1 Samueli 20:1-42

  • Yonatani anali wokhulupirika kwa Davide (1-42)

20  Ndiyeno Davide anathawa kuchoka ku Nayoti, ku Rama. Koma anapita kwa Yonatani nʼkumuuza kuti: “Kodi ine ndatani?+ Ndalakwa chiyani, ndipo bambo ako ndawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?”  Yonatani anamuyankha kuti: “Nʼzosatheka zimenezo,+ suufa. Bambo anga sangachite chilichonse, kaya chachikulu kapena chachingʼono, osandiuza. Ndiye bambo anga angandibisire nkhani imeneyi chifukwa chiyani? Sizingachitike zimenezo.”  Koma Davide analumbira kuti: “Bambo ako akudziwa kuti umandikonda.+ Choncho akhoza kunena kuti, ‘Yonatani musamuuze zimenezi chifukwa akwiya nazo.’ Moti ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, komanso pamaso pako, imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+  Kenako Yonatani anauza Davide kuti: “Ndikuchitira chilichonse chimene unganene.”  Davide anauza Yonatani kuti: “Paja mawa ndi tsiku limene mwezi watsopano uoneke,+ ndipo ndiyenera kukadya ndi mfumu. Ndimati undilole ndipite kukabisala kutchire mpaka mkuja madzulo.  Ngati bambo ako angazindikire kuti ine palibe, uwauze kuti, ‘Davide anandichonderera kuti ndimulole kuchoka mwamsanga kuti apite kumzinda wakwawo ku Betelehemu,+ chifukwa banja lawo lonse likukapereka nsembe ya pachaka.’+  Ngati anganene kuti, ‘Palibe vuto!’ ndiye kuti zinthu zili bwino kwa ine mtumiki wako. Koma ngati angakwiye, udziwe kuti atsimikiza mtima kundichitira zoipa.  Undisonyeze chikondi chokhulupirika ine mtumiki wako,+ chifukwa iwe ndi ine tinachita pangano pamaso pa Yehova.+ Koma ngati ndili wolakwa,+ undiphe iweyo, mʼmalo moti ukandipereke kwa bambo ako.”  Yonatani anayankha kuti: “Nʼzosatheka kuti iwe ukhale wolakwa! Ngati ndingadziwe zoipa zimene bambo anga akufuna kukuchitira, ukuganiza kuti sindingakuuze?”+ 10  Ndiyeno Davide anafunsa Yonatani kuti: “Nanga adzandiuza ndani ngati bambo ako ayankha mwaukali?” 11  Yonatani anayankha Davide kuti: “Tiye tipite kutchire.” Choncho onse anapita kutchire. 12  Yonatani anauza Davide kuti: “Ndidzalankhula ndi bambo anga mawa kapena mkuja ndipo Yehova Mulungu wa Isiraeli akhale mboni. Ngati alibe nawe chifukwa, ndikutumizira uthenga wokudziwitsa. 13  Yehova andilange ine Yonatani mowirikiza, ndikadziwa kuti bambo anga akufuna kukuchitira zoipa koma osakudziwitsa nʼkukulola kuti upite mwamtendere. Yehova akhale nawe+ ngati mmene anakhalira ndi bambo anga.+ 14  Ndipo kodi sudzandisonyeza chikondi chokhulupirika cha Yehova ndili moyo ngakhalenso nditafa?+ 15  Usadzasiye kusonyeza anthu amʼbanja langa chikondi chokhulupirika,+ ngakhale pamene Yehova adzawononga mdani aliyense wa Davide padziko lapansi.” 16  Choncho Yonatani anachita pangano ndi nyumba ya Davide kuti: “Yehova adzaimba mlandu adani a Davide.” 17  Choncho Yonatani anachititsa kuti Davide alumbirenso posonyeza kuti ankamukonda kwambiri chifukwa Yonatani ankakonda Davide ngati mmene ankadzikondera yekha.+ 18  Kenako Yonatani ananena kuti: “Mawa ndi tsiku limene mwezi watsopano uoneke,+ ndipo anthu adzazindikira kuti iwe palibe chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu. 19  Ndipo mkuja ayenera kuti adzafunsa za iweyo. Udzapite kukabisala pamalo amene unabisala tsiku lijali* ndipo udzakhale pafupi ndi mwala uwu. 20  Ineyo ndidzaponya mivi itatu kumbali ina ya mwalawo, ngati kuti ndikufuna kubaya chinachake. 21  Ndiyeno ndidzauza mtumiki wanga kuti, ‘Pita ukatole miviyo.’ Koma ndikadzauza mtumikiyo kuti, ‘Mivi ili mbali iyo, pita ukatole,’ iweyo ukatuluke chifukwa ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, zinthu zidzakhala kuti zili bwino ndipo palibe chodetsa nkhawa chilichonse. 22  Koma ndikadzauza mnyamatayo kuti, ‘Mivi ili kutali kwambiri ndi iwe,’ ndiye kuti uyenera kuchoka, chifukwa Yehova wakulola kupita. 23  Yehova akhale mboni yathu mpaka kalekale+ pa zimene iwe ndi ine talonjezana.”+ 24  Choncho Davide anapita kutchire kukabisala. Pa tsiku looneka mwezi watsopano, mfumu inakhala pampando wake kuti idye chakudya.+ 25  Inakhala pamalo ake a nthawi zonse, pafupi ndi khoma. Yonatani anakhala moyangʼanizana ndi mfumuyo, pamene Abineri+ anakhala pambali pa mfumu. Koma mpando wa Davide unali wopanda munthu. 26  Pa tsiku limeneli Sauli sananene chilichonse, chifukwa ankaganiza kuti: ‘Chinachake chachitika ndipo wadetsedwa.+ Ayenera kuti wadetsedwa ndithu.’ 27  Tsiku lotsatira,* mpando wa Davide unakhalabe wopanda munthu. Choncho Sauli anafunsa mwana wake Yonatani kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwana wa Jese+ sanabwere kudzadya dzulo ndi lero?” 28  Yonatani anayankha Sauli kuti: “Davide anandichonderera kuti ndimulole kupita ku Betelehemu.+ 29  Anandiuza kuti, ‘Chonde ndilole ndipite chifukwa banja lathu likukapereka nsembe mumzinda wakwathu. Mchimwene wanga ndi amene wandiitanitsa. Choncho ngati ungandikomere mtima, ndilole ndipite ndikaone abale anga.’ Nʼchifukwa chake sanabwere kudzadya ndi mfumu.” 30  Koma Sauli anamukwiyira kwambiri Yonatani, ndipo anamuuza kuti: “Chimwana cha mkazi wopanduka iwe! Ukuganiza sindikudziwa kuti wasankha kugwirizana ndi mwana wa Jese, nʼkudzichititsa manyazi wekha ndiponso kuvula mayi ako? 31  Ngati mwana wa Jeseyo angakhale ndi moyo, iweyo ndi ufumu wako sudzakhazikika.+ Tumiza munthu akamugwire nʼkumubweretsa kwa ine, chifukwa ayenera kufa ndithu.”+ 32  Koma Yonatani anayankha Sauli bambo ake kuti: “Aphedwe chifukwa chiyani?+ Walakwa chiyani?” 33  Atatero, Sauli anaponya mkondo wake kuti amuphe.+ Apa tsopano Yonatani anadziwa kuti bambo ake atsimikiza zopha Davide.+ 34  Nthawi yomweyo, Yonatani ananyamuka patebulopo atakwiya kwambiri, ndipo tsiku limeneli* sanadye. Iye anachita zimenezi chifukwa chopsa mtima ndi nkhani ya Davide+ komanso chifukwa bambo ake anamʼchititsa manyazi. 35  Kutacha, Yonatani anapita kutchire kumene anapangana kukakumana ndi Davide ndipo anapita ndi mnyamata wake.+ 36  Ndiyeno anauza mnyamata wakeyo kuti: “Thamanga ukatole mivi imene ndikuponya.” Mnyamatayo anathamanga, ndipo Yonatani anaponya muvi moti unamupitirira. 37  Mnyamata uja atafika pamalo amene muvi wa Yonatani unagwera, Yonatani anafuula kuti: “Muvi wagwera patali kutsogolo kwako!” 38  Yonatani anapitiriza kuti: “Fulumira! Thamanga, usachedwe!” Ndiyeno mnyamatayo anatola miviyo nʼkupita nayo kwa mbuye wakeyo. 39  Mnyamatayo sanazindikire chilichonse. Yonatani ndi Davide okha ndi amene ankadziwa zomwe zikuchitika. 40  Kenako, Yonatani anapatsa mnyamata wakeyo zida zake nʼkumuuza kuti: “Tenga zidazi uzipita nazo.” 41  Mnyamatayo atapita, Davide anatuluka pamene anabisala, ndipo panali pafupi pompo, chakumʼmwera. Ndiyeno anagwada nʼkuwerama katatu. Atatero, Davide ndi Yonatani anakisana ndipo onse anayamba kulira, koma Davide ndi amene analira kwambiri. 42  Kenako Yonatani anauza Davide kuti: “Pita mwamtendere, chifukwa tonse talumbira+ mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndiponso pakati pa mbadwa* zako ndi mbadwa* zanga mpaka kalekale.’”+ Kenako Davide ananyamuka nʼkumapita ndipo Yonatani anabwerera kwawo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “pa tsiku logwira ntchito.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Tsiku lotsatizana ndi tsiku lomwe mwezi watsopano unaoneka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tsiku lachiwiri lotsatizana ndi tsiku limene mwezi watsopano unaoneka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”