1 Samueli 5:1-12

  • Likasa linakhala mʼdziko la Afilisiti (1-12)

    • Dagoni anachititsidwa manyazi (1-5)

    • Afilisiti analangidwa (6-12)

5  Afilisiti atalanda Likasa+ la Mulungu woona, analitenga ku Ebenezeri nʼkupita nalo ku Asidodi.  Afilisitiwo anaika Likasa la Mulungu woonalo mʼnyumba* ya Dagoni ndipo analikhazika pafupi ndi Dagoniyo.+  Tsiku lotsatira anthu a ku Asidodi atadzuka mʼmawa, anapeza Dagoni atagwa chafufumimba patsogolo pa Likasa la Yehova.+ Zitatero, anatenga Dagoni nʼkumubwezeretsa pamalo ake.+  Atadzuka mʼmawa tsiku lotsatira, anapeza kuti Dagoni wagwanso chafufumimba patsogolo pa Likasa la Yehova. Mutu wa Dagoni ndi manja ake zinali zitaduka nʼkugwera pakhomo. Mbali yooneka ngati nsomba ndi imene inatsala.*  Nʼchifukwa chake ansembe a Dagoni ndi anthu onse omwe amalowa mʼnyumba ya Dagoni ku Asidodi saponda pakhomo la nyumba ya Dagoni mpaka lero.  Dzanja la Yehova linayamba kukhaulitsa anthu a ku Asidodi, ndipo linachititsa kuti anthu amumzinda wa Asidodi komanso madera ake ozungulira ayambe kudwala matenda a mudzi.*+  Anthu a ku Asidodi ataona zimenezi, anati: “Musalole kuti Likasa la Mulungu wa Isiraeli likhalebe kuno chifukwa iye watisautsa kwambiri pamodzi ndi mulungu wathu, Dagoni.”  Choncho anaitanitsa olamulira onse a Afilisiti nʼkuwafunsa kuti: “Tipange bwanji ndi Likasa la Mulungu wa Isiraeli?” Iwo anayankha kuti: “Likasa limeneli, la Mulungu wa Isiraeli, tilitumize ku Gati.”+ Choncho Likasa la Mulungu wa Isiraeli analipititsa kumeneko.  Atafika nalo kumeneko, dzanja la Yehova linakhaulitsanso anthu amumzindawo moti anasowa mtendere. Iye anachititsa kuti anthu onse a mumzindawo, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adwale matenda a mudzi.+ 10  Choncho anatumiza Likasa la Mulungu woona ku Ekironi.+ Ndiyeno Likasa la Mulungu woona litangofika ku Ekironi, anthu akumeneko anayamba kulira, kuti: “Atibweretsera Likasa la Mulungu wa Isiraeli kuti atiphe tonse!”+ 11  Kenako anaitanitsa olamulira onse a Afilisiti nʼkuwauza kuti: “Chotsani Likasa la Mulungu wa Isiraeli kuno, libwerere kwawo kuti anthufe tisaphedwe.” Ananena zimenezi chifukwa mumzinda wonsewo anthu ankaopa kuti afa, chifukwa dzanja la Mulungu woona linkawasautsa.+ 12  Anthu amene sanafe anadwala matenda a mudzi. Ndipo anthu amumzindawo ankalira mokweza moti mawu awo ankamveka kumwamba.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼkachisi.”
Kapena kuti, “Dagoni yekha ndi amene anatsala.”
Matendawa amachititsa kuti munthu atupe kotulukira chimbudzi ndipo nthawi zina amatha kutuluka thumbo.