2 Mafumu 6:1-33

  • Elisa anayandamitsa nkhwangwa (1-7)

  • Elisa ndi Asiriya (8-23)

    • Maso a mtumiki wa Elisa anatsegulidwa (16, 17)

    • Asiriya anachititsidwa khungu lamaganizo (18, 19)

  • Mumzinda wa Samariya munali njala chifukwa choti unazunguliridwa (24-33)

6  Ana a aneneri+ anauza Elisa kuti: “Malo amene tikukhalawa ndi opanikiza.  Bwanji tipite ku Yorodano? Aliyense akatenge mtengo kuti tikamangire malo okhala.” Elisa anati: “Pitani.”  Ndiyeno wina anati: “Bwanji inu ndi ife atumiki anu tipitire limodzi?” Elisa anayankha kuti: “Chabwino, ndipita nanu.”  Choncho anapita nawo limodzi ndipo atafika ku Yorodano anayamba kudula mitengo.  Munthu wina akudula mtengo, nkhwangwa inaguluka nʼkugwera mʼmadzi. Zitatero munthuyo anafuula kuti: “Mayo ine! Nkhwangwayi inali yobwereka!”  Munthu wa Mulungu woonayo anafunsa kuti: “Yagwera pati?” Iye anamusonyeza pamene inagwera. Elisa anadula kamtengo nʼkukaponya pamene inagwerapo ndipo nkhwangwayo inayandama.  Ndiyeno anamuuza kuti, “Itenge,” ndipo munthuyo anaitenga.  Kenako mfumu ya Siriya inapita kukamenyana ndi Aisiraeli.+ Choncho inakambirana ndi atumiki ake kuti: “Tikasonkhane pamalo akutiakuti.”  Ndiyeno munthu wa Mulungu woona uja+ anatumiza uthenga kwa mfumu ya Isiraeli, wakuti: “Musadutse pamalo akutiakuti chifukwa Asiriya akupita kumeneko.” 10  Mfumu ya Isiraeli inatumiza uthenga wochenjeza anthu akumalo amene munthu wa Mulungu woona uja ananena. Elisa anachenjeza mfumu ya Isiraeli maulendo angapo* ndipo akaichenjeza sinkapitako.+ 11  Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mfumu ya Siriya, choncho inaitanitsa atumiki ake nʼkuwafunsa kuti: “Ndiuzeni, ndi ndani pa gulu lathuli amene ali kumbali ya mfumu ya Isiraeli?” 12  Mmodzi wa atumiki ake anati: “Palibe, mbuyanga mfumu. Mneneri Elisa wa ku Isiraeli, ndi amene amauza mfumu ya Isiraeli zinthu zimene inuyo mumalankhula kuchipinda kwanu.”+ 13  Choncho mfumuyo inati: “Pitani mukafufuze kumene ali kuti nditumizeko anthu akamugwire.” Kenako mfumuyo inauzidwa kuti: “Ali ku Dotani.”+ 14  Nthawi yomweyo mfumuyo inatumizako mahatchi, magaleta ankhondo ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iwo anafikako usiku nʼkuzungulira mzindawo. 15  Mtumiki wa munthu wa Mulungu woona atadzuka mʼmawa nʼkutuluka panja, anaona kuti gulu lankhondo lazungulira mzindawo ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo. Nthawi yomweyo mtumikiyo anauza mbuye wake kuti: “Mayo ine mbuyanga! Titani?” 16  Koma iye anati: “Usaope,+ ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.”+ 17  Kenako Elisa anayamba kupemphera kuti: “Inu Yehova, chonde mutseguleni maso kuti aone.”+ Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumikiyo, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa+ linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.+ 18  Asiriyawo atayamba kupita kumene kunali Elisa, iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Chonde chititsani khungu+ mtundu uwu.” Choncho Mulungu anawachititsa khungu mogwirizana ndi zimene Elisa anapempha. 19  Kenako Elisa anawauza kuti: “Njira yake si imeneyi ndipo mzinda wake si umenewu. Nditsatireni, ndikulondolerani kwa munthu amene mukufuna.” Koma anawapititsa ku Samariya.+ 20  Atangofika ku Samariya, Elisa anati: “Chonde Yehova, atseguleni maso anthuwa kuti aone.” Choncho Yehova anatsegula maso awo ndipo anaona kuti ali pakatikati pa Samariya. 21  Mfumu ya Isiraeli itaona anthuwo, inafunsa Elisa kuti: “Kodi ndiwaphe? Bambo anga, ndiwaphe?” 22  Koma Elisa anati: “Musawaphe. Kodi mukufuna kupha anthu amene mwawagonjetsa ndi lupanga ndi uta nʼkuwagwira? Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa.+ Kenako azipita kwa mbuye wawo.” 23  Choncho mfumuyo inawakonzera phwando lalikulu ndipo anadya ndi kumwa. Atatha anawauza kuti azipita kwa mbuye wawo. Kuchokera pamenepo, magulu a achifwamba a ku Siriya+ sanabwerenso ku Isiraeli. 24  Patapita nthawi Beni-hadadi mfumu ya Siriya anasonkhanitsa asilikali ake onse ndipo anapita kukazungulira mzinda wa Samariya.+ 25  Choncho mu Samariya munagwa njala yaikulu.+ Asiriyawo anapitirizabe kuzungulira mzindawo mpaka mtengo wogulira mutu wa bulu+ unafika pa ndalama 80 zasiliva ndipo zitosi za nkhunda zodzaza manja awiri* mtengo wake unali ndalama 5 zasiliva. 26  Mfumu ya Isiraeli ikuyenda pamwamba pa khoma, mayi wina anafuulira mfumuyo kuti: “Ndithandizeni mbuyanga mfumu!” 27  Mfumuyo inayankha kuti: “Ngati Yehova sakukuthandiza ndiye ine ndingakuthandize ndi chiyani? Kodi ndingakuthandize ndi zochokera popunthira mbewu, mopondera mphesa kapena moyengera mafuta?” 28  Ndiyeno mfumuyo inamʼfunsa kuti: “Chavuta nʼchiyani?” Mayiyo anayankha kuti: “Mayi uyu anandiuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye lero ndipo mawa tidzadya mwana wanga.’+ 29  Choncho tinaphika mwana wanga nʼkumudya.+ Tsiku lotsatira ndinauza mayiyu kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye.’ Koma iye anakamʼbisa.” 30  Mfumuyo itangomva mawu a mayiyo, inangʼamba zovala zake.+ Pamene inkayenda pamwamba pa khomalo, anthu anaona kuti yavala chiguduli mkati. 31  Kenako inanena kuti: “Mulungu andilange mowirikiza, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati sudulidwa lero!”+ 32  Elisa anali mʼnyumba mwake pamodzi ndi akulu. Mfumu inatumiza munthu kuti atsogole kupita kwa Elisa, koma munthuyo asanafike Elisa anauza akuluwo kuti: “Kodi mwaona kuti mwana wa munthu wopha anthu+ uja watumiza munthu kuti adzandidule mutu? Muonetsetse kuti munthuyo akangofika mutseke chitseko ndipo muchitsamire kuti asalowe. Kodi mapazi a mbuye wake si amene akumveka pambuyo pakewo?” 33  Elisa ali mkati molankhula nawo, munthu uja anafika ndipo mfumu inati: “Tsokali lachokera kwa Yehova. Kodi pali chifukwa choti ndipitirizire kuyembekezera Yehova?”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “osati kamodzi kapena kawiri kokha.”
Zitosi zimenezi zinali zokwana gawo limodzi la magawo 4 a kabu. Kabu imodzi inali pafupifupi lita imodzi. Onani Zakumapeto B14.