1 Samueli 25:1-44

  • Samueli anamwalira (1)

  • Nabala anakana kuthandiza anyamata a Davide (2-13)

  • Abigayeli anachita zinthu mwanzeru (14-35)

    • ‘Yehova adzakulunga moyo wanu mʼphukusi la moyo’ (29)

  • Yehova anapha Nabala wopanda nzeru (36-38)

  • Abigayeli anakhala mkazi wa Davide (39-44)

25  Patapita nthawi, Samueli+ anamwalira. Aisiraeli onse anasonkhana kuti alire maliro ake ndipo anamuika mʼmanda kunyumba kwake ku Rama.+ Kenako Davide ananyamuka nʼkupita kuchipululu cha Parana.  Panali munthu wina amene ankakhala ku Maoni,+ koma ntchito yake ankagwirira ku Karimeli.*+ Munthu ameneyu anali wolemera kwambiri ndipo anali ndi nkhosa 3,000 komanso mbuzi 1,000. Pa nthawiyi, iye ankameta ubweya wa nkhosa zake ku Karimeli.  Munthuyu dzina lake linali Nabala+ ndipo mkazi wake anali Abigayeli.+ Mkazi wakeyu anali wanzeru ndiponso wokongola, koma mwamunayu anali wouma mtima komanso wopanda khalidwe.+ Iye anali wakubanja la Kalebe.+  Davide ali kuchipululu, anamva kuti Nabala akumeta ubweya wa nkhosa zake.  Choncho Davide anatuma anyamata ake 10 nʼkuwauza kuti: “Pitani ku Karimeli kwa Nabala ndipo mukamufunse za moyo wake mʼdzina langa.  Kenako mukamuuze kuti, ‘Mukhale ndi moyo wautali komanso wabwino.* Anthu onse amʼnyumba yanu akhale ndi moyo wabwino limodzi ndi zonse zimene muli nazo.  Ndamva kuti mukumeta ubweya wa nkhosa zanu. Pamene abusa anu anali ndi ife, sitinawachitire choipa chilichonse,+ ndipo pa nthawi yonse imene anali ku Karimeli, palibe chinthu chawo chimene chinasowa.  Funsani anyamata anu zimenezi ndipo akuuzani. Ndikupempha kuti muwakomere mtima anyamata anga chifukwa tabwera pa nthawi yachisangalalo.* Chonde mugawire atumiki anu ndi ine mwana wanu Davide chilichonse chimene mungakonde kutipatsa.’”+  Choncho anyamata a Davide anapita kukauza Nabala zonsezi mʼdzina la Davide. Atamaliza kufotokoza, 10  Nabala anawayankha kuti: “Kodi Davide ndi ndani, ndipo mwana wa Jese ndi ndani? Masiku ano atumiki ambiri akukonda kuthawa ambuye awo.+ 11  Ndiye zoona ine nditenge mkate wanga, madzi ndi nyama imene ndaphera antchito anga ometa ubweya wa nkhosa nʼkupereka kwa amuna amene sindikudziwa kumene achokera?” 12  Zitatero, anyamata a Davide ananyamuka nʼkumapita ndipo atafika anamufotokozera zonse. 13  Nthawi yomweyo Davide anauza amuna amene anali naye kuti: “Aliyense amangirire lupanga lake mʼchiuno!”+ Choncho onse anamangirira malupanga awo mʼchiuno ndipo Davide nayenso anamangirira lake. Amuna pafupifupi 400 anapita limodzi ndi Davide, koma 200 anatsala kuti aziyangʼanira katundu. 14  Izi zili choncho, mmodzi wa antchito a Nabala anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala kuti: “Davide anatuma anthu kuchokera kuchipululu kudzafunira zabwino abwana, koma abwanawo awalalatira.+ 15  Anthu amenewa anatichitira zabwino kwambiri ndipo sanatichitire choipa chilichonse. Pa nthawi yonse imene tinali nawo kutchire, palibe chinthu chathu chimene chinasowa.+ 16  Iwo anali ngati khoma lotiteteza masana ndi usiku, pa nthawi yonse yomwe tinali nawo pamene tinkaweta nkhosa. 17  Ndiye muona zimene mungachite, chifukwa zimenezi zibweretsa tsoka kwa abwana ndi anthu onse amʼnyumba yawo.+ Abwana athu ndi munthu wopanda pake+ ndipo palibe amene angalankhule nawo.” 18  Nthawi yomweyo, Abigayeli+ anatenga mikate 200, mitsuko iwiri ikuluikulu ya vinyo komanso anapha nkhosa 5. Anatenganso tirigu wokazinga wokwana miyezo 5 ya seya,* makeke 100 a mphesa zouma ndiponso makeke 200 a nkhuyu zouma nʼkuzikweza pa abulu.+ 19  Kenako anauza antchito ake kuti: “Tsogolani, ine ndikubwera.” Koma mwamuna wake Nabala sanamuuze chilichonse. 20  Pamene Abigayeli ankatsika phiri atakwera bulu, anangoona Davide ndi amuna amene anali naye akubwera, ndipo anakumana nawo. 21  Davide anali atanena kuti: “Ndinagwira ntchito pachabe polondera zinthu za munthu ameneyu mʼchipululu ndipo palibe chinthu chake ngakhale chimodzi chimene chinasowa.+ Koma akundibwezera zoipa pa zabwino zimene ndinamʼchitira.+ 22  Choncho Mulungu alange mowirikiza adani a Davide,* ngati ine ndidzasiya mwamuna* aliyense wa mʼnyumba ya Nabala ali ndi moyo mpaka mʼmawa.” 23  Abigayeli ataona Davide, nthawi yomweyo anatsika pabulu wake ndipo anagwada patsogolo pa Davide nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi. 24  Kenako anawerama pamapazi a Davide nʼkunena kuti: “Mbuyanga, zolakwa zonse zikhale pa ine. Lolani kuti ine kapolo wanu wamkazi ndilankhule nanu ndipo mvetserani zimene kapolo wanu akufuna kunena. 25  Chonde mbuyanga, musaganizire za Nabala, munthu wopanda pake,+ chifukwa zochita zake nʼzogwirizana ndi dzina lake. Dzina lake ndi Nabala* ndipo ndi wopandadi nzeru. Koma ine kapolo wanu sindinawaone anyamata amene inu mbuyanga munawatuma. 26  Mbuyanga, ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo komanso pamaso panu. Yehova ndi amene wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wa magazi+ komanso kuti musabwezere* nokha ndi dzanja lanu. Adani anu ndiponso onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala. 27  Ndiyeno mphatso*+ imene ine kapolo wanu wamkazi ndakubweretserani mbuyanga, muipereke kwa anyamata amene akukutsatirani.+ 28  Chonde, khululukani machimo a ine kapolo wanu wamkazi, chifukwa mosakayikira Yehova adzachititsa kuti nyumba ya mbuyanga ikhazikike,+ chifukwa inu mbuyanga mukumenya nkhondo za Yehova.+ Ndipo pa moyo wanu simunapezekepo ndi choipa chilichonse.+ 29  Munthu akakuukirani ndi kufunafuna moyo wanu, Yehova Mulungu wanu adzakulunga moyo wanu mʼphukusi la moyo kuti utetezeke. Koma moyo wa adani anu adzauponya kutali ngati mmene munthu amaponyera mwala ndi gulaye.* 30  Ndipo Yehova akadzakuchitirani mbuyanga zabwino zonse zimene analonjeza nʼkukuikani kukhala mtsogoleri wa Isiraeli,+ 31  simudzadandaula kapena kuvutika mumtima kuti munakhetsa magazi popanda chifukwa, kapena chifukwa choti munabwezera* nokha ndi dzanja lanu.+ Yehova akadzakuchitirani zabwino mbuyanga, mudzandikumbukire ine kapolo wanu wamkazi.” 32  Zitatero, Davide anauza Abigayeli kuti: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana ndi ine lero! 33  Iwenso udalitsike chifukwa cha kuganiza bwino kwako. Udalitsike chifukwa chondiletsa kuti ndisapalamule mlandu wa magazi+ ndiponso kuti ndisabwezere* ndekha ndi manja anga. 34  Mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo wa Isiraeli, amene wandiletsa kuti ndisakuchitire zoipa,+ ukanapanda kubwera mwamsanga kudzakumana ndi ine,+ ndithu sipakanatsala mwamuna* aliyense wamʼbanja la Nabala pofika mawa mʼmawa.”+ 35  Kenako Davide analandira zimene Abigayeli anamubweretsera nʼkumuuza kuti: “Pita kunyumba kwako mwamtendere. Ndamvera mawu ako ndipo ndidzachita zimene wapempha.” 36  Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anamupeza mʼnyumba mwake akuchita phwando ngati la mfumu. Nabala* anali akusangalala kwambiri ndiponso ataledzereratu. Abigayeli sanamuuze chilichonse mpaka mʼmawa. 37  Mʼmawa kutacha, vinyo atamuthera mʼmutu, mkazi wake anamuuza zonse zimene zinachitika. Nabala atamva zimenezi, mtima wake unaferatu ndipo anauma ngati mwala. 38  Patapita masiku pafupifupi 10, Yehova anapha Nabala. 39  Davide atamva kuti Nabala wamwalira ananena kuti: “Adalitsike Yehova amene wandiweruzira mlandu+ wa mawu onyoza a Nabala,+ komanso wandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa chilichonse.+ Yehova wabwezera zoipa za Nabala pamutu pake!” Kenako Davide anatuma anthu kuti akamufunsirire Abigayeli kuti akhale mkazi wake. 40  Choncho atumiki a Davide anapita kwa Abigayeli ku Karimeli ndipo anamuuza kuti: “Davide watituma kuti tidzakutenge ukakhale mkazi wake.” 41  Nthawi yomweyo, ananyamuka nʼkugwada mpaka nkhope yake kufika pansi, ndipo ananena kuti: “Ine kapolo wanu ndine wokonzeka kukhala wantchito wosambitsa mapazi+ a atumiki a mbuyanga.” 42  Kenako Abigayeli+ ananyamuka mofulumira nʼkukwera pabulu ndipo atsikana ake 5 antchito ankamutsatira pambuyo. Iye anapita limodzi ndi anthu amene anatumidwa ndi Davide ndipo anakakhala mkazi wake. 43  Davide anali atakwatiranso Ahinowamu+ wa ku Yezereeli+ ndipo onse awiri anakhala akazi ake.+ 44  Koma Sauli anali atapereka Mikala+ mwana wake wamkazi, mkazi wa Davide, kwa Paliti,+ mwana wamwamuna wa Laisi wa ku Galimu.

Mawu a M'munsi

Umenewu unali mzinda wa ku Yuda; si wofanana ndi phiri la Karimeli.
Kapena kuti, “Mtendere ukhale nanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pa tsiku labwino.”
Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati: “Davide” osati “adani a Davide.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
Kutanthauza, “Wopanda Nzeru; Wopusa.”
Kapena kuti, “musadzipulumutse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dalitso.”
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.
Kapena kuti, “munadzipulumutsa.”
Kapena kuti, “ndisadzipulumutse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mtima wa Nabala.”