1 Samueli 26:1-25
26 Patapita nthawi, amuna a ku Zifi+ anapita kwa Sauli ku Gibeya+ kukamuuza kuti: “Davide akubisala kuphiri la Hakila mbali imene yayangʼanizana ndi Yesimoni.”*+
2 Choncho Sauli ananyamuka nʼkupita kuchipululu cha Zifi ndi amuna 3,000 osankhidwa mu Isiraeli kuti akafunefune Davide kuchipululuko.+
3 Sauli anamanga msasa mʼmbali mwa msewu, paphiri la Hakila mbali yoyangʼanizana ndi Yesimoni. Pa nthawiyi Davide anali mʼchipululu ndipo anamva kuti Sauli wabwera kuchipululuko kudzamusakasaka.
4 Choncho Davide anatuma anthu kuti akaone ngati Sauli wabweradi.
5 Kenako Davide anapita kumene Sauli anamanga msasa. Iye anaona pamene Sauli komanso Abineri+ mwana wa Nera, mtsogoleri wa asilikali, anagona. Sauli anali atagona pakati pa msasa ndipo asilikali onse anagona momuzungulira.
6 Ndiyeno Davide anauza Ahimeleki Muhiti+ ndi Abisai+ mwana wa Zeruya,+ mchimwene wake wa Yowabu, kuti: “Ndani apite nane kwa Sauli kumsasa?” Abisai anayankha kuti: “Ine ndipita nanu.”
7 Choncho Davide ndi Abisai anapita kwa asilikaliwo usiku. Atafika anaona Sauli atagona pakati pa msasawo, mkondo wake atauzika pansi chakumutu kwake. Ndipo Abineri ndi asilikali ena onse anali atagona momuzungulira.
8 Ndiyeno Abisai anauza Davide kuti: “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu.+ Bwanji ndimubaye ndi mkondo nʼkumukhomerera pansi? Ndimubaya kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.”
9 Koma Davide anauza Abisai kuti: “Ayi, usamubaye. Ndani angavulaze wodzozedwa wa Yehova+ nʼkukhala wopanda mlandu?”+
10 Davide anapitiriza kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, Yehova adzamulanga yekha,+ kapena tsiku lidzafika+ ndipo adzamwalira, kapenanso adzapita kunkhondo nʼkukaphedwa.+
11 Ndikaiganizira nkhaniyi mmene Yehova akuionera, sindingayerekeze kuvulaza wodzozedwa wa Yehova.+ Ingotenga mkondo umene uli chakumutu kwakewo ndi jagi ya dothi ya madziyo tizipita.”
12 Choncho Davide anatenga mkondo ndi jagi ya madzi zimene zinali chakumutu kwa Sauli nʼkumapita. Palibe aliyense amene anadzuka, kuwaona+ kapena kuzindikira, chifukwa onse anali mʼtulo tofa nato tochokera kwa Yehova.
13 Kenako Davide anapita kutsidya lina nʼkukaima pamwamba pa phiri, chapatali. Pakati pawo panali kamtunda ndithu.
14 Davide anayamba kuitana asilikaliwo ndi Abineri mwana wa Nera kuti: “Abineri, kodi sukuyankha?” Abineri+ anati: “Ndiwe ndani amene ukuitana mfumu?”
15 Ndiyeno Davide anauza Abineri kuti: “Kodi si iwe mwamuna? Ndani angafanane nawe mu Isiraeli? Ndiye nʼchifukwa chiyani walephera kuyangʼanira mbuye wako mfumu? Msilikali winatu anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuye wako mfumu!+
16 Wachitazi si zabwino. Ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, anthu inu mukuyenera kufa chifukwa mwalephera kuyangʼanira mbuye wanu, yemwe ndi wodzozedwa wa Yehova.+ Ndiye tayangʼanani! Kodi mkondo wa mfumu ndi jagi yadothi ya madzi+ zimene zinali chakumutu kwake zili kuti?”
17 Sauli anazindikira mawu a Davide, ndipo anati: “Kodi ndi mawu ako mwana wanga Davide?”+ Davide anayankha kuti: “Inde ndi mawu anga, mbuyanga mfumu.”
18 Davide ananenanso kuti: “Nʼchifukwa chiyani mbuyanga mukundithamangitsa ine mtumiki wanu?+ Ndachita chiyani ine, ndipo ndalakwa chiyani?+
19 Mbuyanga mfumu, mvetserani mawu anga, ine mtumiki wanu: Ngati Yehova ndi amene wakutumani kuti mulimbane nane, iye alandire* nsembe yanga yambewu. Koma ngati ndi anthu amene akutumani,+ atembereredwe pamaso pa Yehova, chifukwa andithamangitsa lero kuti ndisakhale pamalo omwe ndi cholowa cha Yehova+ ndipo andiuza kuti, ‘Pita ukatumikire milungu ina!’
20 Musalole kuti magazi anga akhetsedwe pamaso pa Yehova, chifukwa mfumu ya Isiraeli yapita kukasakasaka nthata imodzi+ ngati ikuthamangitsa nkhwali imodzi mʼmapiri.”
21 Sauli anayankha kuti: “Ndachimwa.+ Bwerera mwana wanga Davide. Sindidzakusakasakanso chifukwa lero waona kuti moyo wanga ndi wamtengo wapatali.+ Ndachita zinthu mopusa komanso ndalakwitsa kwambiri.”
22 Davide anayankha kuti: “Eni, mkondo wa mfumu uwu! Tumani mmodzi wa anyamata anu adzatenge.
23 Yehova ndi amene adzabwezera aliyense mogwirizana ndi chilungamo chake+ komanso kukhulupirika kwake. Lero Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga, koma sindinafune kuvulaza wodzozedwa wa Yehova.+
24 Ine lero ndaona moyo wanu kukhala wamtengo wapatali. Mofanana ndi zimenezi, moyo wanganso ukhale wamtengo wapatali pamaso pa Yehova ndipo andipulumutse mʼmasautso anga onse.”+
25 Ndiyeno Sauli anayankha Davide kuti: “Mulungu akudalitse mwana wanga Davide. Mosakayikira iwe udzachita ntchito zazikulu komanso zidzakuyendera bwino.”+ Zitatero, Davide anachoka ndipo Sauli anabwerera kwawo.+