2 Mbiri 10:1-19

  • Aisiraeli anagalukira Rehobowamu (1-19)

10  Rehobowamu anapita ku Sekemu+ chifukwa Aisiraeli onse anapita kumeneko kuti akamuveke ufumu.+  Yerobowamu+ mwana wa Nebati atangomva zimenezi, anabwerera kuchokera ku Iguputo. (Iye anali adakali ku Iguputoko chifukwa anathawa Mfumu Solomo.)+  Kenako anthu anatumiza uthenga womuitana Yerobowamuyo ndipo iye ndi Aisiraeli onse anabwera nʼkuyamba kulankhula ndi Rehobowamu kuti:  “Bambo anu anachititsa kuti goli lathu likhale lowawa.+ Koma inuyo mukatifewetsera ntchito yowawa ya bambo anu komanso goli lolemera limene ankatisenzetsa, tizikutumikirani.”  Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Mukabwerenso pakatha masiku atatu.” Choncho anthuwo anapitadi.+  Ndiyeno Mfumu Rehobowamu anafunsa nzeru kwa anthu achikulire* amene ankatumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Anawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?”  Iwo anamuuza kuti: “Mukakhala munthu wabwino kwa anthuwa, kuchita zowasangalatsa ndiponso kuwayankha bwino, iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”  Koma iye sanamvere malangizo amene anthu achikulirewo* anamupatsa, ndipo anapita kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi, omwe ankamutumikira.+  Iye anawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti tiwayankhe bwanji anthuwa, amene andiuza kuti, ‘Mutifewetsere goli limene bambo anu anatisenzetsaʼ?” 10  Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Anthu amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsirekoʼ mukawauze kuti, ‘Chala changa chachingʼono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga. 11  Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo. Bambo anga ankakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndizikukwapulani ndi zikoti zaminga.’” 12  Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, mogwirizana ndi zimene mfumuyo inanena kuti: “Mukabwerenso pakatha masiku atatu.”+ 13  Koma mfumuyo inawayankha mwaukali. Ndipo Mfumu Rehobowamu sanamvere malangizo a anthu achikulire* aja. 14  Inayankha anthuwo motsatira malangizo a achinyamata aja. Inati: “Ine ndidzachititsa kuti goli lanu likhale lolemera kwambiri, ndipo ndidzaliwonjezera. Bambo anga ankakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndizikukwapulani ndi zikoti zaminga.” 15  Choncho mfumu sinamvere anthuwo. Mulungu woona+ ndi amene anachititsa kuti zinthu zikhale chonchi, kuti akwaniritse mawu amene Yehova analankhula kwa Yerobowamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya+ wa ku Silo. 16  Aisiraeli onse ataona kuti mfumuyo yakana kuwamvera, anayankha kuti: “Ife Davide tilibe naye ntchito ndipo sitingapatsidwe cholowa kuchokera kwa mwana wa Jese. Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu yake! Tsopano iwe Davide,+ uziyangʼanira nyumba yako yokha.” Zitatero, Aisiraeli onsewo anabwerera kunyumba* kwawo.+ 17  Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira Aisiraeli amene ankakhala mʼmizinda ya ku Yuda.+ 18  Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Hadoramu+ amene ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yokakamiza, koma Aisiraeli anamugenda ndi miyala nʼkumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inatha kukwera galeta lake nʼkuthawira ku Yerusalemu.+ 19  Ndipo Aisiraeli akupitiriza kuukira nyumba ya Davide mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akulu.”
Kapena kuti, “akuluwo.”
Kapena kuti, “akulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumatenti.”