2 Mafumu 2:1-25

  • Eliya anatengedwa ndi mphepo yamkuntho (1-18)

    • Elisa anatenga chovala chauneneri cha Eliya (13, 14)

  • Elisa anachititsa kuti madzi a ku Yeriko akhale abwino (19-22)

  • Zimbalangondo zinapha anyamata a ku Beteli (23-25)

2  Yehova atatsala pangʼono kutenga Eliya+ mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,*+ Eliya ndi Elisa+ ananyamuka ku Giligala.+  Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo utsale kuno, chifukwa Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anapita ku Beteli.+  Ndiyeno ana a aneneri* amene anali ku Beteli anabwera kwa Elisa nʼkumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?”+ Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa zimenezo. Khalani chete.”  Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Elisa, utsale kuno chifukwa Yehova wandituma ku Yeriko.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anafika ku Yeriko.  Kenako ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa nʼkumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?” Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa zimenezo. Khalani chete.”  Ndiyeno Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo utsale kuno, chifukwa Yehova wandituma ku Yorodano.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anapitiriza ulendo wawo.  Ndiyeno ana a aneneri okwana 50 anaima chapatali nʼkumawayangʼana. Koma Eliya ndi Elisa anaima pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.  Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ ndipo anachipinda nʼkumenya madzi a mumtsinjewo. Madziwo anagawanika uku ndi uku moti iwo anawoloka pouma.+  Iwo atangowoloka, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanatengedwe nʼkukusiya.” Elisa anati: “Chonde, ndilandire magawo awiri+ a mzimu wanu.”+ 10  Eliya anati: “Wapempha chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.” 11  Pamene ankayenda, uku akulankhulana, anangoona galeta* lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto.+ Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo nʼkuwalekanitsa ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho nʼkupita kumwamba.*+ 12  Elisa ankaona zonse zimene zinkachitikazo ndipo ankafuula kuti: “Bambo anga ine! Bambo anga ine! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Elisa ataona kuti Eliya wapita, anagwira zovala zake nʼkuzingʼamba pakati.+ 13  Atatero anatola chovala chauneneri+ cha Eliya chimene chinagwa pansi ndipo anabwerera nʼkukaima mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano. 14  Kenako anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija nʼkumenya madzi amumtsinjewo ndipo anati: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Atatero madziwo anagawanika ndipo Elisa anawoloka.+ 15  Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu umene unali ndi Eliya uli ndi Elisa.”+ Choncho anapita kukakumana naye ndipo anamugwadira mpaka nkhope zawo kufika pansi. 16  Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu. Bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu* wa Yehova wamunyamula ndipo wamʼponya paphiri linalake kapena mʼchigwa.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatume.” 17  Koma iwo anamʼkakamiza mpaka iye anachita manyazi, moti anati: “Atumeni.” Choncho anatuma amuna 50 ndipo anamufufuza kwa masiku atatu koma sanamʼpeze. 18  Anthuwo atabwerera kwa Elisa ku Yeriko,+ Elisa ananena kuti: “Pajatu ndinakuuzani kuti musapite.” 19  Patapita nthawi, anthu amumzindawo anauza Elisa kuti: “Inu mbuyathu mukudziwa kuti mzindawu uli pamalo abwino,+ koma madzi ake ndi oipa ndipo nthaka ndi yosabereka.”* 20  Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni kambale katsopano kolowa ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anamʼbweretseradi. 21  Ndiyeno Elisa anapita pamene panayambira madziwo nʼkuponyapo mchere uja+ nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndakonza madziwa kuti akhale abwino ndipo sadzachititsanso imfa kapena kusabereka.’”* 22  Madziwo ndi abwino mpaka lero mogwirizana ndi zimene Elisa ananena. 23  Kenako Elisa ananyamuka nʼkumapita ku Beteli. Ali mʼnjira, anyamata ena a mumzindawo anayamba kumunyoza+ kuti: “Choka kuno wadazi iwe! Choka kuno wadazi iwe!” 24  Kenako Elisa anatembenuka nʼkuwayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Ndiyeno zimbalangondo+ ziwiri zazikazi zinatuluka patchire nʼkukhadzula anyamata 42.+ 25  Elisa anapitiriza ulendo wake ndipo anakafika kuphiri la Karimeli.+ Atachoka kumeneko anabwerera ku Samariya.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mumlengalenga.”
Mawu akuti “ana a aneneri” mwina akutanthauza sukulu yopereka malangizo kwa aneneri, kapena kagulu ka aneneri.
Ena amati “mahosi.”
Kapena kuti, “mumlengalenga.”
Kapena kuti, “mphepo.”
Mabaibulo ena amati, “nthaka ikuchititsa kuti akazi azipita padera.”
Mabaibulo ena amati, “kupita padera.”