2 Mafumu 21:1-26

  • Manase, mfumu ya Yuda; anapha anthu (1-18)

    • Yerusalemu adzawonongedwa (12-15)

  • Amoni, mfumu ya Yuda (19-26)

21  Manase+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 12 ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali Hefiziba.  Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo ankatsatira zinthu zonyansa zomwe ankachita anthu a mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli.+  Iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Komanso anamanga maguwa ansembe a Baala ndi mzati wopatulika,*+ ngati mmene Ahabu mfumu ya Isiraeli anachitira.+ Manase ankalambira ndiponso kutumikira gulu lonse la zinthu zakuthambo.+  Anamanganso maguwa ansembe mʼnyumba ya Yehova,+ imene Yehova ananena kuti: “Ku Yerusalemu ndidzaikako dzina langa.”+  Iye anamanga maguwa ansembe a gulu lonse la zinthu zakumwamba+ mʼmabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+  Manase anatentha* mwana wake wamwamuna pamoto, ankachita zamatsenga, ankawombeza+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu komanso olosera zamʼtsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.  Komanso iye anaika mʼnyumbayo chifaniziro cha mzati wopatulika+ chimene anapanga. Koma ponena za nyumbayo, Yehova anauza Davide ndi mwana wake Solomo kuti: “Mʼnyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+  Sindidzachititsanso mapazi a Aisiraeli kuchoka mʼdziko limene ndinapatsa makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ mogwirizana ndi Chilamulo chonse chimene Mose mtumiki wanga anawauza kuti azitsatira.”  Koma sanamvere ndipo Manase anapitiriza kusocheretsa anthu ndiponso kuwachititsa zinthu zoipa kuposa zimene mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa Aisiraeli inkachita.+ 10  Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri,+ kuti: 11  “Manase mfumu ya Yuda wachita zinthu zonyansa zonsezi. Wachita zinthu zoipa kwambiri kuposa zonse zimene anachita Aamori+ amene analiko iye asanakhale mfumu.+ Iye wachititsa Yuda kuchimwa ndi mafano ake onyansa.* 12  Choncho Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndibweretsera tsoka Yerusalemu+ ndi Yuda loti aliyense akamva, mʼmakutu ake onse mudzalira.+ 13  Ndidzayeza Yerusalemu ndi chingwe chimene ndinayezera+ Samariya+ ndiponso ndidzamuyeza ndi levulo imene ndinayezera nyumba ya Ahabu.+ Yerusalemu ndidzamʼpukuta mpaka kuyera ngati mmene munthu amapukutira mbale yolowa mpaka kuyera, nʼkuitembenuza.+ 14  Anthu otsala pa cholowa changa+ ndidzawasiya ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Iwo pamodzi ndi katundu wawo adzatengedwa ndi adani awo onse.+ 15  Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti iwo anachita zoipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuyambira tsiku limene makolo awo anatuluka ku Iguputo mpaka lero.’”+ 16  Manase anaphanso anthu ambiri osalakwa mpaka magazi awo anadzaza Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto,+ kuwonjezera pa tchimo lake lochititsa kuti Ayuda achimwe pochita zoipa pamaso pa Yehova. 17  Nkhani zina zokhudza Manase, zonse zimene anachita ndiponso machimo ake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 18  Kenako Manase, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mʼmunda wapanyumba pake, mʼmunda wa Uziza.+ Ndiyeno mwana wake Amoni anakhala mfumu mʼmalo mwake. 19  Amoni+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yotiba ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi. 20  Amoni ankachita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Manase bambo ake.+ 21  Iye ankayenda mʼnjira zonse zimene bambo ake anayendamo ndipo anapitiriza kutumikira mafano onyansa amene bambo ake ankawatumikira komanso kuwagwadira.+ 22  Choncho anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.+ 23  Patapita nthawi, atumiki a Mfumu Amoni anamukonzera chiwembu nʼkumupha mʼnyumba mwake momwe. 24  Koma anthu a mʼdzikolo anapha anthu onse amene anakonzera chiwembu Mfumu Amoni. Kenako anthu amʼdzikolo anaika mwana wake Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwake.+ 25  Nkhani zina zokhudza Amoni ndiponso zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 26  Choncho anamuika mʼmanda ake mʼmunda wa Uziza+ ndipo mwana wake Yosiya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anadutsitsa.”
Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.