2 Mafumu 5:1-27

  • Elisa anachiritsa khate la Namani (1-19)

  • Gehazi wadyera anakhala wakhate (20-27)

5  Panali munthu wina dzina lake Namani, yemwe anali mkulu wa asilikali a mfumu ya Siriya. Iye anali munthu wotchuka ndipo mbuye wake ankamulemekeza kwambiri chifukwa Yehova anapulumutsa Asiriya kudzera mwa iyeyo. Namani anali msilikali wamphamvu ngakhale kuti anali wakhate.*  Ulendo wina asilikali a Siriya atapita kukaukira Aisiraeli anakagwirako kamtsikana nʼkupita nako kwawo ndipo kamtsikanako kanayamba kutumikira mkazi wa Namani.  Kamtsikanako kanauza mbuye wake wamkazi kuti: “Abwanawa akanapita kwa mneneri+ amene ali ku Samariya, bwenzi atakawachiritsa khate lawo.”+  Choncho anakauza* mfumu ya Siriya zimene kamtsikana ka ku Isiraeliko kananena.  Ndiyeno mfumu ya Siriya inauza Namani kuti: “Nyamuka upite. Nditumiza kalata kwa mfumu ya Isiraeli.” Choncho iye ananyamuka atatenga matalente* 10 a siliva, masekeli* 6,000 a golide ndi zovala 10.  Namani anapititsa kalatayo kwa mfumu ya Isiraeli. Mʼkalatayo analembamo kuti: “Ndatumiza kalatayi komanso mtumiki wanga Namani kuti mumʼchiritse khate lake.”  Mfumu ya Isiraeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba zovala zake nʼkunena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu kuti ndili ndi mphamvu zoti ndingaphe munthu kapena kumusiya wamoyo?+ Wanditumizira munthu uyu nʼkundiuza kuti ndimuchiritse khate. Mukhoza kuona nokha kuti akufuna kuyambana nane.”  Koma Elisa, munthu wa Mulungu woona, atamva kuti mfumu ya Isiraeli yangʼamba zovala zake, nthawi yomweyo anatumiza uthenga kwa mfumuyo wakuti: “Nʼchifukwa chiyani mwangʼamba zovala zanu? Muuzeni abwere kuno kuti adziwe kuti ku Isiraeli kuli mneneri.”+  Choncho Namani anapita ndi mahatchi komanso magaleta ake ankhondo ndipo anaima pakhomo la nyumba ya Elisa. 10  Koma Elisa anatuma munthu kukamuuza kuti: “Pitani mukasambe maulendo 7+ mumtsinje wa Yorodano+ ndipo thupi lanu libwerera mwakale ndipo mukhala woyera.” 11  Namani atamva zimenezi anapsa mtima ndipo ananyamuka nʼkumapita. Iye anati: “Ine ndimaganiza kuti abwera kudzaima nane pafupi nʼkuitana dzina la Yehova Mulungu wake, kwinaku akuyendetsa dzanja lake uku ndi uku pamwamba pa khateli kuti andichiritse. 12  Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko,+ si yabwino kuposa madzi onse a mu Isiraeli? Sindingathe kukasamba mmenemo nʼkuyeretsedwa?” Atatero anatembenuka nʼkumapita atakwiya kwambiri. 13  Koma atumiki ake anamutsatira nʼkumufunsa kuti: “Bambo wanga, kodi mneneriyo akanakuuzani kuti muchite chinthu chachikulu, simukanachita? Nanga bwanji poti wangokuuzani kuti, ‘Kasambeni ndipo mukhala woyeraʼ?” 14  Namani atamva zimenezi, anapita kumtsinje wa Yorodano nʼkukasamba* maulendo 7, mogwirizana ndi zimene munthu wa Mulungu woona uja ananena.+ Kenako thupi lake linabwerera mwakale moti khungu lake linakhala ngati la kamnyamata+ ndipo anakhala woyera.+ 15  Zitatero iye ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona uja.+ Atafika ananena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu koma ku Isiraeli.+ Chonde landirani mphatso* iyi kuchokera kwa ine mtumiki wanu.” 16  Koma Elisa anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo amene ndimamutumikira, sindilandira.”+ Namani anamukakamiza kuti alandire, koma iye anakanabe. 17  Kenako Namani anati: “Ngati mukukana, chonde mundipatse ine mtumiki wanu dothi lakuno loti nyulu* ziwiri zikhoza kunyamula. Ndikutero chifukwa ine mtumiki wanu sindidzaperekanso nsembe yopsereza kapena nsembe iliyonse kwa milungu ina, koma kwa Yehova basi. 18  Koma Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani iyi yokha: Mbuyanga akalowa mʼnyumba* ya Rimoni kuti akamugwadire, amatsamira mkono wanga choncho ndimafunika kugwada mʼnyumba ya Rimoni. Ndikagwada mʼnyumba ya Rimoni, chonde Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani imeneyi.” 19  Elisa atamva zimenezi anamuuza kuti: “Pitani mwamtendere.” Choncho iye ananyamuka. Atayenda kamtunda ndithu, 20  Gehazi,+ mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu woona,+ anaganiza mumtima mwake kuti: ‘Zoona mbuyanga wangomusiya Namani wa ku Siriya+ uja osalandira zinthu zomwe anabweretsa? Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, ndimʼthamangira kuti ndikatengeko zinthu zina.’ 21  Gehazi anathamangiradi Namani ndipo Namani ataona kuti munthu akumʼthamangira, anatsika pagaleta lake kuti akumane naye. Kenako anati: “Nʼkwabwino?” 22  Gehazi anayankha kuti: “Inde nʼkwabwino. Mbuyanga wandituma kuti, ‘Posachedwapa kwabwera anyamata awiri, ana a aneneri, kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu. Muwapatseko talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.’”+ 23  Namani anamuuza kuti: “Chabwino. Tenga matalente awiri.” Anamuumiriza+ ndipo anamʼmangira matalente awiri a siliva mʼmatumba awiri ndi zovala ziwiri. Anapereka zinthuzo kwa atumiki ake awiri kuti amunyamulire. 24  Atafika ku Ofeli,* Gehazi anawalandira anthuwo katunduyo ndipo anamuika mʼnyumba nʼkuwauza kuti azipita. Anthuwo atapita, 25  Gehazi anapita kukaima pafupi ndi mbuye wake. Kenako Elisa anamʼfunsa kuti: “Kodi unapita kuti Gehazi?” Koma iye anayankha kuti: “Ine mtumiki wanu sindinapite kulikonse.”+ 26  Ndiyeno Elisa anati: “Kodi mtima wanga sunali nawe limodzi pamene munthuyo amatsika pagaleta lake kuti akumane nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira siliva, zovala, minda ya maolivi, minda ya mpesa, nkhosa, ngʼombe, antchito aamuna kapena antchito aakazi?+ 27  Tsopano khate la Namani+ libwera kwa iweyo ndi mbadwa zako ndipo silidzachoka mpaka kalekale.” Nthawi yomweyo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa, atachita khate moti anayera kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anali ndi matenda apakhungu.”
Nʼkutheka kuti ameneyu ndi Namani.
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nʼkukamira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dalitso.”
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Kapena kuti, “kachisi.”
Malo amenewa anali ku Samariya. Nʼkutheka kuti linali phiri kapena malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri.