1 Samueli 29:1-11

  • Afilisiti sanakhulupirire Davide (1-11)

29  Afilisiti+ anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Aisiraeli anamanga msasa pafupi ndi kasupe wa ku Yezereeli.+  Olamulira a Afilisiti ankadutsa ndi magulu awo a asilikali 100 ndi 1,000, ndipo Davide ndi amuna amene ankayenda naye ankabwera pambuyo pawo limodzi ndi Akisi.+  Ndiyeno akalonga a Afilisiti anafunsa kuti: “Kodi Aheberiwa akudzatani kuno?” Akisi anayankha akalonga a Afilisitiwo kuti: “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Mfumu Sauli ya Isiraeli. Iye wakhala ndi ine kwa chaka chimodzi kapena kuposa.+ Kuyambira tsiku limene anathawira kwa ine mpaka lero, sindinamupeze ndi vuto lililonse.”  Koma akalonga a Afilisiti anamʼpsera mtima kwambiri Akisi ndipo anati: “Muuzeni abwerere,+ apite kumalo amene munamʼpatsa. Musamulole kuti apite nafe kunkhondo chifukwa akhoza kukatitembenukira.+ Mukuganiza kuti munthu ameneyu angachite chiyani kuti mbuye wake amukonde? Akaphatu asilikali athu.  Kodi ameneyu si Davide uja amene ankamuimbira nyimbo kwinaku akuvina nʼkumati: ‘Sauli wapha adani ake masauzande,Ndipo Davide wapha masauzande ambirimbiriʼ?”+  Choncho Akisi+ anaitana Davide nʼkumuuza kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, iweyo ndiwe wolungama ndipo ndikanakonda kupita nawe kunkhondo,+ chifukwa sindinakupeze ndi vuto lililonse kuyambira tsiku limene unabwera kwa ine mpaka lero.+ Koma olamulira ena sakukukhulupirira.+  Ndiye bwerera mwamtendere ndipo usachite chilichonse chimene chingakhumudwitse olamulira a Afilisiti.”  Koma Davide anayankha Akisi kuti: “Ndibwerere chifukwa chiyani? Ndakulakwirani chiyani ine mtumiki wanu, kuyambira tsiku limene ndinabwera kudzakhala nanu mpaka lero? Ndisapite kukamenyana ndi adani anu mbuyanga mfumu chifukwa chiyani?”  Akisi anayankha Davide kuti: “Ineyo ndikuona kuti wakhala ukuchita zabwino ngati mngelo wa Mulungu.+ Koma akalonga a Afilisiti ndi amene anena kuti, ‘Musamulole kuti apite nafe kunkhondo.’ 10  Choncho udzuke mʼmamawa pamodzi ndi atumiki a mbuye wako amene unabwera nawo limodzi. Mukangoona kuti kwayera, munyamuke.” 11  Choncho Davide anadzuka mʼmamawa pamodzi ndi amuna amene ankayenda naye nʼkubwerera kudziko la Afilisiti. Koma Afilisitiwo anapita ku Yezereeli.+

Mawu a M'munsi