1 Samueli 7:1-17

  • Likasa ku Kiriyati-yearimu (1)

  • Samueli anati: ‘Muzitumikira Yehova yekha’ (2-6)

  • Aisiraeli anapambana ku Mizipa (7-14)

  • Samueli anayamba kuweruza Aisiraeli (15-17)

7  Choncho amuna a ku Kiriyati-yearimu anabweradi nʼkutenga Likasa la Yehova ndipo anakaliika mʼnyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Ndiyeno anasankha* Eliezara mwana wake kuti azilondera Likasa la Yehova.  Kuchokera pamene Likasa linayamba kukhala ku Kiriyati-yearimu, panapita nthawi yaitali mpaka zinakwana zaka 20 ndipo Aisiraeli onse anayamba kufunafuna* Yehova.+  Kenako Samueli anauza Aisiraeli onse kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova ndi mtima wanu wonse,+ chotsani milungu yachilendo+ komanso zifaniziro za Asitoreti,+ ndipo muzitumikira Yehova yekha ndi mtima wanu wonse.+ Mukatero, adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisiti.”+  Choncho Aisiraeli anachotsa Abaala ndi zifaniziro za Asitoreti nʼkuyamba kutumikira Yehova yekha.+  Ndiyeno Samueli anawauza kuti: “Sonkhanitsani Aisiraeli onse pamodzi ku Mizipa,+ ndipo ndikakupemphererani kwa Yehova.”+  Choncho iwo anasonkhana pamodzi ku Mizipa, kenako anatunga madzi nʼkuwathira pansi pamaso pa Yehova ndipo anasala kudya tsiku limenelo.+ Iwo ananena kuti: “Tachimwira Yehova.”+ Ndipo Samueli anayamba kuweruza+ Aisiraeli ku Mizipa.  Afilisiti atamva kuti Aisiraeli asonkhana ku Mizipa, olamulira awo+ ananyamuka kuti akamenyane ndi Aisiraeli. Ndipo Aisiraeli atamva zimenezi, anachita mantha chifukwa cha Afilisitiwo.  Choncho Aisiraeli anauza Samueli kuti: “Musasiye kupemphera kwa Yehova Mulungu wathu kuti atithandize+ komanso kutipulumutsa mʼmanja mwa Afilisiti.”  Ndiyeno Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa nʼkumupereka nsembe yopsereza+ yathunthu kwa Yehova. Atatero anapemphera kwa Yehova kuti athandize Aisiraeli ndipo Yehova anamuyankha.+ 10  Pamene Samueli ankapereka nsembe yopsereza, Afilisiti anali akuyandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze+ Afilisiti. Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa ndi Aisiraeli.+ 11  Aisiraeli ananyamuka ku Mizipa nʼkuyamba kuthamangitsa Afilisiti ndipo ankawapha mpaka kumʼmwera kwa Beti-kara. 12  Kenako Samueli anatenga mwala+ nʼkuuimika pakati pa Mizipa ndi Yesana ndipo anaupatsa dzina lakuti Ebenezeri,* popeza anati: “Mpaka pano Yehova akutithandizabe.”+ 13  Choncho Afilisiti anagonjetsedwa ndipo sanabwerenso mʼdera la Isiraeli.+ Pa nthawi yonse imene Samueli anali moyo, Yehova sanalole kuti Afilisiti alowe mʼdera la Aisiraeli.+ 14  Komanso Aisiraeli anatenga mizinda imene Afilisitiwo analanda kuyambira ku Ekironi mpaka ku Gati. Kuwonjezera pamenepo, Aisiraeli anatenganso dera lawo lomwe Afilisiti anawalanda. Komanso pakati pa Aisiraeli ndi Aamori panali mtendere.+ 15  Samueli anapitiriza kuweruza Isiraeli kwa moyo wake wonse.+ 16  Chaka chilichonse Samueli ankapita ku Beteli,+ Giligala+ ndi Mizipa+ ndipo ankaweruza Aisiraeli mʼmadera onsewa. 17  Akazungulirazungulira, ankabwerera ku Rama+ chifukwa nʼkumene kunali nyumba yake, ndipo kumeneko ankaweruzanso Aisiraeli. Iye anamangira Yehova guwa lansembe kumeneko.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anayeretsa.”
Kapena kuti, “kulilira.”
Kutanthauza “Mwala wa Thandizo.”