1 Samueli 30:1-31

  • Aamaleki anaukira ndi kutentha mzinda wa Zikalaga (1-6)

    • Davide anapeza mphamvu kwa Mulungu (6)

  • Davide anagonjetsa Aamaleki (7-31)

    • Davide anapulumutsa anthu amene anatengedwa (18, 19)

    • Lamulo la Davide lokhudza zotengedwa kunkhondo (23, 24)

30  Davide ndi asilikali ake atafika ku Zikilaga+ tsiku lachitatu, anapeza kuti Aamaleki+ aukira anthu akumʼmwera* ndi amumzinda wa Zikilaga. Iwo anaukira mzindawo nʼkuutentha ndi moto.  Aamalekiwo anatenga akazi+ amumzindawo komanso anthu ena onse, kuyambira mwana mpaka wamkulu. Sanaphe aliyense koma anangowatenga nʼkumapita nawo.  Davide ndi anthu amene anali naye atafika, anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndipo akazi awo komanso ana awo aamuna ndi aakazi atengedwa.  Davide ndi anthuwo anayamba kulira mofuula mpaka anafooka osathanso kulira.  Akazi awiri a Davide nawonso anatengedwa, Ahinowamu wa ku Yezereeli ndi Abigayeli amene anali mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.+  Davide anali ndi nkhawa kwambiri chifukwa anthu ankakambirana zoti amuponye miyala. Anthuwo ankafuna kuchita zimenezi chifukwa anakwiya kwambiri ndi kutengedwa kwa ana awo aamuna ndi aakazi. Koma Davide anakhulupirira Yehova Mulungu wake ndipo anapeza mphamvu.+  Kenako Davide anauza Abiyatara+ wansembe, mwana wa Ahimeleki kuti: “Chonde bweretsa efodi.”+ Choncho Abiyatara anapititsa efodi kwa Davide.  Ndiyeno Davide anayamba kufunsa Yehova+ kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la achifwambali? Kodi ndiwapeza?” Iye anamuyankha kuti: “Inde athamangitse chifukwa uwapeza ndithu ndipo ukapulumutsa anthu amene awatenga.”+  Nthawi yomweyo, Davide ndi amuna 600+ amene anali naye ananyamuka nʼkuyenda mpaka kukafika kuchigwa cha Besori, ndipo amuna ena anatsala pamenepo. 10  Davide ndi amuna 400 anapitiriza ulendo wawo koma amuna 200 amene anatopa kwambiri moti sanathe kuwoloka chigwa cha Besori, anatsala pomwepo.+ 11  Ndiyeno anapeza munthu wina wa ku Iguputo patchire. Anamutenga nʼkupita naye kwa Davide ndipo anamupatsa chakudya ndi madzi akumwa. 12  Anamupatsanso keke ya nkhuyu zouma ndi makeke awiri a mphesa zouma. Atadya anapeza mphamvu, chifukwa anakhala osadya chakudya kapena kumwa madzi kwa masiku atatu, masana ndi usiku. 13  Kenako Davide anamufunsa kuti: “Ndiwe kapolo wa ndani, nanga kwanu nʼkuti?” Munthuyo anayankha kuti: “Ndine wa ku Iguputo, kapolo wa Mwamaleki, koma mbuyanga anandisiya pano masiku atatu apitawa nditayamba kudwala. 14  Tinakaukira kumʼmwera kwa dziko* la Akereti+ ndi dera la Yuda komanso kumʼmwera kwa dera* la Kalebe.+ Ndipo mzinda wa Zikilaga tinautentha ndi moto.” 15  Ndiyeno Davide anamufunsa kuti: “Kodi ungandilondolere kumene kuli gulu la achifwambali?” Iye anayankha kuti: “Ndilumbirireni pamaso pa Mulungu kuti simundipha, komanso kuti simundipereka mʼmanja mwa mbuyanga. Mukatero ndikulondolerani kumene kuli gulu la achifwambali.” 16  Choncho munthuyo analondolera Davide kumene kunali achifwambawo, ndipo anawapeza atamwazikana mʼdziko lonselo, akudya ndi kumwa komanso kusangalala chifukwa chakuti analanda zinthu zambiri mʼdziko la Afilisiti ndi la Yuda. 17  Ndiyeno Davide anayamba kuwapha kuyambira mʼbandakucha mpaka madzulo. Palibe aliyense amene anapulumuka kupatulapo amuna 400 amene anakwera ngamila nʼkuthawa.+ 18  Davide anatenga zonse zimene Aamaleki analanda+ ndipo anapulumutsanso akazi ake awiri aja. 19  Palibe chinthu chawo chilichonse chimene chinasowa, ngakhale chachingʼono. Anapulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi komanso zonse zimene anatenga.+ Davide anapulumutsa zonse zimene iwo anatenga. 20  Choncho Davide anatenga nkhosa zonse ndi ngʼombe zonse za Aamaleki ndipo anthu ake anapita nazo limodzi ndi ziweto zawo. Iwo anati: “Izi ndi zimene Davide walanda.” 21  Kenako Davide anafika kuchigwa cha Besori kumene kunali amuna 200 omwe anawasiya aja, amene sanathe kupita naye chifukwa anatopa kwambiri.+ Iwo ananyamuka nʼkukalandira Davide ndi anthu amene anali naye. Atakumana, Davide anawafunsa za moyo wawo. 22  Koma anthu ena oipa ndi opanda pake amene anatsatira Davide anati: “Chifukwa chakuti amenewa sanapite nawo, sitiwapatsa zinthu zimene talandazi. Aliyense tingomupatsa mkazi wake ndi ana ake, kenako azipita.” 23  Koma Davide anati: “Ayi abale anga, musatero ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watiteteza ndiponso wapereka mʼmanja mwathu gulu la achifwamba limene linadzatiukira.+ 24  Ndani angavomereze zimenezo? Zomwe alandire munthu amene anapita kunkhondo, zikhala zofanana ndi zimene alandire munthu amene amalondera katundu.+ Aliyense alandirapo kenakake.”+ 25  Ndipo kuyambira tsiku limenelo, iye anaonetsetsa kuti limeneli likhale lamulo loti Aisiraeli azitsatira mpaka lero. 26  Davide atafika ku Zikilaga anatumiza zina mwa zinthu zimene analandazo kwa akulu a ku Yuda omwe anali anzake nʼkunena kuti: “Landirani mphatsoyi* kuchokera pa zimene talanda kwa adani a Yehova.” 27  Anatumiza zimenezi kwa akulu a ku Beteli,+ a ku Ramoti wa ku Negebu,* a ku Yatiri,+ 28  a ku Aroweli, a ku Sifimoti, a ku Esitemowa,+ 29  a ku Rakala ndiponso kwa okhala mʼmizinda ya Ayerameeli+ ndi mʼmizinda ya Akeni.+ 30  Anatumizanso kwa akulu a ku Horima,+ a ku Borasani, a ku Ataki, 31  a ku Heburoni+ ndiponso kumadera onse kumene Davide ndi anthu ake ankafikako kawirikawiri.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ku Negebu.”
Kapena kuti, “ku Negebu mʼdera.”
Kapena kuti, “ku Negebu mʼdziko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dalitsoli.”
Kapena kuti, “wakumʼmwera.”