1 Samueli 24:1-22
24 Sauli atangobwerera kuchokera kothamangitsa Afilisiti, anauzidwa kuti: “Davide ali mʼchipululu cha Eni-gedi.”+
2 Ndiyeno Sauli anatenga amuna 3,000 osankhidwa mu Isiraeli monse, ndipo anapita mʼmatanthwe amene munkakhala mbuzi zamʼmapiri kukafunafuna Davide ndi amuna amene ankayenda naye.
3 Kenako, Sauli anafika kumakola a nkhosa amiyala mʼmbali mwa msewu, kumene kunali phanga. Iye analowa mʼphangamo kukadzithandiza. Pa nthawiyi nʼkuti Davide ndi amuna amene ankayenda naye atakhala pansi kumbuyo kwa phangalo pamalo osaonekera.+
4 Amuna amene anali ndi Davidewo anamuuza kuti: “Lerotu ndi tsiku limene Yehova akukuuzani kuti, ‘Taona, ndapereka mdani wako mʼmanja mwako,+ ndipo ukhoza kumuchita chilichonse chimene ukufuna.’” Choncho Davide ananyamuka ndipo mwakachetechete anadula kansalu kamʼmunsi mwa mkanjo wodula manja wa Sauli.
5 Koma kenako Davide anayamba kuvutika mumtima*+ chifukwa anadula kansalu kamʼmunsi mwa mkanjo wodula manja wa Sauli.
6 Iye anauza anthu amene anali naye kuti: “Ndikaiona nkhaniyi mmene Yehova akuionera, ndikuona kuti sindingayerekeze kuchitira zimenezo mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Sindingamuchitire zoipa chifukwa iye ndi wodzozedwa wa Yehova.”+
7 Choncho ndi mawu amenewa, Davide analetsa* anthu amene anali naye kuti asachitire Sauli choipa chilichonse. Kenako Sauli anatuluka mʼphangamo nʼkumapita.
8 Nayenso Davide anatuluka mʼphangamo ndipo anaitana Sauli kuti: “Mbuyanga mfumu!”+ Sauli atatembenuka, Davide anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi.
9 Ndiyeno Davide anauza Sauli kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukumvera zimene anthu akunena zakuti, ‘Davide akufuna kukuchitirani zoipa?’+
10 Lero mwaona nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphangamu. Winawake anandiuza kuti ndikupheni,+ koma ndinakumverani chisoni nʼkunena kuti, ‘Sindingachitire zoipa mbuyanga, chifukwa ndi wodzozedwa wa Yehova.’+
11 Bambo anga, onani kansalu aka, kamʼmunsi mwa mkanjo wanu wodula manja. Pamene ndimadula kansalu kameneka sindinakupheni. Ndiye mukhoza kuona kuti ndilibe maganizo oipa kapena oukira, ndipo sindinakuchimwireni.+ Koma inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.+
12 Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu,+ ndipo Yehova abwezere mʼmalo mwa ine,+ koma dzanja langali silidzakuchitirani choipa.+
13 Paja mwambi wakale umati, ‘Choipa chimachokera kwa munthu woipa,’ koma dzanja langa silidzakuchitirani choipa.
14 Kodi mfumu ya Isiraeli ikusakasaka ndani? Kodi mukuthamangitsa ndani? Zoona mukuthamangitsa galu wakufa? Nthata imodzi?+
15 Yehova akhale woweruza, ndipo aweruze pakati pa ine ndi inu. Iye adzaona nkhaniyi nʼkundiweruza kuti ndine wosalakwa+ ndipo adzandipulumutsa mʼmanja mwanu.”
16 Davide atangomaliza kulankhula mawu amenewa, Sauli anati: “Kodi ndi mawu ako, mwana wanga Davide?”+ Kenako Sauli anayamba kulira mokweza.
17 Iye anauza Davide kuti: “Ndiwe wolungama kwambiri kuposa ine, chifukwa wandichitira zabwino, koma ine ndakubwezera zoipa.+
18 Lero wandiuza zabwino zimene wandichitira, chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka mʼmanja mwako.+
19 Ndi ndani amene angapeze mdani wake nʼkumusiya kuti apite mwamtendere? Yehova adzakupatsa zinthu zabwino+ chifukwa cha zimene wandichitira lero.
20 Ine ndikudziwa kuti iweyo udzakhala mfumu,+ ndipo ufumu wa Isiraeli udzakhalabe mʼmanja mwako.
21 Tsopano ndilumbirire mʼdzina la Yehova+ kuti sudzawononga mbadwa* zanga komanso sudzafafaniza dzina langa mʼnyumba ya bambo anga.”+
22 Kenako, Davide analumbirira Sauli ndipo Sauliyo anapita kwawo.+ Koma Davide ndi amuna amene anali naye anapita kumalo ovuta kufikako.+