2 Mbiri 16:1-14
16 Mʼchaka cha 36 cha ulamuliro wa Asa, Basa+ mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda ndipo anayamba kumanganso mzinda wa Rama+ kuti ukhale wolimba. Anachita zimenezi kuti anthu asamalowe kapena kutuluka mʼdera la Asa mfumu ya Yuda.+
2 Zitatero, Asa anatenga siliva ndi golide pa chuma chamʼnyumba ya Yehova+ ndi chamʼnyumba ya mfumu nʼkutumiza kwa Beni-hadadi mfumu ya Siriya,+ amene ankakhala ku Damasiko, ndi uthenga wakuti:
3 “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe ndiponso pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Ndakutumizira siliva ndi golide. Bwera udzaphwanye pangano lako ndi Basa mfumu ya Isiraeli kuti achoke mʼdera langa.”
4 Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a asilikali ake kuti akamenyane ndi anthu amʼmizinda ya Isiraeli. Iwo analanda Iyoni,+ Dani,+ Abele-maimu ndi malo onse osungiramo zinthu a mʼmizinda ya Nafitali.+
5 Basa atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga* Rama nʼkuimitsa ntchito yake.
6 Ndiyeno Mfumu Asa inatenga Ayuda onse nʼkupita kukatenga miyala ndi matabwa za ku Rama+ zimene Basa ankamangira+ ndipo anakamangira mzinda wa Geba+ ndi wa Mizipa+ kuti mizindayi ikhale yolimba.
7 Pa nthawi imeneyo, wamasomphenya Haneni+ anapita kwa Asa mfumu ya Yuda nʼkumuuza kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya, osadalira Yehova Mulungu wanu, simunagonjetse asilikali a mfumu ya Siriya.+
8 Kodi Aitiyopiya ndi Alibiya sanali gulu la asilikali ambiri lokhala ndi magaleta ambiri ndi okwera pamahatchi ambirinso? Koma chifukwa chakuti munadalira Yehova, iye anawapereka mʼmanja mwanu.+
9 Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake* kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.*+ Mwachita zopusa pa nkhani imeneyi. Kuyambira pano mʼdziko lanu muzichitika nkhondo.”+
10 Koma Asa anakwiyira wamasomphenyayo ndipo anamuika mʼndende* popeza anamupsera mtima kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi. Pa nthawi yomweyo, Asa anayambanso kupondereza anthu ake ena.
11 Nkhani zokhudza Asa, kuyambira pa chiyambi mpaka pamapeto, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli.+
12 Mʼchaka cha 39 cha ulamuliro wake, Asa anadwala matenda a mapazi mpaka matendawo anakula kwambiri. Koma ngakhale pamene ankadwala, iye anafunafuna thandizo kwa ochiritsa osati kwa Yehova.
13 Kenako Asa, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ mʼchaka cha 41 cha ulamuliro wake.
14 Choncho anamuika mʼmanda olemekezeka kwambiri, amene iye anakumbiratu mu Mzinda wa Davide.+ Pomuika mʼmandamo, anamugoneka pachithatha pomwe anathirapo mafuta a basamu ambiri ndi mafuta apadera opangidwa posakaniza zinthu zosiyanasiyana.+ Kuwonjezera pamenepo, pamaliro ake anawotchapo zinthu zambiri zonunkhira.