2 Mafumu 22:1-20

  • Yosiya, mfumu ya Yuda (1, 2)

  • Malangizo okhudza kukonza kachisi (3-7)

  • Anapeza buku la Chilamulo (8-13)

  • Hulida analosera tsoka (14-20)

22  Yosiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 8 ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Bozikati.+ Dzina lawo linali Yedida mwana wa Adaya.  Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake.+ Iye sanapatukire kumanja kapena kumanzere.  Mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, mfumuyo inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu yemwe anali mlembi, kuti apite kunyumba ya Yehova.+ Inamuuza kuti:  “Pita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti asonkhanitse ndalama zonse zimene zikubwera kunyumba ya Yehova,+ zimene alonda a pakhomo atolera kwa anthu.+  Azipereke kwa omwe asankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova, kuti akazipereke kwa amene akugwira ntchitoyo mʼnyumba ya Yehova, kuti akonze* nyumbayo.+  Akazipereke kwa amisiri, kwa omanga nyumba ndiponso kwa amisiri omanga ndi miyala. Agulirenso matabwa ndi miyala yosema kuti akonzere nyumbayo.+  Koma anthu amene akupatsidwa ndalamazo asafunsidwe mmene akuziyendetsera chifukwa ndi anthu odalirika.”+  Kenako Hilikiya mkulu wa ansembe anauza Safani mlembi+ kuti: “Ndapeza buku la Chilamulo+ mʼnyumba ya Yehova!” Choncho Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani ndipo iye anayamba kuliwerenga.+  Ndiyeno Safani mlembi anapita kwa mfumu kukanena kuti: “Atumiki anu akhuthula ndalama zimene anazipeza mʼnyumbayo ndipo azipereka kwa omwe anasankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova.”+ 10  Safani mlembi anauzanso mfumuyo kuti: “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku+ linalake.” Ndiyeno Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo. 11  Mfumuyo itangomva mawu a mʼbuku la Chilamulo, inangʼamba zovala zake.+ 12  Kenako mfumuyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti: 13  “Pitani mukafunse kwa Yehova mʼmalo mwa ineyo, anthuwa ndiponso mʼmalo mwa Ayuda onse. Mukafunse zokhudza mawu a mʼbuku limene lapezekali, chifukwa Yehova watikwiyira kwambiri,+ popeza makolo athu sanamvere mawu a mʼbukuli. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.” 14  Choncho wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya anapita kwa Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe ankayangʼanira mosungira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi. Hulidayo ankakhala Kumbali Yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+ 15  Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Munthu amene wakutumaniyo mukamuuze kuti: 16  “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake pokwaniritsa mawu onse amʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga.+ 17  Chifukwa chakuti andisiya nʼkumapereka nsembe zautsi kwa milungu+ ina kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo,+ mkwiyo wanga udzayakira malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’”+ 18  Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: ‘Ponena za mawu amene wamvawo, 19  chifukwa chakuti mtima wako unali womvera* ndipo unadzichepetsa+ pamaso pa Yehova utamva zimene ndanena zokhudza malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chinthu chodabwitsa ndi temberero ndipo unangʼamba zovala zako+ nʼkuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva, watero Yehova. 20  Nʼchifukwa chake ndidzakuika mʼmanda a makolo ako ndipo udzaikidwa mʼmanda ako mwamtendere. Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndidzabweretse pamalo ano.’”’” Kenako iwo anakauza mfumuyo zimenezi.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amate mingʼalu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wofewa.”