2 Mafumu 13:1-25

  • Yehoahazi mfumu ya Isiraeli (1-9)

  • Yehoasi mfumu ya Isiraeli (10-13)

  • Elisa anayesa khama la Yehoasi (14-19)

  • Elisa anamwalira; mafupa ake anaukitsa munthu (20, 21)

  • Ulosi womaliza wa Elisa unakwaniritsidwa (22-25)

13  Mʼchaka cha 23 cha Yehoasi+ mwana wa Ahaziya+ mfumu ya Yuda, Yehoahazi mwana wa Yehu+ anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya ndipo analamulira kwa zaka 17.  Yehoahazi anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ndipo sanasiye tchimo limene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ Iye anapitiriza kuchita tchimolo.  Choncho Yehova anakwiyira+ kwambiri Aisiraeli+ ndipo ankawapereka mʼmanja mwa Hazaeli+ mfumu ya Siriya ndi mʼmanja mwa Beni-hadadi+ mwana wa Hazaeli.  Patapita nthawi Yehoahazi anachonderera Yehova kuti awachitire chifundo ndipo Yehova anamumvera, chifukwa anaona kuti mfumu ya Siriya inkapondereza Aisiraeli.+  Choncho Yehova anapatsa Aisiraeli munthu amene anawapulumutsa+ mʼmanja mwa Siriya moti Aisiraeli anayamba kukhala mʼnyumba zawo ngati kale.*  (Koma sanasiye machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha anthu amʼnyumba ya Yerobowamu.+ Iwo anapitiriza kuchita machimowo ndipo mzati wopatulika*+ unalipobe ku Samariya.)  Yehoahazi anangotsala ndi asilikali 50 okwera pamahatchi, magaleta 10 ndi asilikali 10,000 oyenda pansi, chifukwa mfumu ya Siriya inawawononga+ ndi kuwapondaponda ngati fumbi la pa nthawi yopuntha mbewu.+  Nkhani zina zokhudza Yehoahazi, zonse zimene anachita ndiponso mphamvu zake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli.  Kenako Yehoahazi, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anamuika mʼmanda ku Samariya.+ Ndiyeno Yehoasi mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake. 10  Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 37 cha Yehoasi mfumu ya Yuda ndipo analamulira kwa zaka 16. 11  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Sanasiye kuchita machimo onse amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ Iye anapitiriza kuchita machimowo. 12  Nkhani zina zokhudza Yehoasi, zonse zimene anachita, mphamvu zake komanso mmene anamenyanirana ndi Amaziya mfumu ya Yuda,+ zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 13  Kenako Yehoasi, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo Yerobowamu*+ anakhala pampando wake wachifumu. Yehoasi anaikidwa ku Samariya mʼmanda a mafumu a Isiraeli.+ 14  Elisa+ atayamba kudwala matenda amene pamapeto pake anafa nawo, Yehoasi mfumu ya Isiraeli anapita kukamuona ndipo anayamba kulira kuti: “Bambo anga ine! Bambo anga ine! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera pamahatchi ake!”+ 15  Ndiyeno Elisa anauza Yehoasi kuti: “Tengani uta ndi mivi.” Choncho iye anatenga uta ndi miviyo. 16  Kenako iye anauza mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Gwirani utawo.” Mfumuyo inaugwiradi ndipo Elisa anaika manja ake pamanja a mfumuyo. 17  Kenako Elisa anati: “Tsegulani windo lakumʼmawa.” Iye analitsegula. Ndiyeno Elisa anati: “Ponyani muviwo!” Choncho iye anauponya. Zitatero Elisa anati: “Muvi wa Yehova wopulumutsa! Muvi wopulumutsa kwa Asiriya! Mudzapha* Asiriya ku Afeki+ mpaka kuwamaliza.” 18  Ananenanso kuti: “Tengani miviyo,” ndipo iye anaitengadi. Ndiyeno Elisa anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Menyani pansi ndi miviyo.” Mfumuyo inamenya katatu nʼkusiya. 19  Munthu wa Mulungu woonayo anakwiyira mfumuyo kwambiri, ndipo anati: “Munayenera kumenya maulendo 5 kapena 6! Mukanatero mukanaphadi Asiriya mpaka kuwamaliza, koma apa mudzawagonjetsa katatu kokha.”+ 20  Kenako Elisa anamwalira ndipo anamuika mʼmanda. Panali magulu a achifwamba a ku Mowabu+ amene ankabwera mʼdzikolo kumayambiriro kwa chaka chilichonse. 21  Tsiku lina anthu akuika maliro, anaona gulu la achifwamba. Nthawi yomweyo iwo anaponya mtembo wa munthuyo mʼmanda a Elisa nʼkuthawa. Mtembowo utakhudza mafupa a Elisa, munthuyo anauka+ ndipo anaimirira. 22  Hazaeli+ mfumu ya Siriya ankapondereza Aisiraeli+ masiku onse a Yehoahazi. 23  Komabe Yehova anakomera mtima Aisiraeli nʼkuwachitira chifundo+ ndipo anasonyeza kuti ankawadera nkhawa chifukwa cha pangano limene anachita ndi Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+ Iye sanafune kuwawononga ndipo sanawachotse pamaso pake mpaka lero. 24  Hazaeli mfumu ya Siriya atamwalira, mwana wake Beni-hadadi anakhala mfumu mʼmalo mwake. 25  Ndiyeno Yehoasi mwana wa Yehoahazi, analandanso kwa Beni-hadadi mwana wa Hazaeli, mizinda imene iye analanda Yehoahazi bambo ake pankhondo. Yehoasi anagonjetsa Beni-hadadi katatu+ ndipo analandanso mizinda ya Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti ankakhala mwabata ndiponso mwamtendere.
Ameneyu anali Yerobowamu Wachiwiri.
Kapena kuti, “Mudzagonjetsa.”