2 Mafumu 11:1-21

  • Ataliya analanda ufumu (1-3)

  • Yehoasi anavekedwa ufumu mobisa (4-12)

  • Ataliya anaphedwa (13-16)

  • Yehoyada anasintha zinthu (17-21)

11  Ataliya,+ mayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa,+ anapha anthu onse amene anali oyenera kulowa ufumu.*+  Koma Yehoseba mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mchemwali wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pagulu la ana aamuna a mfumu amene ankayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi ndi mayi amene ankamusamalira nʼkukawaika mʼchipinda chamkati chogona. Anakwanitsa kubisa mwanayo kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.  Anakhalabe ndi mayi womusamalirayo mʼnyumba ya Yehova mmene anamubisa kwa zaka 6, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.  Mʼchaka cha 7, Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 olondera mfumu a Chikariya ndiponso atsogoleri a magulu a asilikali 100 a asilikali olondera nyumba yachifumu+ ndipo anabwera kudzakumana naye kunyumba ya Yehova. Iye anachita nawo pangano nʼkuwalumbiritsa kunyumba ya Yehovayo ndipo kenako anawaonetsa mwana wa mfumu uja.+  Ndiyeno anawalamula kuti: “Muchite izi: Mukhale mʼmagulu atatu ofanana ndipo gulu limodzi lidzabwere pa tsiku la Sabata kudzalondera nyumba yachifumu mosamala.+  Gulu lina lidzakhale pageti lotchedwa Maziko ndipo gulu lachitatu lidzakhale pageti kumbuyo kwa asilikali olondera nyumba yachifumu. Muzidzasinthana kulondera nyumbayo.  Magulu awiri amene anayenera kupuma pa Sabata asadzachoke. Onsewa adzalondere mosamala nyumba ya Yehova poteteza mfumu.  Mudzazungulire mfumuyo kumbali zonse mutatenga zida ndipo aliyense wofuna kudutsa pakati panu, adzaphedwe. Muzidzateteza mfumuyo kulikonse kumene ingapite.”  Atsogoleri a magulu a asilikali 100+ anachitadi zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga asilikali ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene ankafunika kupuma pa Sabata, nʼkupita kwa wansembe Yehoyada.+ 10  Wansembeyo anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja mikondo ndi zishango zozungulira zimene zinali za Mfumu Davide, zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova. 11  Asilikali olondera nyumba yachifumu+ anaima pamalo awo, aliyense atanyamula zida zake, kuyambira kumanja kwa nyumbayo mpaka kumanzere kwa nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe+ ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse. 12  Kenako Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumu+ uja nʼkumuveka chipewa chachifumu nʼkuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Choncho anamuveka ufumu nʼkumudzoza. Ndiyeno anayamba kuwomba mʼmanja nʼkumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+ 13  Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga, nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova.+ 14  Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala mogwirizana ndi mwambo wawo.+ Atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ anali ndi mfumuyo ndipo anthu onse amʼdzikolo ankasangalala komanso ankaimba malipenga. Ataliya ataona zimenezi anangʼamba zovala zake nʼkuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!” 15  Koma wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ omwe anasankhidwa kuti aziyangʼanira asilikali, ndipo anawauza kuti: “Mʼchotseni pakati pa asilikali ndipo aliyense amene angamutsatire aphedwe ndi lupanga!” Wansembeyo anali atanena kuti: “Musamuphere mʼnyumba ya Yehova.” 16  Choncho anamugwira ndipo atafika naye pakhomo la kunyumba ya mfumu+ lolowera mahatchi, anamuphera pomwepo. 17  Ndiyeno Yehoyada anachita pangano pakati pa Yehova, mfumu ndi anthu,+ kuti iwo apitiriza kukhala anthu a Yehova. Anachitanso pangano pakati pa mfumu ndi anthuwo.+ 18  Kenako anthu onse amʼdzikolo anapita kukachisi wa Baala nʼkukagwetsa maguwa ake ansembe,+ kuphwanyaphwanya mafano ake+ komanso anapha wansembe wa Baala+ dzina lake Mateni kutsogolo kwa maguwa ansembewo. Ndiyeno wansembe Yehoyada anasankha anthu kuti aziyangʼanira nyumba ya Yehova.+ 19  Atatero anauza atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ asilikali olondera mfumu a Chikariya, asilikali olondera nyumba yachifumu+ ndi anthu onse amʼdzikolo, kuti aperekeze mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anafika kunyumba ya mfumu kudzera pageti la asilikali olondera kunyumba yachifumu. Kenako mfumuyo inakhala pampando wachifumu wa mafumu.+ 20  Choncho anthu onse amʼdzikolo anasangalala ndipo mumzindawo munali bata chifukwa Ataliya anali ataphedwa ndi lupanga panyumba ya mfumu. 21  Yehoasi+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 7.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zonse za ufumu.”