1 Samueli 21:1-15

  • Davide anadya mkate wachionetsero ku Nobu (1-9)

  • Davide ananamizira misala ku Gati (10-15)

21  Kenako Davide anafika ku Nobu+ kwa Ahimeleki wansembe. Ahimeleki ataona Davide anayamba kunjenjemera, ndipo anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani uli wekhawekha?”+  Davide anayankha Ahimeleki wansembe kuti: “Mfumu yandituma kuti ndikachite zinazake ndipo yandiuza kuti, ‘Usauze aliyense zimene ndakutumazi komanso malangizo amene ndakupatsa.’ Ndapangana ndi anyamata anga kuti ndikumane nawo penapake.  Ndiye ngati muli ndi mikate 5 kapena chakudya chilichonse mundipatseko.”  Koma wansembeyo anayankha Davide kuti: “Palibe mkate wamba, koma pali mkate wopatulika.+ Nditha kukupatsa umenewu ngati anyamatawo ayesetsa kudzisunga osagona ndi akazi.”+  Davide anayankha wansembeyo kuti: “Akazi sanatiyandikire ngati mmene zinalilinso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba, ndiye kuli bwanji lero?”  Choncho wansembeyo anamupatsa mkate wopatulika,+ chifukwa panalibe mkate wina koma mkate wachionetsero umene anauchotsa pamaso pa Yehova tsiku limenelo kuti aikepo watsopano.  Pa tsikuli, mmodzi wa atumiki a Sauli anali kumeneko chifukwa anali atamusunga pamaso pa Yehova. Dzina lake anali Doegi+ ndipo anali wa ku Edomu.+ Iye anali mkulu wa abusa a Sauli.  Davide anafunsa Ahimeleki kuti: “Kodi muli ndi mkondo kapena lupanga? Ndinalephera kutenga lupanga kapena zida zanga, chifukwa zimene mfumu yandituma ndi zofunika mwamsanga.”  Wansembeyo anayankha kuti: “Limene lilipo ndi lupanga la Goliyati+ Mfilisiti amene unamupha mʼchigwa cha Ela.+ Lakulungidwa ndi nsalu ndipo lili kuseli kwa efodi.+ Ngati ungalikonde ukhoza kutenga, chifukwa lilipo ndi lokhalo.” Ndiyeno Davide anati: “Palibenso lina ngati limeneli, ndipatseni.” 10  Davide ananyamuka tsiku lomwelo ndipo anapitiriza kuthawa+ Sauli. Patapita nthawi anafika kwa Mfumu Akisi ya ku Gati.+ 11  Atafika kumeneko, atumiki a Akisi ananena kuti: “Kodi ameneyu si Davide mfumu ya dziko la Isiraeli? Suja ankamuimbira nyimbo uku akuvina nʼkumati,‘Sauli wapha adani ake masauzande,Ndipo Davide wapha masauzande ambirimbiri.’”+ 12  Davide atamva zimenezi, anachita mantha kwambiri+ poopa zimene Akisi mfumu ya ku Gati angachite. 13  Choncho pamene anali ndi anthuwo* anayamba kuchita zinthu ngati wamisala kuti asadziwike kuti ndi wabwinobwino.+ Iye ankalembalemba pazitseko zapageti, uku dovu likuyenderera pandevu zake. 14  Zitatero Akisi anauza atumiki ake kuti: “Simukuona kuti munthuyu ndi wamisala? Ndiye nʼchifukwa chiyani mwabwera naye kwa ine? 15  Kodi ine ndikusowa anthu amisala kuti mundibweretsere munthu ameneyu kudzachita zamisala kunoko? Kodi ameneyu ndi woyenera kulowa mʼnyumba mwanga?”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmanja mwawo.”