2 Mafumu 24:1-20

  • Kugalukira kwa Yehoyakimu komanso imfa yake (1-7)

  • Yehoyakini, mfumu ya Yuda (8, 9)

  • Ayuda oyamba kupita ku Babulo (10-17)

  • Zedekiya, mfumu ya Yuda; anagalukira (18-20)

24  Mʼmasiku a Yehoyakimu, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera kudzamenyana naye. Ndipo Yehoyakimu anakhala mtumiki wake kwa zaka zitatu, koma kenako anamugalukira.  Yehova anayamba kumʼtumizira Yehoyakimu magulu a achifwamba a Akasidi,+ a Asiriya, a Amowabu ndi a Aamoni. Ankawatumiza ku Yuda kuti awononge dzikolo mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene ananena kudzera mwa atumiki ake, aneneri.  Zimenezi zinachitikira Ayuda molamulidwa ndi Yehova, kuti awachotse pamaso pake+ chifukwa cha machimo onse amene Manase anachita+  komanso chifukwa cha anthu ambiri osalakwa amene anawapha,+ moti anadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osalakwa ndipo Yehova sanafune kukhululuka.+  Nkhani zina zokhudza Yehoyakimu ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.+  Kenako Yehoyakimu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ ndipo mwana wake Yehoyakini anakhala mfumu mʼmalo mwake.  Mfumu ya Iguputo sinatulukenso mʼdziko lake, chifukwa mfumu ya Babulo inali itatenga zinthu zonse za mfumu ya Iguputo,+ kuyambira kuchigwa* cha Iguputo+ mpaka kumtsinje wa Firate.+  Yehoyakini+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 18 ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Nehusita mwana wa Elinatani.  Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene bambo ake anachita. 10  Pa nthawi imeneyo, atumiki a Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu nʼkuzungulira mzindawo.+ 11  Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo atumiki ake atauzungulira. 12  Yehoyakini mfumu ya Yuda anapita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake, atumiki ake, akalonga ake ndi nduna za panyumba yake+ ndipo mfumu ya Babuloyo inamutenga nʼkupita naye ku ukapolo mʼchaka cha 8 cha ufumu wake.+ 13  Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha mʼnyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapanga kuti zikhale za mʼkachisi wa Yehova.+ Zimenezi zinachitika mogwirizana ndi zimene Yehova analosera. 14  Mfumuyo inatenga anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ asilikali onse amphamvu, amisiri onse ndiponso anthu osula zitsulo*+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu osauka kwambiri a mʼdzikolo.+ 15  Choncho iye anatenga Yehoyakini+ nʼkupita naye ku Babulo.+ Ku Yerusalemu anatenganso mayi a mfumuyo, akazi ake, nduna za panyumba yake komanso akuluakulu a mʼdzikolo, nʼkupita nawo ku Babulo. 16  Mfumu ya Babulo inatenganso asilikali onse amphamvu okwana 7,000, amisiri okwana 1,000 komanso anthu osula zitsulo* ndipo onse anali amuna amphamvu komanso ophunzitsidwa kumenya nkhondo nʼkupita nawo ku Babulo. 17  Mfumu ya Babulo inatenga Mataniya, bambo ake aangʼono a Yehoyakini,+ nʼkuwaika kukhala mfumu mʼmalo mwake. Kenako inawasintha dzina kuti akhale Zedekiya.+ 18  Zedekiya anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 19  Zedekiya ankachita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+ 20  Zinthu zimenezi zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda chifukwa Yehova anakwiya kwambiri mpaka anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anagalukira mfumu ya Babulo.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “omanga makoma achitetezo.”
Mabaibulo ena amati, “omanga makoma achitetezo.”