1 Samueli 31:1-13

  • Imfa ya Sauli ndi ana ake atatu (1-13)

31  Afilisiti anayamba kumenyana ndi Aisiraeli+ ndipo asilikali a Isiraeli ankathawa moti ambiri anaphedwa mʼphiri la Giliboa.+  Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake ndipo kenako anapha Yonatani,+ Abinadabu ndi Malikisuwa, ana aamuna a Sauli.+  Nkhondo inamʼkulira kwambiri Sauli, moti oponya mivi ndi uta anamupeza nʼkumuvulaza koopsa.+  Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako undibaye kuti anthu osadulidwawa+ asandipeze nʼkundipha mwankhanza.” Koma womunyamulira zidayo sankafuna chifukwa ankachita mantha kwambiri. Choncho Sauli anatenga lupanga lake nʼkuligwera.+  Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa,+ nayenso anagwera lupanga lake ndipo anafera limodzi.  Choncho Sauli, ana ake atatu, womunyamulira zida komanso asilikali ake onse anafera limodzi pa tsikuli.+  Aisiraeli amene ankakhala kuchigwa ndiponso mʼdera la Yorodano ataona kuti asilikali a Isiraeli athawa komanso kuti Sauli ndi ana ake afa, anachoka mʼmizinda yawo nʼkuthawa.+ Kenako Afilisiti anabwera kudzakhala mʼmizindayo.  Tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzatenga zinthu za anthu amene anaphedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa paphiri la Giliboa.+  Iwo anadula mutu wa Sauli nʼkumuvula zida zake. Kenako anauza anthu mʼdziko lonse la Afilisiti kuti afalitse uthengawu+ mʼnyumba* za mafano awo+ ndiponso kwa anthu awo. 10  Kenako anakaika zida zakezo mʼnyumba ya zifaniziro za Asitoreti ndipo anapachika mtembo wake pakhoma la mzinda wa Beti-sani.+ 11  Anthu a ku Yabesi-giliyadi+ atamva zimene Afilisiti anamuchita Sauli, 12  asilikali onse ananyamuka nʼkuyenda usiku wonse ndipo anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pakhoma la mzinda wa Beti-sani. Kenako anabwerera ku Yabesi nʼkutentha mitemboyo kumeneko. 13  Atatero, anatenga mafupa awo+ nʼkuwaika mʼmanda pansi pa mtengo wa bwemba ku Yabesi+ ndipo anasala kudya masiku 7.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mu akachisi.”