Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 11:1-33

  • Paulo ndiponso atumwi apamwamba (1-15)

  • Mavuto amene mtumwi Paulo anakumana nawo (16-33)

11  Ndikanakonda kuti mundilole ndidzikweze pangʼono. Ndipotu zoona zake nʼzakuti, mwandilola kale. 2  Ndikukuchitirani nsanje, ngati imene Mulungu amakuchitirani, popeza ndine ndinakuchititsani kulonjezedwa ukwati ndi mwamuna mmodzi, Khristu, ndipo ndikufuna kukuperekani ngati namwali woyera kwa iye.+ 3  Mofanana ndi mmene njoka inanamizira Hava ndi chinyengo chake,+ nkhawa yanga ndi yakuti mwina maganizo anunso angapotozedwe moti simungakhalenso oona mtima ndiponso oyera. Koma munthu wa Khristu amafunika kukhala woona mtima komanso woyera.+ 4  Chifukwa wina akabwera kwa inu nʼkulalikira za Yesu wosiyana ndi amene tinamulalikira, kapena akakubweretserani mzimu wosiyana ndi umene munalandira kale, kapena uthenga wabwino wosiyana ndi umene munaulandira,+ inu mumangomulandira munthu woteroyo. 5  Koma ine ndikuona kuti sindikuchepa mwanjira iliyonse poyerekeza ndi atumwi anu apamwambawo.+ 6  Ngati ndilibe luso la kulankhula,+ sikuti ndine wosadziwanso zinthu ndipo tinakusonyezani zimenezi mʼnjira iliyonse komanso pa zinthu zonse. 7  Kapena kodi ndinalakwa pamene ndinadzichepetsa kuti inuyo mukwezedwe, muja ndinalalikira mosangalala uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu, popanda inuyo kulipira?+ 8  Ndinalandira chithandizo kuchokera kumipingo ina ndipo zinali ngati ndikuwabera nʼcholinga choti nditumikire inuyo.+ 9  Koma pamene ndinasowa zofunika zina ndili kwanuko, sindinalemetse munthu aliyense, popeza abale amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkafunikira.+ Ndithu, ndinayesetsa kuti ndisakulemetseni mʼnjira iliyonse, ndipo ndipitirizabe kutero.+ 10  Ndikulankhula choonadi cha Khristu, choncho sindidzasiya kudzitamandira+ mʼmadera a ku Akaya. 11  Kodi ndikuchita zimenezi chifukwa chiyani? Chifukwa sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani. 12  Ndipitiriza kuchita zimene ndikuchita,+ kuti nditsekereze anthu amene akuyesetsa kupeza chifukwa chonenera kuti ndi ofanana ndi ife pa zinthu zimene amadzitamandira. 13  Anthu amenewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo ndipo amadzichititsa kuoneka ngati atumwi a Khristu.+ 14  Zimenezi nʼzosadabwitsa, popeza ngakhale Satana amadzichititsa kuoneka ngati mngelo wa kuwala.+ 15  Choncho nʼzosadabwitsa ngati atumiki ake nawonso amadzichititsa kukhala ngati atumiki a chilungamo. Koma mapeto awo adzakhala ogwirizana ndi ntchito zawo.+ 16  Ndikubwerezanso kunena kuti, munthu aliyense asandione ngati wopanda nzeru. Koma ngati mukundiona kuti ndine wopanda nzeru, ingovomerezani kuti ndi mmene ndilili, kuti nanenso ndidzitame pangʼono. 17  Zimene ndikulankhulazi, sindikulankhula ngati munthu wotsatira chitsanzo cha Ambuye. Koma ngati munthu wopanda nzeru ndiponso wodzitama ndi wodzidalira kwambiri. 18  Popeza anthu ambiri akudzitama pa zinthu zamʼdzikoli, inenso ndidzitama. 19  Simuvutika kuchita zinthu ndi anthu opanda nzeru popeza mumadziona kuti ndinu anzeru kwambiri. 20  Ndipotu mumalolera aliyense wokuchititsani kukhala akapolo, wotenga zinthu zanu, wolanda zimene muli nazo, wodziona kuti ndi wapamwamba kuposa inuyo ndiponso aliyense wokuwombani mbama. 21  Ndikunena zimenezi modzinyoza tokha, popeza tikuoneka ngati tachita zinthu mofooka. Koma ngati anthu ena akuchita zinthu molimba mtima, ndikulankhula ngati wopanda nzeru, inenso ndikuchita zinthu molimba mtima. 22  Kodi iwo ndi Aheberi? Inenso chimodzimodzi.+ Kodi ndi Aisiraeli? Nanenso. Kapena iwo ndi mbadwa* za Abulahamu? Inenso chimodzimodzi.+ 23  Kapena kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankha ngati wamisala, ineyo ndiye mtumiki wa Khristu woposa iwowo. Ndachita zambiri kuposa iwowo,+ ndinamangidwa kambirimbiri,+ ndinamenyedwa kosawerengeka ndipo ndinabwererapo lokumbakumba kambirimbiri.+ 24  Maulendo 5 Ayuda anandikwapula zikwapu 40, kuchotsera chimodzi.+ 25  Katatu anandimenya ndi ndodo.+ Kamodzi anandiponya miyala.+ Ngalawa inandiswekerapo katatu.+ Kamodzi ndinakhala panyanja usiku ndi masana wonse. 26  Ndinayenda maulendo ambirimbiri, ndinakumana ndi zoopsa mʼmitsinje komanso ndinakumana ndi achifwamba pamsewu. Ndinakumananso ndi zoopsa kuchokera kwa anthu a mtundu wanga,+ anthu a mitundu ina,+ mumzinda,+ mʼchipululu, panyanja ndi pakati pa abale achinyengo. 27  Ndinkagwira ntchito zowawa komanso zotulutsa thukuta. Nthawi zambiri usiku sindinkagona,+ ndinkakhala ndi njala ndiponso ludzu+ ndipo nthawi zambiri ndinkakhala osadya,+ ndinkazizidwa komanso ndinalibe zovala zokwanira.* 28  Kuwonjezera pa zinthu zimenezi, palinso chinthu china chomwe panopa chimandivutitsa maganizo tsiku ndi tsiku. Ndimadera nkhawa mipingo yonse.+ 29  Ndani angafooke, inenso osafooka? Ndani angakhumudwitsidwe, ine osakwiya nazo? 30  Ngati ndikuyenera kudzitama, ndidzadzitama pa zinthu zimene zimasonyeza zofooka zanga. 31  Mulungu ndiponso Atate wa Ambuye Yesu, amene ndi woyenera kutamandidwa mpaka kalekale, akudziwa kuti sindikunama. 32  Ku Damasiko, bwanamkubwa wa mfumu Areta anaika alonda mʼmageti a mzinda wa Damasiko kuti andigwire. 33  Koma anthu anandiika mʼdengu nʼkunditsitsira pawindo la mpanda wa mzindawo+ ndipo ndinapulumuka mʼmanja mwake.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinkakhala osavala.”