Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 8:1-24

  • Zopereka za Akhristu a ku Yudeya (1-15)

  • Tito anatumizidwa ku Korinto (16-24)

8  Tsopano abale, tikufuna kukudziwitsani za kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wasonyeza mipingo ya ku Makedoniya.+ 2  Pamene iwo ankakumana ndi mayesero aakulu chifukwa cha mavuto, ankasangalala kwambiri ndiponso anasonyeza kuwolowa manja ngakhale kuti anali pa umphawi wadzaoneni. 3  Iwo anachita mogwirizana ndi zimene akanatha,+ komanso ndikuwachitira umboni kuti anachita ngakhale zoposa pamenepo,+ 4  ndipo anayamba okha kutipempha mochokera pansi pa mtima kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo kuti achite nawo utumiki wothandiza oyerawo.+ 5  Ndipo sanachite zimene tinkayembekezera zokha, koma choyamba anayesetsa ndi mtima wonse kutumikira Ambuye ndipo anatithandiza ifeyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. 6  Choncho tinalimbikitsa Tito+ kuti, popeza iye ndi amene anayambitsa ntchito yotolera zopereka zanu, iyeyo amalizitsenso kusonkhanitsa mphatso zanu zachifundo. 7  Inuyo mukuchita bwino pa chilichonse. Chikhulupiriro chanu ndi cholimba, muli ndi luso la kulankhula, mumadziwa zambiri, mumachita zinthu zonse mwakhama ndiponso mumakonda ena mmene ife timakukonderani. Choncho pitirizaninso kukhala ndi mtima wofuna kupereka.+ 8  Sindikukulamulani, koma ndikulankhula izi kuti mudziwe zimene ena achita mwakhama komanso kuti ndione ngati chikondi chanu chilidi chenicheni. 9  Chifukwa mukudziwa kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti ngakhale kuti anali wolemera, anakhala wosauka chifukwa cha inu,+ kuti inuyo mulemere kudzera mʼkusauka kwakeko. 10  Ndipereke maganizo anga pamenepa.+ Mungachite bwino kumalizitsa ntchito ya zoperekayi, chifukwa munaiyamba chaka chatha ndiponso munasonyeza mtima wofunitsitsa kuchita zimenezi. 11  Tsopano malizitsani ntchito imene munaiyamba. Popeza munkafunitsitsa kuchita zimenezi, mumalizitsenso kuzichita mogwirizana ndi zimene muli nazo. 12  Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angakwanitse,+ osati zimene sangakwanitse. 13  Sindikufuna kuti kwa ena zikhale zosavuta, koma kwa inu zikhale zovuta. 14  Koma ndikufuna kuti zinthu zambiri zimene muli nazo zithandize pa zimene iwowo alibe, ndipo zambiri zimene iwowo ali nazo zithandize pa zimene inuyo mulibe, kuti pakhale kufanana. 15  Mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Munthu amene anali ndi zambiri sanali ndi zopitirira muyezo, ndipo munthu amene anali ndi zochepa sanali ndi zoperewera.”+ 16  Tikuthokoza Mulungu chifukwa chothandiza Tito+ kuti azikuderani nkhawa ngati mmene ifeyo timachitira. 17  Iyeyo wamveradi zimene tinamulimbikitsa kuti achite, ndipo popeza akufunitsitsa kuthandiza, akubwera kumeneko mwa kufuna kwake. 18  Komanso tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale wina amene akutamandidwa mʼmipingo yonse chifukwa cha zimene akuchita zokhudza uthenga wabwino. 19  Si zokhazo, koma anasankhidwanso ndi mipingo kuti aziyenda nafe pamene tikubweretsa mphatso zachifundozi. Tikupereka mphatsozi kuti Ambuye alandire ulemerero komanso kuti tisonyeze kuti tikufunitsitsa kuthandiza ena. 20  Choncho sitikufuna kuti munthu aliyense atipezere chifukwa pa zopereka zaufulu zimene tikubweretsazi.+ 21  Chifukwa ‘timasamalira zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova* pokha, komanso pamaso pa anthu.’+ 22  Abalewa tikuwatumizanso limodzi ndi mʼbale wathu amene tamuyesa mobwerezabwereza ndipo taona kuti ndi wakhama pa zinthu zambiri. Panopa wasonyezanso kuti ndi wakhama kwambiri chifukwa akukukhulupirirani kwambiri. 23  Koma ngati mukukayikira zilizonse zokhudza Tito, ndikufuna ndikuuzeni kuti iye ndi mnzanga komanso ndikugwira naye ntchito limodzi pokuthandizani inuyo. Kapena ngati mungakayikire zilizonse zokhudza abale athuwa, iwo ndi nthumwi za mipingo ndipo amabweretsa ulemerero kwa Khristu. 24  Choncho asonyezeni kuti mumawakonda+ ndiponso musonyeze mipingo chifukwa chake timakunyadirani.

Mawu a M'munsi