2 Mbiri 14:1-15

  • Imfa ya Abiya (1)

  • Asa, mfumu ya Yuda (2-8)

  • Asa anagonjetsa Aitiyopiya 1 miliyoni (9-15)

14  Kenako Abiya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.+ Ndiyeno mwana wake Asa anakhala mfumu mʼmalo mwake. Mʼmasiku ake, mʼdzikomo munali mtendere kwa zaka 10.  Asa anachita zabwino ndiponso zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.  Iye anachotsa maguwa ansembe achilendo,+ anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika+ komanso anagwetsa mizati yopatulika.*+  Anauzanso Ayuda kuti afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndiponso kuti azitsatira Chilamulo ndi zonse zimene anawalamula.  Iye anachotsa malo okwezeka ndi maguwa operekera nsembe zonunkhira+ mʼmizinda yonse ya Yuda, ndipo ufumu wake unapitiriza kukhala wopanda chosokoneza chilichonse.  Anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri mʼdziko la Yuda,+ chifukwa mʼdzikolo munalibe chosokoneza chilichonse komanso munalibe nkhondo pa zaka zimenezi, chifukwa Yehova anamʼpatsa mpumulo.+  Iye anauza Ayuda kuti: “Tiyeni timange mizindayi ndi mipanda yake ndiponso nsanja.+ Tiikenso mageti* ndi mipiringidzo. Dzikoli lidakali mʼmanja mwathu chifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu. Tamufunafuna ndipo watipatsa mpumulo mʼdziko lonse.” Choncho ntchito yawo yomanga inayenda bwino.+  Asa anali ndi asilikali 300,000 a fuko la Yuda onyamula zishango zazikulu ndi mikondo ingʼonoingʼono. Analinso ndi asilikali amphamvu okwana 280,000 a fuko la Benjamini onyamula mauta* ndi zishango zazingʼono.*+  Kenako Zera wa ku Itiyopiya anabwera kudzamenyana nawo ali ndi gulu lankhondo la asilikali 1 miliyoni ndi magaleta 300.+ Atafika ku Maresha,+ 10  Asa anapita kukamenyana naye ndipo iwo anakonzekera kumenya nkhondo mʼchigwa cha Sefata ku Maresha. 11  Ndiyeno Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake+ kuti: “Inu Yehova, zilibe kanthu kuti anthu amene mukufuna kuwathandizawo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera mʼdzina lanu kudzamenyana ndi chigulu cha anthuchi.+ Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+ 12  Choncho Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo pamaso pa Asa ndi Ayuda ndipo Aitiyopiyawo anayamba kuthawa.+ 13  Asa ndi anthu amene anali naye anawathamangitsa mpaka kukafika ku Gerari+ ndipo anapitiriza kupha Aitiyopiyawo moti palibe amene anatsala ndi moyo, chifukwa Yehova ndi gulu lake anawagonjetseratu. Kenako anthuwo anatenga zinthu zambiri za Aitiyopiya. 14  Iwo anawononganso mizinda yonse yozungulira Gerari chifukwa Yehova anachititsa kuti anthu amʼmizindayo akhale ndi mantha. Anatenga katundu wamʼmizinda yonseyo, chifukwa munali zinthu zambiri zoti angatenge. 15  Anakaukiranso anthu amʼmatenti okhala ndi ziweto nʼkutengamo ziweto zambiri ndi ngamila. Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mageti a zitseko ziwiriziwiri.”
Nthawi zambiri amene ankanyamula zishango zimenezi anali oponya mivi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “opinda mauta.”