Kalata Yoyamba Yopita kwa Timoteyo 1:1-20
1 Ndine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu molamulidwa ndi Mulungu amene ndi Mpulumutsi wathu komanso molamulidwa ndi Khristu Yesu, yemwe ndi chiyembekezo chathu.+
2 Ndikukulembera iwe Timoteyo,*+ mwana wanga weniweni+ mʼchikhulupiriro:
Mulungu Atate wathu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu akupatse kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere.
3 Nditatsala pangʼono kupita ku Makedoniya, ndinakupempha kuti ukhalebe ku Efeso. Ndikukupemphanso kuti ukhalebe komweko nʼcholinga choti uletse anthu ena kuti asamaphunzitse zosiyana ndi zimene timaphunzitsa,
4 ndiponso kuti asamamvere nkhani zonama+ ndi zofufuzana mibadwo ya makolo.* Zimenezi nʼzosathandiza,+ koma zimangoyambitsa nkhani zopanda umboni ndipo siziphunzitsa anthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro.
5 Cholinga cha malangizo amenewa nʼchakuti tikhale ndi chikondi+ chochokera mumtima woyera, mʼchikumbumtima chabwino ndiponso mʼchikhulupiriro+ chopanda chinyengo.
6 Anthu ena akana kutsatira zimenezi ndipo asocheretsedwa nʼkuyamba kutsatira nkhani zopanda pake.+
7 Anthu amenewa amafuna kukhala aphunzitsi+ a chilamulo koma samvetsa zimene akunena kapena mfundo zimene akuzilimbikira.
8 Tikudziwa kuti Chilamulo nʼchabwino ngati munthu akuchigwiritsa ntchito moyenera.
9 Ndipotu lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Koma limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo,+ oukira, osaopa Mulungu, ochimwa, osakhulupirika, onyoza zinthu zopatulika, opha abambo ndi amayi awo, opha anthu,
10 achiwerewere,* amuna amene amagonana ndi amuna anzawo, oba anthu, abodza, olumbira monama ndiponso ochita china chilichonse chosagwirizana ndi mfundo zolondola zimene Mulungu amaphunzitsa.+
11 Mfundozi nʼzogwirizana ndi uthenga wabwino waulemerero wochokera kwa Mulungu wachimwemwe, umene anauika mʼmanja mwanga.+
12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye wathu, amene anandipatsa mphamvu nʼkundipatsanso utumiki chifukwa anaona kuti ndine wokhulupirika.+
13 Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.+ Komabe anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita zinthu mosadziwa komanso ndinalibe chikhulupiriro.
14 Koma ndinalandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu Ambuye wathu. Ndinalandiranso chikhulupiriro ndi chikondi cha Khristu Yesu.
15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona komanso oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+
16 Komabe, ndinachitiridwa chifundo kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa kwambiri, kuti chikhale chitsanzo kwa amene adzamukhulupirire nʼcholinga choti adzapeze moyo wosatha.+
17 Kwa Mulungu yekhayo+ yemwe ndi Mfumu yamuyaya,+ amene saafa+ komanso wosaoneka,+ kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka kalekale. Ame.
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukulangiza kuchita zimenezi mogwirizana ndi maulosi amene ananeneratu za iwe, kuti mogwirizana ndi maulosiwo upitirize kumenya nkhondo yabwino.+
19 Ukhale ndi chikhulupiriro komanso chikumbumtima chabwino+ chimene anthu ena asiya kuchitsatira, moti chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa.
20 Ena mwa anthuwa ndi Hemenayo+ ndi Alekizanda, ndipo ndawapereka kwa Satana+ kuti akalangidwa, aphunzirepo kanthu nʼkusiya kunyoza Mulungu.
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza “Amene Amalemekeza Mulungu.”
^ Kapena kuti, “kukumbana mibadwo ya makolo.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.