Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 3:1-18

  • Makalata otichitira umboni (1-3)

  • Atumiki a pangano latsopano (4-6)

  • Ulemerero wa pangano latsopano ndi waukulu (7-18)

3  Kodi tikuyambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi nʼkofunika kuti ifenso, mofanana ndi anthu ena, tikhale ndi makalata otichitira umboni obwera kwa inu kapena ochokera kwa inu?  Inuyo ndinu kalata yathu,+ yolembedwa mʼmitima yathu, yodziwika ndiponso yowerengedwa ndi anthu onse.  Chifukwa zikuonekeratu kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu yolembedwa ndi ifeyo atumiki a Mulungu.+ Kalatayo si yolembedwa ndi inki koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo. Si yolembedwa pazolembapo zamiyala+ koma mʼmitima.*+  Kudzera mwa Khristu, tikhoza kunena zimenezi molimba mtima pamaso pa Mulungu.  Sitinganene kuti ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha mphamvu zathu, koma ndife oyenera kugwira ntchitoyi chifukwa cha Mulungu,+  ndipo iyeyo anationa kuti ndife oyenera kukhala atumiki a pangano latsopano,+ osati kudzera mʼmalamulo olembedwa,+ koma kudzera mu mzimu. Malamulo olembedwa amaweruza munthu kuti afe,+ koma mzimu umapatsa munthu moyo.+  Malamulo amene amachititsa kuti munthu afe, amenenso analembedwa pamiyala,+ anabwera ndi ulemerero waukulu kwambiri moti Aisiraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa inkawala ndi ulemerero+ umene unatha patapita nthawi.  Ndiye kodi mzimu sukuyenera kuperekedwa+ ndi ulemerero waukulu kuposa pamenepa?+  Ngati malamulo oweruza anthu kuti alangidwe+ anaperekedwa ndi ulemerero,+ chilungamo chikuyenera kuperekedwa ndi ulemerero woposa pamenepo.+ 10  Nawonso malamulo olembedwa amene anapatsidwa ulemerero, achotsedwa ulemererowo chifukwa ulemerero umene wabwera pambuyo pake ndi waukulu kuposa woyambawo.+ 11  Ngati malamulo olembedwa, amene anatha patapita nthawi, anaperekedwa ndi ulemerero,+ ndiye kuti malamulo amene sadzatha adzakhala ndi ulemerero waukulu kuposa pamenepo.+ 12  Popeza tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ tili ndi ufulu wambiri wolankhula, 13  osati ngati Mose amene ankaphimba nkhope yake ndi nsalu,+ kuti Aisiraeli asaone kutha kwa ulemerero wosakhalitsawo. 14  Ndipo maganizo awo anachita khungu.+ Mpaka lero, nsaluyo imakhalabe yophimba pangano lakale likamawerengedwa,+ chifukwa imachotsedwa kudzera mwa Khristu basi.+ 15  Ndipotu mpaka pano, zimene Mose analemba zikamawerengedwa,+ mitima yawo imakhalabe yophimba.+ 16  Koma munthu akasintha nʼkuyamba kulambira Yehova,* chophimbacho chimachotsedwa.+ 17  Yehova* ndi Mzimu+ ndipo pamene pali mzimu wa Yehova,* pali ufulu.+ 18  Tonsefe tili ndi nkhope zosaphimba ndipo tili ngati magalasi amene amaonetsa ulemerero wa Yehova.* Tikamaonetsa ulemererowu, timasintha nʼkukhala ngati chifaniziro chake ndipo timaonetsa ulemerero wowonjezerekawonjezereka* mofanana ndendende ndi mmene Yehova,* amene ndi Mzimu, watisinthira.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “zolembapo zamnofu, mʼmitima.”
Mabaibulo ena amati, “mwa mzimu wa Yehova.”