2 Mafumu 15:1-38

  • Azariya, mfumu ya Yuda (1-7)

  • Mafumu omaliza a Yuda: Zekariya (8-12), Salumu (13-16), Menahemu (17-22), Pekahiya (23-26), Peka (27-31)

  • Yotamu, mfumu ya Yuda (32-38)

15  Azariya*+ mwana wa Amaziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 27 cha Yerobowamu* mfumu ya Isiraeli.+  Azariya anakhala mfumu ali ndi zaka 16 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yekoliya.  Azariya ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Amaziya bambo ake.+  Komabe sanachotse malo okwezeka.+ Anthu ankaperekabe nsembe zautsi ndi nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+  Yehova anachititsa khate mfumuyo moti inali yakhate+ mpaka tsiku lomwe inamwalira. Inkakhala mʼnyumba kwayokha+ ndipo mwana wake Yotamu+ ndi amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu komanso kuweruza anthu amʼdzikolo.+  Nkhani zina zokhudza Azariya+ komanso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.  Kenako Azariya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake+ mu Mzinda wa Davide. Ndiyeno Yotamu mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.  Mʼchaka cha 38 cha Azariya+ mfumu ya Yuda, Zekariya+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya ndipo analamulira miyezi 6.  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira makolo ake. Sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ 10  Ndiyeno Salumu mwana wa Yabesi anakonzera chiwembu Zekariya nʼkumupha+ ku Ibuleamu+ ndipo iye anakhala mfumu mʼmalo mwake. 11  Nkhani zina zokhudza Zekariya, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 12  Izi zinakwaniritsa mawu amene Yehova anauza Yehu akuti: “Ana ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli+ mpaka mʼbadwo wa 4.”+ Ndipo zimenezi ndi zomwe zinachitikadi. 13  Salumu mwana wa Yabesi, anakhala mfumu mʼchaka cha 39 cha Uziya+ mfumu ya Yuda. Iye analamulira ku Samariya kwa mwezi umodzi. 14  Ndiyeno Menahemu mwana wa Gadai, anachoka ku Tiriza+ kupita ku Samariya nʼkukapha Salumu+ mwana wa Yabesi ku Samariyako. Kenako iye anakhala mfumu mʼmalo mwake. 15  Nkhani zina zokhudza Salumu komanso chiwembu chimene anakonza, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 16  Pa nthawi imeneyi mʼpamene Menahemu anachoka ku Tiriza nʼkupita kukaukira mzinda wa Tifisa. Iye anapha anthu onse amumzindawo ndiponso a mʼdera lozungulira chifukwa choti sanamutsegulire geti. Komanso anatumbula akazi onse oyembekezera. 17  Menahemu mwana wa Gadai anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 39 cha Azariya mfumu ya Yuda ndipo analamulira kwa zaka 10. 18  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Masiku ake onse, sanasiye kuchita machimo onse amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ 19  Puli+ mfumu ya Asuri anabwera mʼdzikomo ndipo Menahemu anamupatsa matalente* 1,000 a siliva chifukwa choti anamuthandiza kulimbitsa ufumu.+ 20  Menahemu anapeza ndalama zasilivazo kuchokera kwa Aisiraeli. Iye anasonkhetsa masekeli* 50 a siliva kwa mwamuna aliyense wachuma+ ndipo anawapereka kwa mfumu ya Asuri. Kenako mfumu ya Asuri inabwerera ndipo sinakhale mʼdzikomo. 21  Nkhani zina zokhudza Menahemu+ komanso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 22  Kenako Menahemu mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo mwana wake Pekahiya anakhala mfumu mʼmalo mwake. 23  Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 50 cha Azariya mfumu ya Yuda ndipo analamulira zaka ziwiri. 24  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ 25  Kenako Peka+ mwana wa Remaliya, yemwe anali msilikali wake womʼthandiza pagaleta, anamʼkonzera chiwembu nʼkumupha ku Samariya. Iye anapha mfumuyo ali limodzi ndi Arigobi, Ariye ndiponso amuna 50 a ku Giliyadi. Anaiphera munsanja ya panyumba ya mfumu, nʼkuyamba kulamulira mʼmalo mwake. 26  Nkhani zina zokhudza Pekahiya ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 27  Peka+ mwana wa Remaliya anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda ndipo analamulira kwa zaka 20. 28  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Sanasiye kuchita machimo amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ 29  Mʼmasiku a Peka mfumu ya Isiraeli, Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri anabwera nʼkulanda Iyoni, Abele-beti-maaka,+ Yanoa, Kedesi,+ Hazori, Giliyadi+ ndi Galileya, dera lonse la Nafitali.+ Anatenga anthu akumeneku nʼkupita nawo ku Asuri.+ 30  Kenako Hoshiya+ mwana wa Ela anakonzera chiwembu Peka mwana wa Remaliya nʼkumupha. Atatero anakhala mfumu mʼmalo mwake mʼchaka cha 20 cha Yotamu+ mwana wa Uziya. 31  Nkhani zina zokhudza Peka ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 32  Mʼchaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, Yotamu+ mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 33  Yotamu anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 34  Iye ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira bambo ake Uziya.+ 35  Komabe sanachotse malo okwezeka ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi komanso nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+ Iye ndi amene anamanga geti lakumtunda la nyumba ya Yehova.+ 36  Nkhani zina zokhudza Yotamu ndiponso zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 37  Pa nthawi imeneyo Yehova anayamba kutumiza Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya kuti akalimbane ndi Yuda.+ 38  Kenako Yotamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira, ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake. Ndiyeno mwana wake Ahazi anakhala mfumu mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Yehova Wathandiza.” Amatchedwanso Uziya pa 2Mf 15:13; 2Mb 26:1-23; Yes 6:1 ndi Zek 14:5.
Uyu ndi Yerobowamu Wachiwiri.
Talenti imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.