2 Mbiri 11:1-23

  • Ulamuliro wa Rehobowamu (1-12)

  • Alevi okhulupirika anasamukira ku Yuda (13-17)

  • Banja la Rehobowamu (18-23)

11  Rehobowamu atangofika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa asilikali ophunzitsidwa bwino* okwana 180,000 a nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi Aisiraeli kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu.+  Kenako Semaya,+ munthu wa Mulungu woona, anamva mawu ochokera kwa Yehova kuti:  “Ukauze Rehobowamu, mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, komanso Aisiraeli onse a ku Yuda ndi ku Benjamini kuti,  ‘Yehova wanena kuti: “Musapite kukamenyana ndi abale anu. Aliyense abwerere kunyumba kwawo chifukwa ine ndi amene ndachititsa zimenezi.”’”+ Choncho anthuwo anamvera mawu a Yehova nʼkubwerera kwawo ndipo sanapite kukamenyana ndi Yerobowamu.  Rehobowamu ankakhala ku Yerusalemu, ndipo anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri mʼdziko la Yuda.  Analimbitsanso mizinda ya Betelehemu,+ Etami, Tekowa,+  Beti-zuri, Soko,+ Adulamu,+  Gati,+ Maresha, Zifi,+  Adoraimu, Lakisi,+ Azeka,+ 10  Zora, Aijaloni+ ndi Heburoni.+ Imeneyi inali mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri imene inali ku Yuda ndi ku Benjamini. 11  Kuwonjezera pamenepo, analimbitsanso malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri nʼkuikamo atsogoleri. Atatero mʼmizindamo anaikamo chakudya, mafuta ndi vinyo. 12  Mʼmizinda yonse anaikamo zishango zazikulu ndi mikondo ingʼonoingʼono. Mizindayo anailimbitsa kwambiri ndipo iye anapitiriza kulamulira Yuda ndi Benjamini. 13  Ansembe ndi Alevi amene anali mʼmadera onse mu Isiraeli anakhala kumbali ya Rehobowamu, ndipo anabwera kuchokera mʼmadera awo onse. 14  Aleviwo anasiya malo awo odyetserako ziweto ndi madera awo+ nʼkupita ku Yuda ndi ku Yerusalemu, chifukwa Yerobowamu ndi ana ake anachotsa Aleviwo pa udindo wokhala ansembe a Yehova.+ 15  Kenako Yerobowamu anaika ansembe ake mʼmalo okwezeka+ kuti azitumikira ziwanda+ zooneka ngati mbuzi* ndi mafano a ana a ngʼombe amene iye anapanga.+ 16  Koma anthu a mʼmafuko onse a Isiraeli amene anali ndi mtima wofunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli, anatsatira ansembe ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.+ 17  Iwo analimbitsa ufumu wa Yuda ndiponso kuthandiza Rehobowamu mwana wa Solomo kwa zaka zitatu, popeza anthuwo anayenda mʼnjira ya Davide ndi ya Solomo kwa zaka zitatu. 18  Rehobowamu anakwatira Mahalati mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide. Amayi ake a Mahalati anali Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Jese.+ 19  Patapita nthawi, Mahalatiyo anaberekera Rehobowamu ana awa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu. 20  Kenako Rehobowamu anakwatira Maaka mdzukulu wa Abisalomu.+ Ndiyeno mkaziyo anamʼberekera ana awa: Abiya,+ Atai, Ziza ndi Selomiti. 21  Rehobowamu ankakonda kwambiri Maaka mdzukulu wa Abisalomu kuposa akazi ake ena onse ndi akazi ake aangʼono.*+ Iye anakwatira akazi 18 ndipo anali ndi akazi aangʼono 60. Iye anabereka ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60. 22  Choncho Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri wa abale ake, chifukwa ankafuna kuti adzamʼpatse ufumu. 23  Komabe anachita mozindikira chifukwa anapititsa ana ake ena mʼmadera onse a ku Yuda ndi ku Benjamini komanso mʼmizinda yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Anawapatsa zinthu zambiri nʼkuwapezeranso akazi ambirimbiri.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ochita kusankhidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “azitumikira mbuzi.”
Kapena kuti, “adzakazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.