2 Mafumu 25:1-30

  • Nebukadinezara anazungulira Yerusalemu (1-7)

  • Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa; Ayuda enanso anapita ku Babulo (8-21)

  • Gedaliya anaikidwa kuti azilamulira (22-24)

  • Gedaliya anaphedwa; anthu anathawira ku Iguputo (25, 26)

  • Yehoyakini anamasulidwa ku Babulo (27-30)

25  Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse.+ Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+  Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.  Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9, njala inafika poipa kwambiri+ mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+  Ndiyeno mpanda wa mzindawo unabooledwa+ ndipo asilikali onse anathawa usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo mfumu inayamba kuthawa kulowera cha ku Araba.+  Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo anaipeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha.  Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo ndipo anaipatsa chigamulo.  Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo.+  Mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 7 la mweziwo, chomwe chinali chaka cha 19 cha Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+  Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu,+ nyumba ya munthu aliyense wotchuka+ komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu.+ 10  Kenako asilikali onse a Akasidi, omwe anali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, anagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+ 11  Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthu amene anatsala mumzindamo, anthu amene anakhala kumbali ya mfumu ya Babulo ndiponso anthu ena onse, nʼkupita nawo ku ukapolo.+ 12  Ena mwa anthu osauka kwambiri amʼdzikolo, mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi alimi ogwira ntchito mokakamizidwa.+ 13  Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki ya kopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova, nʼkutenga kopa wake kupita naye ku Babulo.+ 14  Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, makapu ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi. 15  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga zopalira moto ndi mbale zolowa, zomwe zinali zagolide+ komanso zasiliva weniweni.+ 16  Koma sanathe kuyeza kulemera kwa kopa wa zipilala ziwiri zija, thanki yosungira madzi ndiponso zotengera zokhala ndi mawilo zimene Solomo anapanga kuti zizigwira ntchito panyumba ya Yehova.+ 17  Chipilala chilichonse chinali chachitali mikono 18*+ ndipo mutu wake unali wakopa. Mutuwo unali wautali mikono itatu ndipo maukonde ndi makangaza* amene anazungulira mutuwo, onse anali akopa.+ Chipilala chachiwiri ndi maukonde ake chinalinso chofanana ndi choyambacho. 18  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri ndi alonda atatu apakhomo.+ 19  Mumzindawo anatengamonso nduna imodzi yapanyumba ya mfumu imene inkayangʼanira asilikali. Anatenganso anzake 5 a mfumu amene anawapeza mumzindawo. Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe ankasonkhanitsa anthu ndiponso amuna 60 mwa anthu wamba amene anawapeza mumzindawo. 20  Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa nʼkupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo.+ 21  Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo ku Ribila mʼdziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anatengedwa kudziko lawo nʼkupita nawo ku ukapolo.+ 22  Ndiyeno Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anasankha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ mwana wa Safani,+ kuti akhale mtsogoleri wa anthu amene anawasiya ku Yuda.+ 23  Akuluakulu onse a asilikali limodzi ndi asilikali awo atamva kuti mfumu ya Babulo yasankha Gedaliya, nthawi yomweyo anapita kwa Gedaliyayo ku Mizipa. Akuluakuluwo anali Isimaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa ndiponso Yaazaniya wa ku Maaka, pamodzi ndi asilikali awo.+ 24  Gedaliya analumbirira akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kukhala atumiki a Akasidi. Khalani mʼdzikoli nʼkumatumikira mfumu ya Babulo ndipo zinthu zikuyenderani bwino.”+ 25  Mʼmwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, yemwe anali wa kubanja lachifumu* anapita kwa Gedaliya pamodzi ndi amuna 10. Iwo anapha Gedaliya ndi Ayuda ndiponso Akasidi amene anali naye ku Mizipa.+ 26  Zitatero, anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu komanso akuluakulu a magulu a asilikali, anathawira ku Iguputo,+ chifukwa ankaopa Akasidi.+ 27  Mʼchaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda,+ Evili-merodaki mfumu ya Babulo anakhala mfumu. Ndiyeno mʼchaka chomwechi mʼmwezi wa 12, pa tsiku la 27 la mweziwo, iye anatulutsa mʼndende Yehoyakini mfumu ya Yuda.+ 28  Ankalankhula naye mokoma mtima ndipo anakweza mpando wake wachifumu kuposa mipando ya mafumu ena amene anali naye ku Babulo. 29  Yehoyakini anavula zovala zake zakundende ndipo ankadya limodzi ndi mfumuyo masiku onse a moyo wake. 30  Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumuyo, kwa moyo wake wonse.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amkuwa.”
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya ufumu.”