1 Samueli 3:1-21

  • Samueli anaitanidwa kuti akhale mneneri (1-21)

3  Pa nthawi imeneyo, mwana uja Samueli ankatumikira+ Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Koma mawu a Yehova anali osowa masiku amenewo ndipo anthu sankaona masomphenya+ pafupipafupi.  Tsiku lina Eli anali atagona kuchipinda kwake. Pa nthawiyi, maso ake anali atachita mdima ndipo sankaona.+  Nyale ya Mulungu+ inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona mʼkachisi*+ wa Yehova mmene munali Likasa la Mulungu.  Kenako Yehova anaitana Samueli ndipo iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga.”  Choncho anathamangira kwa Eli nʼkunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, ndamva kuitana.” Koma Eli anamuuza kuti: “Sindinakuitane. Pita ukagone.” Atatero Samueli anapita kukagonanso.  Yehova anamuitananso kuti: “Samueli!” Ndiyeno Samueli anadzuka nʼkupitanso kwa Eli kukanena kuti: “Ndabwera chifukwa ndamva mukundiitana.” Koma Eli anamuuza kuti: “Sindinakuitane mwana wanga. Pita ukagone.”  (Pa nthawiyi Samueli anali asanadziwe Yehova ndipo Yehova anali asanayambe kulankhula naye.)+  Ndiyeno Yehova anaitananso kachitatu kuti: “Samueli!” Choncho Samueli anadzuka nʼkupita kwa Eli, ndipo ananena kuti: “Ndabwera, chifukwa mwandiitana ndithu.” Zitatero Eli anazindikira kuti Yehova ndi amene ankaitana mwanayo.  Choncho Eli anauza Samueli kuti: “Pita ukagone, ndipo akakuitananso unene kuti, ‘Lankhulani Yehova, ine mtumiki wanu ndikumva.’” Ndiyeno Samueli anabwerera nʼkukagona. 10  Kenako Yehova anabwera nʼkuima pamalopo ndipo anaitananso ngati poyamba paja kuti: “Samueli! Samueli!” Samueli anayankha kuti: “Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumva.” 11  Ndiye Yehova anauza Samueli kuti: “Tamvera! Ndichita zinazake mu Isiraeli zoti munthu aliyense akadzamva mʼmakutu ake onse mudzalira.+ 12  Tsiku limenelo ndidzachitira Eli zonse zimene ndinanena zokhudza nyumba yake, kuyambira zoyambirira mpaka zomalizira.+ 13  Umuuze kuti ndidzaweruza nyumba yake mpaka kalekale chifukwa cha zinthu zolakwika zimene iye akuzidziwa.+ Ana ake akunyoza Mulungu+ koma sakuwadzudzula.+ 14  Nʼchifukwa chake ndalumbirira nyumba ya Eli kuti machimo a anthu a mʼnyumba ya Eli sadzaphimbidwa ndi nsembe ina iliyonse.”+ 15  Samueli anagonabe mpaka mʼmawa. Atadzuka anatsegula zitseko za nyumba ya Yehova, koma ankaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona. 16  Tsopano Eli anaitana Samueli kuti: “Samueli, mwana wanga!” Ndipo iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga.” 17  Ndiyeno Eli anamuuza kuti: “Kodi Mulungu wakuuza uthenga wotani? Chonde usandibisire. Mulungu akulange ndi kuwonjezerapo, ukandibisira ngakhale mawu amodzi pa mawu amene wakuuza.” 18  Choncho Samueli anamuuza zonse ndipo sanamʼbisire chilichonse. Zitatero Eli anati: “Ndi Yehova amene wanena. Achite zimene akuona kuti nʼzabwino.” 19  Samueli anapitiriza kukula ndipo Yehova anali naye,+ moti palibe mawu ake alionse amene sanakwaniritsidwe. 20  Aisiraeli onse kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba, anadziwa kuti Samueli ndi amene wasankhidwa kukhala mneneri wa Yehova. 21  Ndipo Yehova anapitiriza kuonekera ku Silo, popeza Yehova anathandiza Samueli kuti amudziwe bwino. Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mawu a Yehova.+

Mawu a M'munsi

Chimenechi chinali chihema.