2 Mbiri 15:1-19

  • Zinthu zimene Asa anasintha (1-19)

15  Tsopano mzimu wa Mulungu unafikira Azariya mwana wa Odedi.  Choncho iye anapita kukakumana ndi Asa nʼkumuuza kuti: “Tamverani mfumu Asa ndi anthu onse a fuko la Yuda ndi Benjamini. Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.+ Mukamufunafuna iye adzalola kuti mumʼpeze,+ koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.+  Kwa nthawi yaitali, Aisiraeli anakhala opanda Mulungu woona, opanda wansembe woti aziwaphunzitsa ndiponso opanda malamulo.+  Koma ali pa mavutowo, anabwerera kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli nʼkumufunafuna, ndipo iye analola kuti amupeze.+  Mʼmasiku amenewo, anthu sankayenda mwamtendere chifukwa panalibe mtendere pakati pa anthu onse okhala mʼdzikolo.  Mtundu unkamenyana ndi mtundu wina ndiponso mzinda ndi mzinda wina, chifukwa Mulungu anawasiya kuti asokonezeke ndi mavuto osiyanasiyana.+  Koma inuyo, chitani zinthu mwamphamvu ndipo musagwe ulesi,+ popeza mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.”  Asa atangomva mawu amenewa komanso ulosi wa mneneri Odedi, analimba mtima nʼkuyamba kuchotsa mafano onyansa mʼdziko lonse la Yuda+ ndi la Benjamini ndiponso mʼmizinda imene analanda mʼdera lamapiri la Efuraimu. Anabwezeretsanso guwa lansembe la Yehova limene linali patsogolo pa khonde la nyumba ya Yehova.+  Atatero anasonkhanitsa anthu onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini ndiponso alendo ambirimbiri ochokera ku fuko la Efuraimu, la Manase ndi la Simiyoni.+ Alendowa anachoka ku Isiraeli nʼkubwera kwa iye ataona kuti Yehova Mulungu wake ali naye. 10  Iwo anasonkhana ku Yerusalemu mʼmwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. 11  Pa tsiku limeneli, anapereka nsembe kwa Yehova kuchokera pa zinthu zimene anatenga kwa adani awo. Anapereka nsembe ngʼombe 700 ndi nkhosa 7,000. 12  Kuwonjezera pamenepo, anachita pangano loti adzafunafuna Yehova Mulungu wa makolo awo ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse.+ 13  Komanso kuti aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli ayenera kuphedwa, kaya ndi wamngʼono kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi.+ 14  Choncho analumbira kwa Yehova ndi mawu okweza, akufuula mosangalala komanso akuliza malipenga ndi nyanga za nkhosa. 15  Ayuda onse anayamba kusangalala chifukwa analumbira ndi mtima wawo wonse, komanso chifukwa anafunafuna Mulungu mwakhama ndipo iye analola kuti amupeze.+ Ndipo Yehova anapitiriza kuwapatsa mpumulo mʼdziko lonse.+ 16  Mfumu Asa inachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu, chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri lolambirira mzati wopatulika.*+ Asa anagwetsa fanolo ndipo analiperapera nʼkukalitentha mʼchigwa cha Kidironi.+ 17  Koma sanachotse malo okwezeka+ mu Isiraeli.+ Ngakhale zinali choncho, Asa anatumikira Mulungu ndi mtima wonse* kwa moyo wake wonse.+ 18  Iye anabweretsa kunyumba ya Mulungu woona zinthu zimene bambo ake komanso iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide ndi ziwiya zina zosiyanasiyana.+ 19  Ku Yuda sikunachitikenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ulamuliro wa Asa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Asa anali ndi mtima wathunthu.”