2 Mbiri 17:1-19

  • Yehosafati, mfumu ya Yuda (1-6)

  • Ntchito yophunzitsa anthu (7-9)

  • Asilikali amphamvu a Yehosafati (10-19)

17  Ndiyeno mwana wake Yehosafati+ anakhala mfumu mʼmalo mwake ndipo analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli.  Iye anaika magulu a asilikali mʼmizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Anamanganso midzi ya asilikali ku Yuda ndi mʼmizinda ya Efuraimu imene Asa bambo ake analanda.+  Yehova anapitiriza kukhala ndi Yehosafati chifukwa anayenda mʼnjira za Davide kholo lake+ ndipo sanafunefune Abaala.  Chifukwa anafunafuna Mulungu wa bambo ake+ ndipo anatsatira malamulo ake, sanatsatire zochita za Aisiraeli.+  Yehova anachititsa kuti ufumuwo ukhazikike mʼmanja mwake+ ndipo Ayuda onse ankapereka mphatso kwa Yehosafati. Choncho iye anali ndi chuma chambiri ndiponso ulemerero wochuluka.+  Komanso ankatsatira njira za Yehova molimba mtima ndipo anachotsa malo okwezeka+ ndi mizati yopatulika*+ mʼdziko la Yuda.  Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wake, anaitana akalonga ake kuti aziphunzitsa mʼmizinda ya Yuda. Akalongawo anali Beni-hayili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya.  Anawaitana pamodzi ndi Alevi awa: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yehonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobi-adoniya, pamodzinso ndi Elisama ndi Yehoramu omwe anali ansembe.+  Iwo anayamba kuphunzitsa mu Yuda ndipo ankatenga buku la Chilamulo cha Yehova.+ Ankayenda mʼmizinda yonse ya Yuda nʼkumaphunzitsa anthu. 10  Yehova anachititsa kuti maufumu onse amʼmayiko ozungulira Yuda akhale ndi mantha ndipo sanamenyane ndi Yehosafati. 11  Afilisiti ankabweretsa mphatso ndi ndalama kwa Yehosafati monga msonkho. Aluya ankamubweretsera ziweto. Ankabweretsa nkhosa zamphongo 7,700 ndi atonde a mbuzi 7,700. 12  Yehosafati anapitiriza kukhala wamphamvu+ ndipo anapitiriza kumanga mipanda yolimba kwambiri+ ndiponso mizinda yosungirako zinthu+ mʼdziko la Yuda. 13  Panali zinthu zambiri zimene anachita mʼmizinda ya Yuda. Analinso ndi asilikali amphamvu ku Yerusalemu. 14  Asilikaliwa anawagawa mʼmagulu potsata nyumba za makolo awo: Adinala anali mmodzi wa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 a fuko la Yuda. Iye anali ndi asilikali amphamvu okwana 300,000.+ 15  Adinalayo ankayangʼanira Yehohanani mtsogoleri wa asilikali, yemwe anali ndi asilikali 280,000. 16  Iye ankayangʼaniranso Amasiya mwana wa Zikiri, yemwe anadzipereka kutumikira Yehova. Amasiyayo anali ndi asilikali amphamvu okwana 200,000. 17  Kuchokera ku fuko la Benjamini+ panali Eliyada, msilikali wamphamvu yemwe anali ndi asilikali 200,000 onyamula mauta ndi zishango.+ 18  Iye ankayangʼanira Yehozabadi yemwe anali ndi asilikali 180,000 okonzekera nkhondo. 19  Amenewa ankatumikira mfumu, kuwonjezera pa anthu amene mfumuyo inawaika mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri mʼdziko lonse la Yuda.+

Mawu a M'munsi