Kalata Yachiwiri Yopita kwa Atesalonika 3:1-18

  • Pitirizani kupemphera (1-5)

  • Anawachenjeza kuti apewe makhalidwe osalongosoka (6-15)

  • Moni womaliza (16-18)

3  Pomaliza abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova* apitirize kufalikira mofulumira+ komanso kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu.  Muzitipemphereranso kuti tipulumutsidwe kwa anthu oipa kwambiri,+ chifukwa si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro.+  Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipayo.  Komanso monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro mwa inu kuti mukutsatira malangizo amene tinakupatsani ndipo mupitiriza kuwatsatira.  Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda Mulungu+ komanso kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.  Tsopano abale tikukupatsani malangizo mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti muzipewa mʼbale aliyense amene akuyenda mosalongosoka+ komanso amene akuchita zinthu zosagwirizana ndi malangizo amene* tinakupatsani.*+  Ndipotu inuyo mukudziwa zimene mukuyenera kuchita potitsanzira,+ chifukwa sitinachite zinthu zosalongosoka pakati panu,  kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.*+ Mʼmalomwake, tinagwira ntchito mwakhama komanso ndi mphamvu zathu zonse usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+  Sikuti tinachita zimenezi chifukwa choti tilibe ulamuliro wokupemphani kuti mutithandize,+ koma tinkafuna kuti tikupatseni chitsanzo choti muzitsanzira.+ 10  Ndipotu pamene tinali ndi inu, tinkakupatsani lamulo lakuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11  Chifukwa tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka pakati panu,+ sakugwira ntchito nʼkomwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12  Anthu otero tikuwalamula ndi kuwachonderera mwa Ambuye Yesu Khristu kuti azigwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena ndipo azidya chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+ 13  Koma inuyo abale, musasiye kuchita zabwino. 14  Koma ngati wina sakumvera mawu athu amene ali mʼkalatayi, muikeni chizindikiro ndipo musiye kuchitira naye zinthu limodzi+ kuti achite manyazi. 15  Komabe musamuone ngati mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga mʼbale. 16  Tsopano Ambuye wamtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mʼnjira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu. 17  Landirani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa.+ Nthawi zonse ndimalemba chonchi mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembera. 18  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mwambo umene.”
Mabaibulo ena amati, “tinawapatsa.”
Kapena kuti, “osalipira.”