Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 12:1-21

  • Masomphenya a Paulo (1-7a)

  • “Minga mʼthupi” la Paulo (7b-10)

  • Sankachepa poyerekezera ndi atumwi apamwamba (11-13)

  • Paulo ankadera nkhawa Akorinto (14-21)

12  Ndikuyenera kudzitama. Choncho ndilankhula nkhani yokhudza masomphenya+ ndi mauthenga ochokera kwa Ambuye,+ ngakhale kuti kudzitama kulibe phindu.  Ndikudziwa munthu wina wogwirizana ndi Khristu. Zaka 14 zapitazo, munthu ameneyu anatengedwa nʼkupita naye kumwamba kwachitatu. Kaya anatengedwa ali ndi thupi lake lenileni kapena ayi, sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu.  Zoonadi, ndikumudziwa munthu ameneyu. Kaya anatengedwa ali ndi thupi lake lenileni kapena ayi, sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu.  Iye anatengedwa nʼkupita naye mʼparadaiso, ndipo ali mʼparadaisomo anamva mawu amene munthu sangawatchule komanso nʼkosaloleka kuwanena.  Ndidzitama pa nkhani yokhudza munthu ameneyo, koma sindidzitama za ineyo, kupatulapo pa zofooka zanga.  Koma ngakhale nditafuna kudzitama, sikuti ndikudzikweza, chifukwa ndikhala kuti ndikunena zoona. Koma sindichita zimenezo, popeza sindikufuna kuti wina anditamande kwambiri kuposa pa zinthu zimene akuona kapena kumva kwa ine,  chifukwa choti ndinaonetsedwa masomphenya apadera. Koma kuti ndisadzikweze mopitirira malire, ndinapatsidwa minga* mʼthupi+ mwanga imene imandibaya, imakhala ngati mngelo wa Satana ndipo imachititsa kuti ndizimva kuwawa nthawi zonse, nʼcholinga choti ndisadzikweze mopitirira malire.  Katatu konse ndinachonderera Ambuye za nkhaniyi kuti mingayi indichoke.  Koma anandiuza kuti: “Kukoma mtima kwakukulu kumene ndakusonyeza nʼkokwanira, chifukwa mphamvu zanga zimaonekera bwino kwambiri iweyo ukakhala wofooka.”+ Choncho mosangalala kwambiri, ndidzadzitama pa zofooka zanga, kuti mphamvu za Khristu zikhalebe pamutu panga ngati tenti. 10  Choncho ndimasangalala ndi kufooka, kunyozedwa, kusowa zofunika pa moyo, kuzunzidwa ndiponso zovuta zina chifukwa cha Khristu. Chifukwa pamene ndili wofooka, mʼpamene ndimakhala wamphamvu.+ 11  Tsopano ndakhala munthu wodzikweza. Koma ndi inuyo amene mwandikakamiza kuchita zimenezi, chifukwa munayenera kundiyamikira pa zabwino zimene ndachita. Ineyo sindikuchepa mwanjira ina iliyonse poyerekezera ndi atumwi anu apamwambawo, ngakhale kuti mumandiona ngati si ine kanthu.+ 12  Ndithudi inuyo munaona umboni wakuti ndine mtumwi. Munaona kuti ndinapirira kwambiri,+ ndinachita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndiponso ntchito zamphamvu.+ 13  Kodi pali njira inanso yomwe tingati munali ndi mwayi wochepa kuyerekezera ndi mipingo yonse, kupatulapo kuti ineyo sindinakhale katundu wolemetsa kwa inu?+ Chonde ndikhululukireni tchimo limeneli lakuti sindinakhale katundu wolemetsa kwa inu. 14  Ndine wokonzeka kubwera kwa inu ndipo kano ndi kachitatu kukhala wokonzeka. Koma sindidzakhala katundu wolemetsa chifukwa sindikufuna zinthu zanu,+ koma inuyo. Paja si udindo wa ana+ kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira chuma ana awo. 15  Koma ineyo ndidzagwiritsa ntchito zinthu zanga zonse komanso ndidzadzipereka ndi mtima wanga wonse chifukwa cha inu, ndipo ndidzachita zimenezi mosangalala.+ Ngati ineyo ndimakukondani kwambiri chonchi, kodi inuyo mukuyenera kundikonda pangʼono? 16  Koma mulimonsemo, sindinakulemetseni.+ Komabe inuyo mumanena kuti, ndinakupusitsani ndiponso ndinachita zachinyengo. 17  Koma inunso mukudziwa kuti sindinakudyereni masuku pamutu kudzera mwa aliyense wa anthu amene ndinawatumiza kwa inu. 18  Ndinalimbikitsa Tito kuti abwere kumeneko ndipo ndinamutumiza limodzi ndi mʼbale wina. Titoyo sanakudyereni masuku pamutu ngakhale pangʼono.+ Tinayenda mumzimu umodzi ndipo tinachita zinthu mofanana. Si choncho? 19  Kodi mwakhala mukuganiza kuti tikudziikira kumbuyo pamaso panu? Tikulankhula pamaso pa Mulungu mogwirizana ndi Khristu. Komatu okondedwa, tikuchita zonsezi kuti tikulimbikitseni. 20  Ndikuopa kuti ndikadzafika, mwina sindidzakupezani mmene ndikufunira ndipo mwina inenso sindidzakhala mmene mukufunira. Mʼmalomwake, nʼkutheka kuti padzakhala ndewu, nsanje, kukwiyitsana, mikangano, miseche, manongʼonongʼo, kudzitukumula ndiponso chipwirikiti. 21  Mwina ndikadzabweranso, Mulungu wanga adzalola kuti ndichite manyazi pamaso panu. Ndipo mwina ndidzalirira anthu ambiri amene anachimwa koma sanalape pa khalidwe lawo lonyansa, chiwerewere* ndiponso khalidwe lawo lopanda manyazi* limene akhala akuchita.

Mawu a M'munsi

Apa akunena minga imodzi. Ena amati, “munga.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.