2 Mafumu 8:1-29

  • Mayi wa ku Sunemu anabwezeredwa malo ake (1-6)

  • Elisa, Beni-hadadi ndi Hazaeli (7-15)

  • Yehoramu, mfumu ya Yuda (16-24)

  • Ahaziya, mfumu ya Yuda (25-29)

8  Elisa anauza mayi amene anamuukitsira mwana+ uja, kuti: “Nyamuka, iwe ndi banja lako, ukakhale mlendo kulikonse kumene ungasankhe, chifukwa Yehova wanena kuti mʼdzikoli mudzakhala njala+ kwa zaka 7.”  Choncho mayiyo ndi banja lake ananyamuka nʼkupita kukakhala mʼdziko la Afilisiti+ kwa zaka 7, mogwirizana ndi zimene munthu wa Mulungu woonayo ananena.  Zaka 7 zitatha, mayiyo anabwerera kuchokera kudziko la Afilisiti nʼkupita kukapempha mfumu kuti imubwezere nyumba yake ndi munda wake.  Pa nthawiyo nʼkuti mfumu ikulankhula ndi Gehazi mtumiki wa munthu wa Mulungu woona, kuti: “Ndifotokozere zinthu zonse zazikulu zimene Elisa wachita.”+  Gehazi akufotokozera mfumuyo mmene Elisa anaukitsira munthu wakufa,+ mayi wa mwana amene anaukitsidwayo anafika kwa mfumu nʼkuyamba kupempha kuti amubwezere nyumba yake ndi munda wake.+ Nthawi yomweyo Gehazi anati: “Mbuyanga mfumu, mayi ndimanena uja ndi uyu ndipo mwana wake amene Elisa anamuukitsayo ndi uyu.”  Ndiyeno mfumuyo inapempha mayiyo kuti afotokoze nkhani yonse ndipo mayiyo anafotokozadi. Kenako mfumuyo inauza nduna ya panyumba yake kuti: “Mayiyu umʼbwezere zinthu zake zonse komanso umupatse ndalama zimene akanapeza pa zokolola za kumunda kwake kuyambira pamene anachoka mpaka lero.”  Kenako Elisa anapita ku Damasiko+ ndipo pa nthawiyo nʼkuti Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya akudwala. Choncho mfumuyo inauzidwa kuti: “Munthu wa Mulungu woona+ uja wabwera kuno.”  Mfumuyo itamva zimenezi, inauza Hazaeli+ kuti: “Tenga mphatso ndipo upite kwa munthu wa Mulungu woonayo.+ Ukafunse kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’”  Choncho Hazaeli anatenga mphatso nʼkupita kukakumana naye. Mphatsozo anazinyamula pa ngamira zokwana 40. Anatenga chinthu chilichonse chabwino cha ku Damasiko. Atafika kwa Elisa anamuuza kuti: “Mwana wanu Beni-hadadi mfumu ya Siriya wandituma kudzakufunsani kuti, ‘Kodi ndichira matenda angawa?’” 10  Ndiyeno Elisa anayankha Hazaeli kuti: “Pita ukamuuze kuti, ‘Muchira ndithu.’ Koma Yehova wandionetsa kuti afa ndithu.”+ 11  Elisa anayangʼanitsitsa Hazaeli mpaka Hazaeliyo anachita manyazi. Kenako munthu wa Mulungu woonayo anayamba kulira. 12  Hazaeli anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulira mbuyanga?” Elisa anayankha kuti: “Chifukwa ndikudziwa zoipa zimene iweyo udzachitire Aisiraeli.+ Malo awo otetezedwa udzawatentha ndi moto, amuna amphamvu udzawapha ndi lupanga, ana awo aangʼono udzawanyenyanyenya ndipo akazi awo apakati udzawatumbula.”+ 13  Hazaeli atamva mawu amenewa, anati: “Zingatheke bwanji kuti ine mtumiki wanu, galu ngati ine, ndichite zinthu ngati zimenezi?” Koma Elisa anati: “Yehova wandionetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Siriya.”+ 14  Kenako Hazaeli anachoka kwa Elisa nʼkubwerera kwa mbuye wake ndipo iye anamufunsa kuti: “Kodi Elisa wakuuza kuti chiyani?” Hazaeli anayankha kuti: “Wandiuza kuti, ‘Muchira ndithu.’”+ 15  Tsiku lotsatira, Hazaeli anatenga chofunda nʼkuchiviika mʼmadzi kenako anaphimba mfumuyo kumaso mpaka inamwalira.+ Ndiyeno Hazaeli anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+ 16  Mʼchaka cha 5 cha Yehoramu+ mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, pamene Yehosafati anali mfumu ya Yuda, Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, anakhala mfumu. 17  Yehoramu anakhala mfumu ali ndi zaka 32 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. 18  Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabu,+ chifukwa anakwatira mwana wa Ahabu.+ Ndipo iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 19  Koma Yehova sanafune kuwononga ufumu wa Yuda chifukwa cha Davide mtumiki wake,+ poti anamulonjeza kuti adzamʼpatsa nyale+ nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake. 20  Mʼmasiku a Yehoramu, Aedomu anagalukira Yuda+ ndipo kenako anasankha mfumu yoti iziwalamulira.+ 21  Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku nʼkukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso atsogoleri a asilikali okwera magaleta ndipo asilikali ena onse anathawira kumatenti awo. 22  Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Pa nthawi imeneyi mʼpamenenso Libina+ anagalukira Yuda. 23  Nkhani zina zokhudza Yehoramu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 24  Kenako Yehoramu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Kenako mwana wake Ahaziya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake. 25  Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 12 cha Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli.+ 26  Ahaziya anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Mayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu wa Omuri+ mfumu ya Isiraeli. 27  Iye anayenda mʼnjira ya anthu a mʼbanja la Ahabu+ ndipo anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabuwo, chifukwa anali wachibale wawo.+ 28  Choncho iye anapita ku nkhondo ndi Yehoramu mwana wa Ahabu kukamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Koma Asiriyawo anavulaza Yehoramu.+ 29  Choncho Mfumu Yehoramu inabwerera ku Yezereeli+ kuti ikachire mabala amene Asiriya anaivulaza ku Rama,* pamene inkamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anali atavulazidwa.*

Mawu a M'munsi

“Rama” ndi chidule cha Ramoti-giliyadi.
Kapena kuti, “anavulala.”