nsembe ya Yehova. 18  Ndiyeno Samueli ankatumikira+ pamaso pa Yehova ndipo ankavala efodi wansalu,+ ngakhale kuti anali mwana. 19  Komanso chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo kodula manja. Iwo ankamupititsira kamalayako akapita ndi amuna awo kukapereka nsembe yapachaka.+ 20  Pa ulendo wina, Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, ndipo anati: “Yehova akupatsenso mwana kudzera mwa mkaziyu kuti alowe mʼmalo mwa amene anaperekedwa kwa Yehova.”+ Kenako makolowo anabwerera kwawo. 21  Yehova anakomera mtima Hana moti anabereka ana ena.+ Anabereka ana aamuna atatu ndi aakazi awiri. Ndipo Samueli anapitiriza kukula akutumikira Yehova.*+ 22  Pa nthawiyi Eli anali atakalamba kwambiri koma anamva zonse zimene ana ake ankachitira+ Aisiraeli onse. Anamvanso kuti ankagona ndi akazi amene ankatumikira pakhomo la chihema chokumanako.+ 23  Ndipo iye ankawauza kuti: “Mukuchitiranji zimenezi? Chifukwatu zimene anthu onse akundiuza zokhudza inu ndi zoipa zokhazokha. 24  Musatero ana anga, chifukwa nkhani zimene ndikumva, zimene anthu a Yehova akunena, si zabwino. 25  Munthu akachimwira mnzake, munthu wina akhoza kumuchonderera kwa Yehova,* koma akachimwira Yehova,+ angamupempherere ndi ndani?” Koma anawo sankamvera bambo awo ndipo tsopano Yehova anali atatsimikiza mtima kuti awaphe.+ 26  Koma Samueli ankakula bwino ndipo ankakondedwa kwambiri ndi Yehova komanso anthu.+ 27  Ndiyeno munthu wa Mulungu anapita kwa Eli nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi ine sindinachititse kuti anthu amʼnyumba ya bambo ako andidziwe pamene anali akapolo kunyumba ya Farao ku Iguputo?+ 28  Pa mafuko onse a Isiraeli ndinasankha kholo lako+ kukhala wansembe wanga, kuti azipita paguwa langa lansembe+ kukapereka nsembe zanyama, azipereka nsembe zofukiza ndiponso kuti azivala efodi pamaso panga. Komanso ndinapatsa nyumba ya kholo lako nsembe zonse zotentha ndi moto za Aisiraeli.+ 29  Nʼchifukwa chiyani anthu inu mukunyoza nsembe zanga zimene ndinalamula kuti ziziperekedwa mʼnyumba yanga?+ Nʼchifukwa chiyani mukulemekezabe ana anu koposa ine podzinenepetsa ndi mbali zabwino kwambiri za nsembe iliyonse ya anthu anga Aisiraeli?+ 30  Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ndinanenadi kuti a mʼbanja lako ndiponso a mʼbanja la kholo lako adzanditumikira mpaka kalekale.”+ Koma tsopano Yehova akuti: “Sindingachitenso zimenezo, chifukwa amene akundilemekeza ndidzawalemekeza+ koma amene akundinyoza, adzanyozedwa.” 31  Tsopano tamvera, masiku adzafika pamene ndidzadula mphamvu zako* ndiponso mphamvu za nyumba ya bambo ako, moti mʼnyumba yako palibe munthu amene adzafike pokalamba.+ 32  Ndipo mʼnyumba yanga udzangoona mdani pakati pa zinthu zonse zabwino zimene zidzachitikira Isiraeli.+ Mʼnyumba yako simudzapezekanso munthu wokalamba. 33  Munthu wa mʼbanja lako amene sindidzamusiyitsa kutumikira paguwa langa lansembe adzachititsa kuti maso ako asamaone komanso adzakuchititsa chisoni. Koma anthu ambiri amʼbanja lako adzaphedwa ndi lupanga.+ 34  Ndipo zimene zidzachitikire ana ako awiri Hofeni ndi Pinihasi zidzakhala chizindikiro kwa iwe: Onse awiri adzafa tsiku limodzi.+ 35  Kenako ndidzasankha wansembe wanga wokhulupirika.+ Ameneyu adzachita mogwirizana ndi zimene mtima wanga ukufuna. Ndidzamʼmangira nyumba yokhalitsa, ndipo adzatumikira wodzozedwa wanga monga wansembe nthawi zonse. 36  Ndiyeno aliyense wotsala mʼnyumba yako adzafika nʼkumugwadira kuti amulipire ndalama ndi chakudya, ndipo adzati: “Ndiloleni chonde ndikhale wansembe kuti ndizipezako kachakudya.”’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wakweza mphamvu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wafota.”
Kapena kuti, “amapereka moyo.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “padzala.”
Mabaibulo ena amati, “Onse olimbana ndi Yehova adzachita mantha.”
Kapena kuti, “mphamvu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “anapitiriza kukula pamaso pa Yehova.”
Mabaibulo ena amati, “akachimwira mnzake, Mulungu adzamuweruzira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzadula dzanja lako.”