2 Mafumu 12:1-21

  • Yehoasi mfumu ya Yuda (1-3)

  • Yehoasi anakonza kachisi (4-16)

  • Asiriya anaukira (17, 18)

  • Yehoasi anaphedwa (19-21)

12  Yehoasi+ anakhala mfumu mʼchaka cha 7 cha Yehu+ ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 40. Mayi ake anali a ku Beere-seba+ ndipo dzina lawo linali Zibiya.  Yehoasi anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova pa nthawi yonse imene wansembe Yehoyada ankamulangiza.  Koma sanachotse malo okwezeka+ ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi komanso nsembe zina mʼmalo okwezekawo.  Yehoasi anauza ansembe kuti: “Mutenge ndalama zonse zimene anthu akubweretsa kunyumba ya Yehova za zopereka zopatulika,+ zomwe ndi ndalama za msonkho zimene munthu aliyense akupereka,+ ndalama zoperekedwa ndi anthu amene analonjeza ndiponso ndalama zonse zimene munthu aliyense watsimikiza mumtima mwake kuti abweretse kunyumba ya Yehova.+  Wansembe aliyense azitenga ndalama zimenezi kwa anthu omwe apereka nʼkuzigwiritsa ntchito kukonza paliponse pamene nyumbayi yawonongeka.”*+  Koma pofika mʼchaka cha 23 cha Mfumu Yehoasi, ansembe anali asanakonzebe nyumbayo.+  Choncho Mfumu Yehoasi anaitana wansembe Yehoyada+ ndi ansembe ena nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani simukukonza nyumbayi? Ndiye musatengenso ndalama zina kwa anthu omwe apereka, pokhapokha ngati mungazigwiritse ntchito pokonza nyumbayi.”+  Ansembewo anavomereza kuti satenganso ndalama kwa anthu ndipo sakonza nyumbayo.  Kenako wansembe Yehoyada anatenga bokosi+ nʼkuboola kachibowo pachivundikiro chake. Kenako anaika bokosilo pambali pa guwa lansembe mbali yakumanja, munthu akamalowa mʼnyumba ya Yehova. Ansembe omwe ankalondera pakhomo ankaika mʼbokosilo ndalama zonse zimene anthu ankabweretsa kunyumba ya Yehova.+ 10  Akaona kuti mʼbokosilo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera nʼkuwerenga komanso kuika* mʼtimatumba ndalama zimene zinkaperekedwa panyumba ya Yehova.+ 11  Iwo ankapereka ndalama zimene awerengazo kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumba ya Yehova. Anthuwo ankagwiritsa ntchito ndalamazo polipira akalipentala, anthu omwe ankagwira ntchito yomanga panyumba ya Yehovayo,+ 12  amisiri omanga ndi miyala ndi anthu osema miyala. Ndalamazo anaguliranso matabwa ndi miyala yosema yokonzera nyumba ya Yehova ndiponso analipirira zonse zimene anagwiritsa ntchito pokonza nyumbayo. 13  Koma ndalama zimene anthu ankabweretsa kunyumba ya Yehova sanazigwiritse ntchito popanga mabeseni asiliva, zozimitsira nyale, mbale zolowa, malipenga+ ndiponso ziwiya zilizonse zagolide kapena zasiliva za mʼnyumba ya Yehova.+ 14  Ankapereka ndalamazo kwa anthu ogwira ntchito okha ndipo zinagwira ntchito pokonza nyumba ya Yehova. 15  Anthu amene ankapatsidwa ndalama kuti azilipira anthu ogwira ntchito, sankafunsidwa mmene ayendetsera ndalamazo chifukwa anali okhulupirika.+ 16  Koma ndalama za nsembe zakupalamula+ ndi za nsembe zamachimo sankazipereka kuti zigwire ntchito yokonzetsera nyumba ya Yehova chifukwa zinali za ansembe.+ 17  Pa nthawi imeneyo Hazaeli+ mfumu ya Siriya anapita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Gati+ nʼkuulanda. Kenako Hazaeli anaganiza zokaukira Yerusalemu.+ 18  Zitatero Yehoasi mfumu ya Yuda anatenga zopereka zonse zopatulika zimene makolo ake Yehosafati, Yehoramu ndi Ahaziya, mafumu a Yuda anaziyeretsa. Anatenganso zopereka za iyeyo zopatulika, ndi golide yense yemwe anali mosungira chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi cha mʼnyumba ya mfumu nʼkuzitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Choncho Hazaeli anabwerera osaukira Yerusalemu. 19  Nkhani zina zokhudza Yehoasi komanso zonse zimene anachita zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 20  Koma atumiki a Yehoasi anamʼkonzera chiwembu+ ndipo anamupha panyumba ya Chimulu cha Dothi*+ panjira yopita ku Sila. 21  Atumiki ake amene anamupha anali Yozakara mwana wa Simeyati ndi Yehozabadi mwana wa Someri.+ Zitatero anamuika mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ili ndi mingʼalu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanga.”
Kapena kuti, “Beti-milo.”