Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 5:1-21

  • Kuvala nyumba ya kumwamba (1-10)

  • Utumiki wogwirizanitsa anthu ndi Mulungu (11-21)

    • Cholengedwa chatsopano (17)

    • Akazembe mʼmalo mwa Khristu (20)

5  Tikudziwa kuti nyumba yathu yapadziko lapansi pano kapena kuti tenti ino, ikadzaphwasuka,+ tidzalandira nyumba yochokera kwa Mulungu. Imeneyo idzakhala nyumba yosamangidwa ndi manja,+ koma yamuyaya ndipo idzakhala kumwamba.  Chifukwa mʼnyumba imene tikukhalayi tikubuula ndipo tikufunitsitsa kuvala nyumba yathu yakumwamba,+  ndipo tikadzaivala, sitidzapezeka amaliseche.  Ndipotu, ife amene tili mutenti ino tikubuula komanso tikulemedwa, osati chifukwa chofuna kuivula, koma kuti tivale nyumba inayo,+ nʼcholinga choti thupi loti lingathe kufali lilowedwe mʼmalo ndi moyo.+  Amene anatikonzekeretsa kuti tilandire zimenezi ndi Mulungu.+ Iye ndi amenenso anatipatsa mzimu kuti ukhale ngati chikole cha zinthu zamʼtsogolo.+  Choncho nthawi zonse timakhala olimba mtima ndipo tikudziwa kuti pamene nyumba yathu ili thupili, tili kutali ndi Ambuye.+  Chifukwa tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro, osati motsogoleredwa ndi zooneka ndi maso.  Koma tikulimba mtima ndipo ndife osangalala kukakhala ndi Ambuye, mʼmalo mokhala mʼthupili.+  Choncho kaya tikhale naye pafupi kapena tikhale naye kutali, cholinga chathu nʼchakuti tikhale ovomerezeka kwa iye. 10  Chifukwa aliyense wa ife adzaonekera kumpando woweruzira milandu wa Khristu, kuti alandire mphoto yake mogwirizana ndi zimene anachita ali mʼthupi, kaya zabwino kapena zoipa.+ 11  Choncho popeza timaopa Ambuye, tikupitiriza kukopa anthu ndipo Mulungu akudziwa bwino zolinga zathu. Koma ndikukhulupirira kuti inunso, chikumbumtima chanu chikudziwa bwino zolinga zathu. 12  Sikuti tayambanso kudzichitira umboni tokha kwa inu. Koma tikukupatsani chifukwa chodzitamandira chifukwa cha ife, kuti muwayankhe amene amadzitama potengera maonekedwe akunja,+ osati zimene zili mumtima. 13  Ngati tinachita misala,+ tinachitira Mulungu. Koma ngati tili olongosoka, ndi zothandiza kwa inuyo. 14  Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse,+ chifukwatu onsewo anali atafa kale. 15  Iye anafera onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha,+ koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera nʼkuukitsidwa. 16  Kuyambira panopa sitiona munthu mwakuthupi.+ Ngakhale titakhala kuti Khristu tinamuonapo mwakuthupi, panopa sitikumuonanso choncho.+ 17  Ndiye ngati aliyense ali wogwirizana ndi Khristu, iye ndi cholengedwa chatsopano.+ Zinthu zakale zinatha, ndipo pali zatsopano. 18  Koma zinthu zonse nʼzochokera kwa Mulungu, amene anatithandiza kuti tigwirizane naye kudzera mwa Khristu,+ ndipo anatipatsa utumiki wothandiza kuti anthu agwirizanenso ndi Mulungu.+ 19  Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu ankagwirizanitsa dziko ndi iyeyo kudzera mwa Khristu,+ moti sanawawerengere anthuwo zolakwa zawo,+ ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolalikira uthenga wothandiza anthu kugwirizananso ndi Mulungu.+ 20  Choncho ndife akazembe+ mʼmalo mwa Khristu,+ ngati kuti Mulungu akuchonderera anthu kudzera mwa ife. Monga anthu amene akugwira ntchito mʼmalo mwa Khristu tikupempha kuti: “Gwirizananinso ndi Mulungu.” 21  Amene analibe uchimoyo,+ Mulungu anamuchititsa kukhala uchimo* chifukwa cha ife, kuti kudzera mwa iye Mulungu azitiona kuti ndife olungama.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nsembe yamachimo.”