2 Mafumu 20:1-21

  • Hezekiya anadwala nʼkuchira (1-11)

  • Anthu anatumidwa kuchokera ku Babulo (12-19)

  • Imfa ya Hezekiya (20, 21)

20  Mʼmasiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pangʼono kufa.+ Ndiyeno mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita, chifukwa iweyo ufa ndithu, suchira.’”+  Hezekiya atamva zimenezi, anatembenukira kukhoma nʼkuyamba kupemphera kwa Yehova kuti:  “Yehova, chonde ndikukupemphani kuti mukumbukire kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse komanso ndachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.  Pamene Yesaya ankabwerera, asanafike nʼkomwe pabwalo lapakati, Yehova anamuuza kuti:+  “Bwerera, ukauze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva pemphero lako ndipo ndaona misozi yako.+ Ndikuchiritsa.+ Pa tsiku lachitatu udzapita kunyumba ya Yehova.+  Ndiwonjezera zaka 15 pa moyo* wako ndipo ndidzapulumutsa iweyo ndi mzindawu mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.+ Ndidzateteza mzindawu chifukwa cha ineyo ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+  Kenako Yesaya anati: “Bweretsani keke ya nkhuyu zouma.” Choncho iwo anabweretsadi nʼkuiika pachotupa* chimene Hezekiya anali nacho ndipo anayamba kuchira.+  Hezekiya anali atafunsa Yesaya kuti: “Kodi chizindikiro+ chakuti Yehova andichiritsa ndipo ndidzapitadi kunyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu nʼchiyani?”  Yesaya anayankha kuti: “Chizindikiro chochokera kwa Yehova chosonyeza kuti Yehova adzakwaniritsadi mawu ake, ndi ichi: Kodi ukufuna kuti mthunzi uyende masitepe* 10 kupita kutsogolo, kapena uyende masitepe 10 kubwerera mʼmbuyo?”+ 10  Hezekiya anayankha kuti: “Nʼzosavuta kuti mthunzi upite kutsogolo masitepe 10, koma nʼzovuta kuti ubwerere mʼmbuyo masitepe 10.” 11  Choncho mneneri Yesaya anafuulira Yehova ndipo iye anachititsa mthunzi umene unali utapita kale kutsogolo kuti ubwerere mʼmbuyo pamasitepe a Ahazi. Mthunziwo unabwerera mʼmbuyo masitepe 10.+ 12  Pa nthawi imeneyo, Berodaki-baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babulo, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya chifukwa anamva kuti Hezekiya anadwala.+ 13  Hezekiya analandira anthuwo ndipo anawaonetsa nyumba yake yonse yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu, mafuta ena amtengo wapatali, nyumba yake yosungiramo zida zankhondo ndiponso chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse mʼnyumba yake* ndi mu ufumu wake wonse. 14  Kenako mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya nʼkuifunsa kuti: “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, nanga anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+ 15  Atatero Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani mʼnyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili mʼnyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.” 16  Ndiyeno Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imva zimene Yehova wanena,+ 17  ‘Masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili mʼnyumba mwako ndiponso zonse zimene makolo ako akhala akusunga mpaka lero, anthu adzazitenga nʼkupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,’ watero Yehova. 18  ‘Ena mwa ana ako, amene iweyo udzabereke, adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna zapanyumba ya mfumu ya ku Babulo.’”+ 19  Hezekiya atamva zimenezi anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwanenawa ndi abwino.”+ Anapitiriza kuti: “Ngati mʼmasiku anga mukhale bata ndi mtendere, ndiye kuti zili bwino.”+ 20  Nkhani zina zokhudza Hezekiya, mphamvu zake ndiponso mmene anakumbira dziwe+ ndi ngalande nʼkubweretsa madzi mumzindawo,+ zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 21  Kenako Hezekiya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ ndipo mwana wake Manase+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku.”
Kapena kuti, “pachithupsa.”
Nʼkutheka kuti masitepe amenewa ankawagwiritsa ntchito ngati chipangizo chodziwira nthawi.
Kapena kuti, “mʼnyumba yachifumu.”