Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 1:1-24

  • Mawu oyamba (1, 2)

  • Mulungu amatitonthoza pa vuto lililonse (3-11)

  • Paulo anasintha mapulani a ulendo wake (12-24)

1  Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu, limodzi ndi Timoteyo+ mʼbale wathu, ndikulembera mpingo wa Mulungu wa ku Korinto komanso oyera onse amene ali ku Akaya konse:+  Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.  Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ Bambo wachifundo chachikulu+ ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,+  amenenso amatitonthoza* pa mayesero* athu onse,+ kuti tithe kutonthoza amene akukumana ndi mayesero*+ amtundu uliwonse, chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.+  Popeza tikukumana ndi mavuto ambiri chifukwa cha Khristu,+ tikutonthozedwanso kwambiri kudzera mwa Khristu.  Tikakumana ndi mayesero,* inuyo mumatonthozedwa ndiponso kupulumutsidwa. Tikatonthozedwa, nanunso mumatonthozedwa ndipo zimenezi zimathandiza kuti mupirire mavuto amene nafenso tikukumana nawo.  Chiyembekezo chathu pa inu sichikugwedezeka, chifukwa tikudziwa kuti popeza mukukumana ndi mavuto ofanana ndi amene ifeyo tikukumana nawo, nanunso mudzatonthozedwa.+  Abale, tikufuna muzidziwa za mavuto amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asia.+ Tinakumana ndi mavuto aakulu oposa mphamvu zathu, moti tinalibe chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.+  Ndipotu tinkangomva ngati taweruzidwa kuti tiphedwe. Izi zinali choncho kuti tisamadzidalire koma tizidalira Mulungu+ amene amaukitsa akufa. 10  Iye anatipulumutsa ku zinthu zimenezi zomwe zikanatha kutipha ndipo adzatipulumutsanso. Tikukhulupirira kuti iye apitiriza kutipulumutsa.+ 11  Inunso mungathandizepo potipempherera mochonderera,+ kuti pakhale anthu ambiri otiperekera mapemphero oyamikira thandizo limene Mulungu amatipatsa poyankha mapemphero a anthu ambiri.+ 12  Ifeyo tili ndi chifukwa chodzitamandira, ndipo chikumbumtima chathu chikutichitiranso umboni, kuti mʼdzikoli, makamaka pakati pa inuyo, tachita zinthu zoyera ndiponso mogwirizana ndi kuona mtima kochokera kwa Mulungu. Tachita zimenezi osati modalira nzeru za mʼdzikoli,+ koma modalira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. 13  Chifukwa zimene tikukulemberanizi ndi zinthu zoti mukhoza kuziwerenga* ndiponso kuzimvetsa. Ndipo ndikukhulupirira kuti mupitiriza kuzimvetsa bwino* zinthu zimenezi. 14  Mukudziwa kale kuti ifeyo ndife chifukwa choti inuyo mudzitamandire, ngati mmene inuyonso mudzakhalire chifukwa choti ifeyo tidzadzitamandire pa tsiku la Ambuye wathu Yesu. 15  Popeza sindikukayikira za zimenezi, ndinali ndi cholinga choti choyamba ndibwere kwanuko, kuti mudzakhalenso ndi mwayi wina wosangalala.* 16  Chifukwa ndinkafuna kuti ndikamapita ku Makedoniya ndidzadutsire kwanuko kudzakuchezerani, ndipo ndikadzachoka ku Makedoniya ndidzabwerenso kwanuko kenako mudzandiperekeze popita ku Yudeya.+ 17  Pamene ndinali ndi cholinga chimenechi, kodi nkhaniyi ndinkaiona mopupeka? Kapena kodi ndinali ndi zolinga zadyera kuti ndikati “Inde, inde” nthawi yomweyo ndisinthe ndinene kuti “Ayi, ayi”? 18  Koma khulupirirani Mulungu kuti zimene tinakuuzani ndi zoona. Sitingakuuzeni kuti Inde, kenako Ayi. 19  Popeza Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene ineyo, Silivano* ndi Timoteyo+ tinakulalikirani za iye, sanakhale “inde” kenako “ayi,” koma “inde” wakhalabe “inde.” 20  Ndiponso malonjezo a Mulungu, kaya akhale ambiri bwanji, akhala “inde” kudzera mwa iye.+ Choncho kudzeranso mwa iye, “Ame” amanenedwa kwa Mulungu+ ndipo Mulungu amalandira ulemerero kudzera mwa ife. 21  Koma Mulungu ndi amene amatitsimikizira kuti inuyo ndi ifeyo ndife a Khristu ndiponso ndi amene anatidzoza.+ 22  Iye watidinda chidindo chake.+ Chidindo chimenechi ndi mzimu woyera+ womwe uli mʼmitima mwathu ndipo uli ngati madalitso amʼtsogolo. 23  Mulungu ndi mboni yanga kuti chifukwa chimene sindinabwerere ku Korintoko mpaka pano nʼchakuti sindinafune kudzawonjezera chisoni chanu. 24  Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu,+ koma ndife antchito anzanu kuti muzisangalala, popeza ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amatilimbikitsa.”
Kapena kuti, “mʼmasautso.”
Kapena kuti, “masautso.”
Kapena kuti, “masautso.”
Mabaibulo ena amati, “mukuzidziwa kale.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mupitiriza kuzimvetsa mpaka pamapeto.”
Mabaibulo ena amati, “kuti mudzapindule kawiri.”
Amatchedwanso Sila.