1 Samueli 27:1-12

  • Afilisiti anapatsa Davide mzinda wa Zikilaga (1-12)

27  Koma Davide anaganiza kuti: “Tsiku lina Sauli adzandipha ndithu. Chanzeru chimene ndingachite nʼkuthawira+ kudziko la Afilisiti. Ndiyeno Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Isiraeli+ ndipo ndidzapulumuka mʼmanja mwake.”  Choncho Davide pamodzi ndi amuna 600+ amene ankayenda naye anapita kwa Akisi+ mfumu ya ku Gati, mwana wa Maoki.  Davide ankakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi amuna amene ankayenda naye, ndipo aliyense anali ndi banja lake. Davide anali ndi akazi awiri, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala.  Sauli atamva kuti Davide wathawira ku Gati, anasiya kumusakasaka.+  Kenako Davide anauza Akisi kuti: “Ngati mungandikomere mtima, ndimapempha kuti andipatseko malo mumzinda umodzi wakutali kuti ndikakhale kumeneko. Palibe chifukwa choti ine mtumiki wanu ndizikhala limodzi ndi inu mumzinda wachifumu.”  Choncho pa tsikuli Akisi anapatsa Davide mzinda wa Zikilaga.+ Nʼchifukwa chake mzinda wa Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda mpaka lero.  Nthawi* yonse imene Davide anakhala mumzinda wakutali wa Afilisiti inali chaka chimodzi ndi miyezi 4.+  Davide ndi amuna amene ankayenda naye ankapita kukamenyana ndi Agesuri,+ Agirezi ndi Aamaleki.+ Anthu amenewa ankakhala mʼdera loyambira ku Telami kukafika ku Shura,+ mpaka kudziko la Iguputo.  Davide akapita kunkhondo sankasiya mwamuna kapena mkazi aliyense wamoyo.+ Iye ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamila ndi zovala ndipo akatero ankabwerera kwa Akisi. 10  Akisi akafunsa kuti: “Kodi lero munakamenya kuti nkhondo?” Davide ankayankha kuti: “Kumʼmwera kwa dziko* la Yuda”+ kapena “Kumʼmwera kwa dziko la Ayerameeli”+ kapena “Kumʼmwera kwa dziko la Akeni.”+ 11  Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi aliyense wamoyo nʼkubwerera naye ku Gati, chifukwa ankaganiza kuti: “Angayambe kukatinenera kuti, ‘Davide wachita zakutizakuti.’” (Izi nʼzimene iye ankachita pa nthawi yonse imene anakhala mumzinda wakutali wa Afilisiti.) 12  Akisi ankamukhulupirira Davide, ndipo mumtima mwake ankati: ‘Ndithu, Davide wakhala ngati fungo lonunkha kwa Aisiraeli anzake, ndipo adzakhalabe mtumiki wanga.’

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku.”
Kapena kuti, “Ku Negebu mʼdziko.”