2 Mafumu 1:1-18

  • Eliya analosera za imfa ya Ahaziya (1-18)

1  Ahabu atamwalira, Amowabu+ anagalukira Isiraeli.  Pa nthawi imeneyi Ahaziya ali mʼnyumba yake ku Samariya, anagwa kuchokera pachipinda chapadenga kudzera pachibowo chotchinga ndipo anavulala. Ndiyeno anatuma anthu kuti: “Pitani kwa Baala-zebabu mulungu wa ku Ekironi,+ mukafunse ngati ndingachire.”+  Koma mngelo wa Yehova anauza Eliya*+ wa ku Tisibe kuti: “Pita ukakumane ndi anthu amene atumidwa ndi mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi ku Isiraeli kulibe Mulungu kuti mupite kukafunsa kwa Baala-zebabu mulungu wa ku Ekironi?+  Choncho Yehova wanena kuti: “Pabedi pamene wagonapo sudzukapo, chifukwa ndithu umwalira.”’” Eliya atanena mawu amenewa, anachoka.  Anthu aja atabwerera kwa Ahaziya, nthawi yomweyo iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwerera?”  Anthuwo anayankha kuti: “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe nʼkutiuza kuti, ‘Bwererani kwa mfumu imene yakutumani ndipo mukaiuze kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi ku Isiraeli kulibe Mulungu kuti utumize anthu kukafunsa kwa Baala-zebabu mulungu wa ku Ekironi? Choncho pabedi pamene wagonapo, sudzukapo, chifukwa ndithu umwalira.’”’”+  Mfumuyo itamva zimenezi inawafunsa kuti: “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo nʼkukuuzani zimenezi amaoneka bwanji?”  Anthuwo anayankha kuti: “Munthuyo anavala chovala chaubweya+ ndi lamba wachikopa mʼchiuno mwake.”+ Mfumuyo itangomva zimenezi, inanena kuti: “Ndi Eliya wa ku Tisibe ameneyo.”  Ndiyeno mfumuyo inatumiza kwa Eliya mtsogoleri wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50. Mtsogoleriyo atafika, anapeza Eliya atakhala pamwamba pa phiri ndipo anamuuza kuti: “Munthu wa Mulungu woona iwe!+ Mfumu ikuti, ‘Utsike pamenepo!’” 10  Koma Eliya anayankha mtsogoleri wa asilikali 50 uja kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu, moto uchokere kumwamba+ ndipo upsereze iweyo ndi asilikali ako 50.” Moto unabweradi kuchokera kumwamba nʼkupsereza mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50. 11  Kenako mfumuyo inatumizanso mtsogoleri wina wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50. Mtsogoleriyo anauza Eliya kuti: “Munthu wa Mulungu woona iwe! Mfumu ikuti, ‘Utsike pamenepo msanga!’” 12  Koma Eliya anawayankha kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu woona, moto uchokere kumwamba ndipo upsereze iweyo ndi asilikali ako 50.” Moto wa Mulungu unabweradi kuchokera kumwamba nʼkupsereza mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50. 13  Ndiyeno mfumuyo inatumizanso mtsogoleri wachitatu wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50. Koma mtsogoleri ameneyo atafika, anagwada nʼkuyamba kuchonderera Eliya kuti awachitire chifundo. Iye anati: “Inu munthu wa Mulungu woona, chonde muone moyo wanga ndiponso wa atumiki anu 50 awa kukhala wamtengo wapatali. 14  Paja moto wochokera kumwamba wapsereza kale atsogoleri awiri ndi magulu awo a asilikali 50. Koma chonde muone moyo wanga kukhala wamtengo wapatali.” 15  Zitatero mngelo wa Yehova anauza Eliya kuti: “Tsika upite naye limodzi, usamuope.” Choncho Eliya ananyamuka nʼkupita ndi mtsogoleriyo kwa mfumu. 16  Atafika, Eliya anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Iweyo unatumiza anthu kuti akafunse kwa Baala-zebabu mulungu wa ku Ekironi.+ Kodi unachita zimenezi chifukwa choti ku Isiraeli kulibe Mulungu?+ Nʼchifukwa chiyani sunafunse kuti umve mawu ake? Ndiyetu sudzuka pabedi wagonapo, chifukwa ndithu umwalira.’” 17  Ahaziya anamwaliradi mogwirizana ndi mawu a Yehova amene Eliya ananena. Ndipo chifukwa choti analibe mwana wamwamuna, Yehoramu*+ anakhala mfumu mʼmalo mwake. Iye anayamba kulamulira mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda. 18  Zinthu zina zokhudza Ahaziya+ komanso zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “Mulungu Wanga Ndi Yehova.”
Ameneyu anali mchimwene wake wa Ahaziya.