1 Samueli 23:1-29

  • Davide anapulumutsa mzinda wa Keila (1-12)

  • Sauli ankasakasaka Davide (13-15)

  • Yonatani analimbikitsa Davide (16-18)

  • Sauli anangotsala pangʼono kupeza Davide (19-29)

23  Patapita nthawi, anthu anauza Davide kuti: “Afilisiti akumenyana ndi mzinda wa Keila,+ ndipo akulanda zokolola zimene zili pamalo opunthira mbewu.”  Ndiyeno Davide anafunsira kwa Yehova+ kuti: “Kodi ndipite kukapha Afilisiti?” Yehova anayankha Davide kuti: “Pita, ukaphe Afilisitiwo ndipo ukapulumutse Keila.”  Koma amuna amene anali ndi Davide ananena kuti: “Ngati tikuchita mantha tili ku Yuda kuno,+ ndiye kuli bwanji tikapita ku Keila kukamenyana ndi asilikali a Afilisiti!”+  Choncho Davide anafunsiranso kwa Yehova.+ Ndipo Yehova anamuyankha kuti: “Nyamuka, pita ku Keila, chifukwa ndipereka Afilisitiwo mʼmanja mwako.”+  Choncho Davide ndi amuna amene anali naye anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisiti. Iye analanda ziweto zawo ndipo anapha Afilisiti ambiri, moti Davide anapulumutsa anthu amumzinda wa Keila.+  Pamene Abiyatara+ mwana wamwamuna wa Ahimeleki ankathawira kwa Davide ku Keila, anatenga efodi.  Kenako Sauli anauzidwa kuti: “Davide ali ku Keila.” Ndiyeno Sauli ananena kuti: “Mulungu wamupereka* kwa ine,+ chifukwa wadzitsekereza yekha polowa mumzinda wokhala ndi mageti otsekedwa mwamphamvu.”  Choncho Sauli anaitanitsa anthu onse kuti apite kunkhondo kuti akazungulire mzinda wa Keila momwe munali Davide ndi anthu ake.  Davide atadziwa kuti Sauli akumukonzera chiwembu, anauza Abiyatara wansembe kuti: “Bweretsa efodi.”+ 10  Kenako Davide anati: “Yehova Mulungu wa Isiraeli, ine mtumiki wanu ndamva kuti Sauli akufuna kubwera kuno ku Keila kudzawononga mzindawu chifukwa cha ine.+ 11  Kodi atsogoleri amumzinda wa Keila adzandipereka mʼmanja mwake? Kodi Sauli abweradi kuno ngati mmene ine mtumiki wanu ndamvera? Yehova Mulungu wa Isiraeli, chonde ndiuzeni ine mtumiki wanu.” Yehova anamuyankha kuti: “Inde abweradi.” 12  Ndiyeno Davide anafunsanso kuti: “Kodi atsogoleri amumzinda wa Keila adzandipereka kwa Sauli pamodzi ndi amuna amene ndili nawowa?” Yehova anayankha kuti: “Inde adzakupereka.” 13  Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi amuna pafupifupi 600 amene anali naye aja.+ Iwo anachoka ku Keila nʼkumapita kulikonse kumene angakhale otetezeka. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanamutsatirenso. 14  Davide ankakhala mʼmalo ovuta kufikako kumapiri mʼchipululu cha Zifi.+ Sauli ankafunafuna Davide nthawi zonse,+ koma Yehova sanamʼpereke mʼmanja mwake. 15  Pamene Davide anali mʼchipululu cha Zifi ku Horesi, anadziwa kuti* Sauli ali mʼderalo ndipo akufunafuna moyo wake. 16  Kenako Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamuthandiza* kuti apeze mphamvu kuchokera kwa Yehova.+ 17  Ndiyeno anamuuza kuti: “Usachite mantha, chifukwa Sauli bambo anga sakupeza, moti iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli,+ ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe. Sauli bambo anga akudziwa bwino zimenezi.”+ 18  Kenako awiriwo anachita pangano+ pamaso pa Yehova ndipo Davide anakhalabe ku Horesi koma Yonatani anabwerera kwawo. 19  Kenako amuna a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya+ nʼkumuuza kuti: “Davide akubisalatu pafupi ndi ife+ kumalo ovuta kufikako ku Horesi,+ paphiri la Hakila+ lomwe lili kumʼmwera* kwa Yesimoni.*+ 20  Nthawi iliyonse imene inu mfumu mungafune kubwera, bwerani, ndipo ife tidzamʼpereka mʼmanja mwanu.”+ 21  Sauli atamva zimenezi anati: “Yehova akudalitseni, chifukwa mwandichitira chifundo. 22  Ndiye ndikupempha kuti mukafufuze malo enieni amene akukhala komanso munthu amene anamuona, chifukwa ndamva kuti ndi wochenjera kwambiri. 23  Mukafufuze nʼkudziwa malo onse obisika kumene iye akubisala, ndipo mukabwere ndi umboni. Kenako ndidzapita nanu ndipo ngati alidi kumeneko, ndidzamʼfufuza pakati pa anthu masauzande* a ku Yuda.” 24  Choncho iwo anamusiya Sauli nʼkutsogola kupita ku Zifi.+ Apa nʼkuti Davide ndi amuna amene ankayenda naye ali mʼchipululu cha Maoni,+ ku Araba,+ kumʼmwera kwa Yesimoni. 25  Kenako Sauli anafika ndi asilikali ake kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anakabisala kuthanthwe,+ ndipo anapitiriza kukhala mʼchipululu cha Maoni. Sauli atauzidwa zimenezi anayamba kusakasaka Davide mʼchipululu cha Maoni. 26  Kenako Sauli anafika mbali ina ya phiri limene Davide ndi amuna amene anali naye anabisala. Zitatero Davide anayamba kukonzeka mwamsanga kuti athawe+ Sauli. Pa nthawiyi nʼkuti Sauli ndi asilikali ake atatsala pangʼono kupeza Davide ndi amuna amene anali naye.+ 27  Koma kenako kunabwera munthu ndi uthenga wakuti: “Bwerani mofulumira, Afilisiti aukira dziko lathu!” 28  Zitatero Sauli anasiya kusakasaka Davide+ ndipo anabwerera kukamenyana ndi Afilisiti. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Thanthwe Logawanitsa. 29  Ndiyeno Davide anachoka kumeneko nʼkukakhala kumalo ovuta kufikako a ku Eni-gedi.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “wamugulitsa.”
Mabaibulo ena amati, “anapitiriza kukhala mwamantha chifukwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “analimbitsa dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja.”
Mabaibulo ena amati, “chipululu.”
Kapena kuti, “mʼmabanja.”