2 Mbiri 1:1-17

  • Solomo anapempha nzeru (1-12)

  • Chuma cha Solomo (13-17)

1  Ufumu wa Solomo mwana wa Davide unakhala wamphamvu. Yehova Mulungu wake anali naye ndipo anamuchititsa kukhala wamphamvu kwambiri.+  Solomo anaitanitsa Aisiraeli onse, atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, oweruza ndi akuluakulu onse a mu Isiraeli, amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo.  Kenako Solomo ndi mpingo wonsewo anapita kumalo okwezeka ku Gibiyoni.+ Anapita kumeneko chifukwa nʼkumene kunali chihema chokumanako cha Mulungu woona, chimene Mose mtumiki wa Yehova anapanga mʼchipululu.  Koma Davide anali atachotsa Likasa la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ nʼkukaliika pamalo amene anakonza. Iye anali atamanga tenti ya Likasalo ku Yerusalemu.+  Guwa lansembe lakopa*+ limene Bezaleli+ mwana wa Uri mwana wa Hura anapanga, anali ataliika patsogolo pa chihema chopatulika cha Yehova. Ndipo Solomo ndi mpingowo ankapemphera patsogolo pa guwalo.  Kenako Solomo anapereka nsembe zopsereza 1,000 pamaso pa Yehova, paguwa lansembe lakopalo+ limene linali kuchihema chokumanako.  Usiku wa tsiku limenelo, Mulungu anaonekera kwa Solomo nʼkumuuza kuti: “Pempha chimene ukufuna ndikupatse.”+  Solomo atamva zimenezi anauza Mulungu kuti: “Inu mwasonyeza kwambiri chikondi chokhulupirika kwa mtumiki wanu Davide+ bambo anga ndipo mwandiika kukhala mfumu mʼmalo mwake.+  Tsopano inu Yehova Mulungu, kwaniritsani lonjezo limene munapereka kwa Davide bambo anga+ popeza mwandiika kukhala mfumu ya anthuwa, omwe ndi ochuluka kwambiri ngati fumbi.+ 10  Mundipatse nzeru ndi luso lodziwa zinthu+ kuti ndizitha kutsogolera anthuwa. Ndani angaweruze anthu anu ochulukawa?”+ 11  Ndiyeno Mulungu anauza Solomo kuti: “Chifukwa zimenezi ndi zimene mtima wako ukulakalaka, ndipo sunapemphe katundu, chuma, ulemu kapenanso moyo wa anthu amene amadana nawe, sunapemphenso kuti ukhale ndi moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luso lodziwa zinthu kuti uziweruza anthu anga amene ndakupatsa kuti ukhale mfumu yawo,+ 12  ndikupatsa nzeru ndi luso lodziwa zinthu. Ndikupatsanso katundu, chuma ndi ulemu zochuluka kwambiri kuposa zimene anali nazo mafumu amene anakhalako iwe usanakhaleko ndiponso zoposa zimene aliyense wobwera pambuyo pako adzakhale nazo.”+ 13  Zitatero, Solomo anabwerera ku Yerusalemu kuchokera kumalo okwezeka ku Gibiyoni,+ kuchihema chokumanako, ndipo anapitiriza kulamulira Isiraeli. 14  Solomo anasonkhanitsa magaleta ndi mahatchi,* moti anakhala ndi magaleta 1,400 ndi mahatchi* 12,000.+ Zonsezi ankazisunga mʼmizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu.+ 15  Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva ndi golide akhale wambiri ngati miyala+ ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ambiri ngati mitengo yamkuyu ya ku Sefela.+ 16  Mahatchi a Solomo ankawagula kuchokera ku Iguputo+ ndipo gulu la amalonda a mfumu linkagula mahatchiwo mʼmagulumagulu.*+ 17  Galeta lililonse lochokera ku Iguputo mtengo wake unali ndalama zasiliva 600 pomwe mtengo wa hatchi unali ndalama zasiliva 150. Ndipo iwo ankagulitsa zinthuzi kwa mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a ku Siriya.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lamkuwa.”
Kapena kuti, “okwera pamahatchi.” Ena amati “mahosi.”
Kapena kuti, “Okwera pamahatchi.”
Mabaibulo ena amati, “kuchokera ku Iguputo ndi ku Kuwe. Amalonda a mfumu ankawagula ku Kuwe,” mwina kutanthauza ku Kilikiya.