2 Mafumu 7:1-20

  • Elisa analosera za kutha kwa njala (1, 2)

  • Chakudya chinangosiyidwa mumsasa wa Asiriya (3-15)

  • Ulosi wa Elisa unakwaniritsidwa (16-20)

7  Elisa anati: “Mverani mawu a Yehova. Yehova wanena kuti, ‘Mawa nthawi ngati ino, pageti* la Samariya ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya,* mtengo wake udzakhala sekeli* limodzi ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake udzakhalanso sekeli limodzi.’”+  Koma msilikali wothandiza mfumu amene mfumu inkamudalira, anayankha munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba, kodi zimenezo zingachitike?”+ Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako,+ koma sudya nawo.”+  Ndiyeno panali anthu 4 akhate amene anali pageti+ ndipo anayamba kukambirana kuti: “Kodi tingokhala pano mpaka tife?  Tikati, ‘Tiyeni tilowe mumzinda,’ tikafa ndi njala.+ Tikatinso tikhale pano, tifa. Ndiye tiyeni tikalowe mumsasa wa Asiriya. Akakapanda kutipha, tikakhala ndi moyo koma akakatipha, basi tikafa.”  Choncho ananyamuka kukungoyamba kumene kuda, kupita kumsasa wa Asiriya. Koma atafika mʼmbali mwa msasawo, anapeza kuti munalibe aliyense.  Yehova anali atachititsa asilikali a mumsasa wa Asiriyawo kumva phokoso la magaleta ankhondo, phokoso la mahatchi ndi phokoso la gulu lalikulu la asilikali.+ Choncho anthuwo anauzana kuti: “Anthuni! Mfumu ya Isiraeli yaitanitsa mafumu a Ahiti ndi mafumu a Iguputo kuti adzamenyane nafe!”  Nthawi yomweyo asilikaliwo ananyamuka nʼkuyamba kuthawa kukungoyamba kumene kuda. Anasiya mahema awo, mahatchi awo komanso abulu awo. Msasawo anausiya mmene unalili nʼkuthawa kuti apulumutse moyo wawo.  Akhate aja atafika mʼmbali mwa msasawo, analowa mutenti ina ndipo anayamba kudya ndi kumwa. Kenako anatengamo siliva, golide ndi zovala nʼkupita kukazibisa. Atatero anabwerera nʼkudzalowanso mutenti ina ndipo anatengamonso zinthu zina nʼkukazibisa.  Kenako anayamba kuuzana kuti: “Zimene tikuchitazi si zabwino. Tiyeni tikauze ena nkhani yabwinoyi! Tikazengereza mpaka kucha, tikhala ndi mlandu woyenera kulangidwa. Tiyeni tipite tikanene nkhaniyi kunyumba ya mfumu.” 10  Choncho akhatewo anapita nʼkukafuulira alonda apageti la mzinda kuti: “Tinapita kumsasa wa Asiriya koma tapeza kuti kulibe anthu ndipo sikukumveka mawu a munthu aliyense! Kuli mahatchi ndi abulu omangidwa, komanso matenti angowasiya mmene analili!” 11  Nthawi yomweyo, alonda apagetiwo anafuula ndipo uthengawo unafika kunyumba ya mfumu. 12  Mfumuyo itangomva inadzuka usikuwo ndipo inauza atumiki ake kuti: “Tadikirani ndikuuzeni zimene Asiriyawa achita. Akudziwa kuti ife tili ndi njala,+ choncho achoka mumsasamo nʼkukabisala kutchire. Maganizo awo ndi akuti, ‘Atuluka mumzindamo ndipo tiwagwira amoyo. Kenako ifeyo tikalowa mumzindamo.’”+ 13  Ndiyeno mtumiki wina wa mfumu anati: “Uzani anthu atenge mahatchi 5 pa mahatchi amene atsala mumzindawu ndipo muwatume akaone. Zimene zingakawachitikire anthuwo sizingasiyane ndi zimene zichitikire gulu la Aisiraeli amene atsala mumzindamu. Komanso sizingasiyane ndi zimene zachitikira gulu la Aisiraeli amene afa.” 14  Choncho iwo anatenga magaleta awiri ndi mahatchi ndipo mfumu inawatuma kumsasa wa Asiriya nʼkuwauza kuti: “Pitani mukaone.” 15  Anthuwo anatsatira Asiriyawo mpaka kukafika ku Yorodano ndipo mʼnjira monse munali zovala ndi ziwiya zimene Asiriyawo anataya pamene ankathawa mwamantha. Kenako anthuwo anabwerera nʼkukanena kwa mfumu. 16  Zitatero, anthu anapita kukatenga zinthu mumsasa wa Asiriya. Choncho ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake unafika pa sekeli imodzi ndipo balere wokwana miyezo iwiri ya seya, mtengo wake unafikanso pa sekeli imodzi, mogwirizana ndi mawu a Yehova.+ 17  Mfumu inaika msilikali woithandiza amene inkamudalira uja kuti aziyangʼanira pageti. Koma anthu anamʼpondaponda pagetipo moti anafa, mogwirizana ndi zimene munthu wa Mulungu woona uja ananena, pamene mfumu inapita kwa iye. 18  Zinachitikadi ngati mmene munthu wa Mulungu woona uja anauzira mfumu, kuti: “Balere wokwana miyezo iwiri ya seya mtengo wake udzakhala sekeli imodzi ndipo ufa wosalala wokwana muyezo umodzi wa seya, mtengo wake udzakhalanso sekeli imodzi mawa, nthawi ngati ino pageti la Samariya.”+ 19  Koma msilikali wothandiza mfumu uja anayankha munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba, kodi zimenezi zingachitike?” Ndiyeno Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako, koma sudya nawo.” 20  Choncho izi ndi zimene zinamuchitikiradi chifukwa anthu anamʼpondaponda pageti mpaka kufa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼmisika.”
Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.