2 Mbiri 12:1-16

  • Sisaki anaukira Yerusalemu (1-12)

  • Kutha kwa ulamuliro wa Rehobowamu (13-16)

12  Ufumu wa Rehobowamu utangokhazikika+ ndiponso iye atangokhala wamphamvu, iye ndi Aisiraeli onse anasiya Chilamulo cha Yehova.+  Mʼchaka cha 5 cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki+ mfumu ya Iguputo anabwera kudzaukira Yerusalemu, chifukwa iwo anachita zosakhulupirika kwa Yehova.  Anabwera kuchokera ku Iguputo ndi magaleta 1,200, amuna okwera pamahatchi 60,000 komanso anthu osawerengeka. Anthuwo anali Alibiya, Asuki ndi Aitiyopiya.+  Sisakiyo analanda mizinda ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo kenako anafika ku Yerusalemu.  Mneneri Semaya+ anapita kwa Rehobowamu ndi kwa akalonga a Yuda amene anasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisaki nʼkuwauza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Inuyo mwandisiya, choncho inenso ndakusiyani+ ndipo ndakuperekani mʼmanja mwa Sisaki.’”  Akalonga a Isiraeliwo ndi mfumuyo atamva zimenezi, anadzichepetsa+ nʼkunena kuti: “Yehova ndi wolungama.”  Yehova ataona kuti anthuwo adzichepetsa, Yehovayo anauza Semaya kuti: “Anthuwa adzichepetsa, choncho sindiwawononga.+ Posachedwapa ndiwapulumutsa, ndipo Yerusalemu sindidzamusonyeza mkwiyo wanga kudzera mwa Sisaki.  Koma iwo akhala atumiki ake kuti adziwe kusiyana kotumikira ine ndi kutumikira mafumu* a mayiko ena.”  Choncho Sisaki mfumu ya Iguputo anaukira Yerusalemu. Iye anatenga chuma chamʼnyumba ya Yehova+ ndi chuma chamʼnyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomo anapanga.+ 10  Choncho Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zakopa* mʼmalomwake ndipo anazipereka kwa akulu a asilikali* olondera pakhomo la nyumba ya mfumu kuti aziziyangʼanira. 11  Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikaliwo ankanyamula zishangozo ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda. 12  Chifukwa chakuti mfumu inadzichepetsa, Yehova anabweza mkwiyo wake+ ndipo sanawononge anthu onsewo.+ Komanso anapeza kuti panali zinthu zina zabwino zomwe anthu a ku Yuda ankachita.+ 13  Mfumu Rehobowamu inalimbitsa ufumu wake ku Yerusalemu ndipo inapitiriza kulamulira. Rehobowamu anali ndi zaka 41 pamene ankayamba kulamulira, ndipo analamulira kwa zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anasankha pa mafuko onse a Isiraeli kuti kukhale dzina lake. Mayi ake anali Naama, mbadwa ya Amoni.+ 14  Koma iye anachita zoipa chifukwa sanatsimikize mumtima mwake kufunafuna Yehova.+ 15  Nkhani zina zokhudza Rehobowamu, kuyambira zoyamba mpaka zomaliza, zikupezeka mʼzimene analemba mneneri Semaya+ ndiponso Ido+ wamasomphenya, motsatira mndandanda wa mayina a makolo. Pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu pankachitika nkhondo nthawi zonse.+ 16  Kenako Rehobowamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.+ Ndiyeno Abiya+ mwana wa Rehobowamu anayamba kulamulira mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “maufumu.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Kapena kuti, “asilikali othamanga.”