2 Mafumu 4:1-44

  • Elisa anachulukitsa mafuta a mkazi wamasiye (1-7)

  • Mtima wochereza wa mayi wa ku Sunemu (8-16)

  • Mayi anakhala ndi mwana; mwanayo anamwalira (17-31)

  • Elisa anaukitsa mwana (32-37)

  • Elisa anachotsa poizoni mʼchakudya (38-41)

  • Elisa anachulukitsa mikate (42-44)

4  Mayi wina yemwe anali mmodzi wa akazi a ana a aneneri,+ anauza Elisa modandaula kuti: “Mtumiki wanu yemwe anali mwamuna wanga anamwalira ndipo inu mukudziwa bwino kuti ankaopa Yehova.+ Tsopano kwabwera wangongole kudzatenga ana anga onse awiri kuti akakhale akapolo ake.”  Elisa anamuyankha kuti: “Ndiye ndikuchitire chiyani? Tandiuze, uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti: “Ine kapolo wanu ndilibe chilichonse mʼnyumba mwanga, ndili ndi kamtsuko ka mafuta kokha basi.”+  Elisa anati: “Pita ukabwereke zotengera zopanda kanthu kwa anthu amene ukukhala nawo pafupi. Usakabwereke zochepa.  Ukakatero, iwe ndi ana akowo mukalowe mʼnyumba nʼkutseka chitseko. Ndiyeno uzikathira mafutawo mʼzotengerazo. Zimene zadzaza uzikaziika pambali.”  Atamuuza zimenezi, mayiyo ananyamuka. Iye ndi ana ake atadzitsekera mʼnyumba, anawo ankamuikira zotengera zija pafupi, iye nʼkumathiramo mafuta.+  Zotengera zija zitadzaza, mayiyo anauza mwana wake kuti: “Bweretsa china.”+ Koma mwanayo anayankha kuti: “Palibe chomwe chatsala.” Zitatero mafutawo analeka.+  Kenako anapita kwa munthu wa Mulungu woona uja kukamuuza zomwe zinachitikazo. Munthu wa Mulungu woonayo anati: “Pita ukagulitse mafutawo nʼkubweza ngongole zako ndipo ndalama zotsalazo zikuthandize iweyo ndi ana ako.”  Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu.+ Kumeneko kunali mayi wina wodziwika. Mayiyo anaumiriza Elisa kuti adye chakudya.+ Nthawi zonse Elisa akamadutsa, ankaima kunyumba kwa mayiyo kuti adye chakudya.  Kenako mayiyo anauza mwamuna wake kuti: “Ndikuona kuti munthu amene amadutsa kuno nthawi zonse uja, ndi munthu woyera wa Mulungu. 10  Tiyeni timʼmangire kachipinda kapadenga+ ndipo timuikiremo bedi, tebulo, mpando ndi choikapo nyale, kuti akabwera azikhala mmenemo.”+ 11  Tsiku lina Elisa anabwera ndipo analowa mʼkachipinda kapadengako kuti agone. 12  Ndiyeno Elisa anauza mtumiki wake Gehazi+ kuti: “Kandiitanire mayi uja.”+ Choncho iye anamuitana ndipo anaima pamaso pa Elisa. 13  Ndiyeno Elisa anauza Gehazi kuti: “Muuze kuti, ‘Mwavutika ndi kutisamalira,+ kodi tingakuchitireni chiyani?+ Kodi pali chinachake choti tikakunenereni kwa mfumu,+ kapena kwa mkulu wa asilikali?’” Koma mayiyo anayankha kuti: “Ayi, palibe. Ndikukhala mwamtendere ndi anthu a mtundu wanga.” 14  Elisa anati: “Ndiye timuchitire chiyani?” Gehazi anayankha kuti: “Mayiyutu alibe mwana wamwamuna+ ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.” 15  Nthawi yomweyo Elisa anati: “Muitane.” Choncho Gehazi anamuitana ndipo mayiyo anaima pakhomo. 16  Ndiyeno Elisa anati: “Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino mudzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Koma mayiyo atamva anati: “Ayi mbuyanga, munthu wa Mulungu woona! Musandinamize ine kapolo wanu.” 17  Komabe, mayiyo anakhala ndi pakati nthawi ngati yomweyo chaka chotsatira ndipo anabereka mwana wamwamuna mogwirizana ndi zimene Elisa anamuuza. 18  Mwanayo anakula ndipo tsiku lina anapita kwa bambo ake, omwe anali kumunda limodzi ndi antchito okolola. 19  Kumeneko mwanayo anayamba kulira kuti: “Mutu wanga ine! Mayo ine mutu wanga!” Kenako bambo akewo anauza wantchito wawo wina kuti: “Munyamule upite naye kwa mayi ake.” 20  Wantchitoyo ananyamuladi mwanayo nʼkupita naye kwa mayi ake. Mayi akewo anamunyamula pamwendo mpaka masana, kenako mwanayo anamwalira.+ 21  Ndiyeno mayiyo anatenga mwanayo nʼkukamugoneka pabedi la munthu wa Mulungu woona uja.+ Atatero anatuluka nʼkutseka chitseko. 22  Kenako anaitana mwamuna wake nʼkumuuza kuti: “Mundipatseko wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi. Ndikufuna ndipite mwamsanga kwa munthu wa Mulungu woona uja.” 23  Mwamuna wakeyo anamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukufuna kupitako lero? Lerotu si tsiku limene mwezi watsopano uoneke+ komanso si la sabata.” Koma mayiyo anayankha kuti: “Zonse zili bwino.” 24  Ndiyeno mayiyo atakwera bulu, anauza wantchito wake kuti: “Buluyu uzimuthamangitsa, usayende pangʼonopangʼono chifukwa cha ine, pokhapokha ndikakuuza.” 25  Choncho mayiyo anapita kwa munthu wa Mulungu woona uja kuphiri la Karimeli. Munthu wa Mulunguyo atangoona mayiyo, anauza mtumiki wake Gehazi kuti: “Mayi wa ku Sunemu uja uyo! Akubwera. 26  Thamanga ukakumane naye. Ukamufunse kuti: ‘Kodi muli bwino? Mwamuna wanu ali bwanji? Nanga mwana wanu ali bwanji?’” Mayiyo anayankha kuti: “Onse ali bwino.” 27  Mayiyo atafika kwa munthu wa Mulungu woona paphiripo, nthawi yomweyo anamʼgwira mapazi.+ Gehazi ataona zimenezo, anabwera pafupi kuti amukankhe mayiyo. Koma munthu wa Mulungu woonayo anamuuza kuti: “Musiye, mtima wake ukumʼpweteka kwambiri. Koma Yehova wandibisira, sanandiuze.” 28  Kenako mayiyo anati: “Kodi ndinakupemphani mwana mbuyanga? Kodi ine sindinanene kuti, ‘Musandipatse chiyembekezo chabodzaʼ?”+ 29  Nthawi yomweyo Elisa anauza Gehazi kuti: “Manga zovala zako mʼchiuno.+ Tenga ndodo yangayi uzipita. Ukakumana ndi munthu aliyense panjira usamʼpatse moni ndipo munthu akakupatsa moni, usamuyankhe. Ukaike ndodo yangayi pankhope ya mnyamatayo.” 30  Koma mayi wa mwanayo anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.”+ Choncho Elisa ananyamuka nʼkupita limodzi ndi mayiyo. 31  Gehazi anatsogola ndipo anakaika ndodo ija pankhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena chizindikiro chosonyeza kuti ali moyo.+ Choncho iye anabwerera nʼkukauza Elisa kuti: “Mwana uja sanadzuke.” 32  Elisa atalowa mʼnyumbamo, anapeza mwana wakufayo atamʼgoneka pabedi lake lija.+ 33  Ndiyeno analowa kuchipinda nʼkutseka chitseko ndipo analiko awiriwiri. Atatero anayamba kupemphera kwa Yehova.+ 34  Kenako anapita pabedipo ndipo anagwada nʼkuweramira mwanayo. Anagunditsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake ndi maso a mwanayo komanso manja ake ndi manja a mwanayo. Anakhalabe choncho mpaka thupi la mwanayo linayamba kutentha.+ 35  Kenako anayamba kuyenda uku ndi uku mʼnyumbamo. Atatero anapitanso kukaweramira mwanayo. Ndiyeno mwanayo anayetsemula maulendo 7, kenako anayamba kuyangʼana.+ 36  Ndiyeno Elisa anaitana Gehazi nʼkumuuza kuti: “Pita ukaitane mayi a mwanayu.”* Gehazi anaitana mayiyo ndipo anabweradi. Elisa anauza mayiyo kuti: “Dzamutengeni mwana wanu.”+ 37  Mayiyo anapita kwa Elisa ndipo anagwada pamapazi ake nʼkumuweramira. Kenako ananyamula mwana wakeyo nʼkutuluka. 38  Kenako Elisa anabwerera ku Giligala ndipo kunali njala.+ Ndiyeno ana a aneneri+ anabwera kwa iye nʼkukhala pansi. Elisa anauza mtumiki wake kuti:+ “Teleka mphika waukulu kuti uwaphikire chakudya ana a aneneriwa.” 39  Mmodzi wa ana aneneriwo anapita kutchire kukathyola masamba. Iye anapezako kamtengo koyanga ka mphonda zakutchire ndipo anathyolapo mphonda zodzaza pachovala chake. Atabwera nazo anaziduladula nʼkuziika mumphika muja koma sankazidziwa bwinobwino. 40  Kenako anapatsa ana a aneneriwo chakudyacho kuti adye. Koma atangoyamba kudya, anakuwa kuti: “Inu munthu wa Mulungu woona, mumphikamu muli poizoni!” Ndipo sanathenso kudya. 41  Ndiyeno Elisa anati: “Bweretsani ufa.” Atathira ufawo mumphikamo, ananena kuti: “Apatseni anthuwa kuti adye.” Atatero, mumphikamo munalibenso poizoni.+ 42  Ndiyeno kunabwera munthu wina kuchokera ku Baala-salisa.+ Iye anabweretsera munthu wa Mulungu woonayo mikate 20 ya balere+ woyambirira kucha komanso thumba la tirigu* watsopano.+ Kenako Elisa anati: “Apatse anthuwa kuti adye.” 43  Koma mtumiki wakeyo anati: “Ndingagawire bwanji anthu 100 chakudya chimenechi?”+ Elisa anati: “Agawire anthuwa kuti adye chifukwa Yehova wanena kuti, ‘Anthu adya nʼkukhuta ndipo china chitsala.’”+ 44  Atamva zimenezi, anagawira anthuwo chakudyacho. Iwo anadya ndipo china chinatsala+ mogwirizana ndi mawu a Yehova.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mayi wa ku Sunemu.”
Nʼkuthekanso kuti anali balere.