2 Mbiri 18:1-34

  • Mgwirizano wa Yehosafati ndi Ahabu (1-11)

  • Mikaya analosera zoti agonjetsedwa (12-27)

  • Ahabu anaphedwa ku Ramoti-giliyadi (28-34)

18  Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndiponso ulemerero waukulu,+ koma anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu.+  Patapita zaka, iye anapita kwa Ahabu ku Samariya.+ Ahabu anapha nkhosa ndi ngʼombe zambiri nʼkuzipereka nsembe mʼmalo mwa Yehosafati ndi anthu amene anali naye. Kenako Ahabu anayamba kunyengerera Yehosafati kuti apite kukamenyana ndi mzinda wa Ramoti-giliyadi.+  Ahabu mfumu ya Isiraeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti: “Kodi tipita limodzi ku Ramoti-giliyadi?” Iye anamuyankha kuti: “Inu ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu anu ndi amodzi ndipo tikuthandizani pa nkhondoyi.”  Koma Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, mufunsire kaye kwa Yehova.”+  Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri. Analipo amuna 400 ndipo inawafunsa kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena ndisapite?” Iwo anayankha kuti: “Pitani ndipo Mulungu woona akapereka mzindawo kwa inu mfumu.”  Kenako Yehosafati anafunsa kuti: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova?+ Ngati alipo, tiyeni tifunsirenso kwa Mulungu kudzera mwa iyeyo.”+  Mfumu ya Isiraeli inayankha Yehosafati kuti: “Patsala munthu mmodzi+ amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye, koma ndimadana naye kwambiri, chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Mfumu siyenera kulankhula choncho.”  Choncho mfumu ya Isiraeli inaitana nduna yapanyumba ya mfumu nʼkuiuza kuti: “Kamutenge Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye mwamsanga.”+  Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala pabwalo* lapageti lolowera mumzinda wa Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu ndipo aneneri onse ankalosera pamaso pawo. 10  Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndi nyanga izi mudzagunda Asiriya mpaka kuwapha onse.’” 11  Aneneri ena onse ankaloseranso zofanana ndi zimenezi. Ankanena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana.+ Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.” 12  Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Aneneri onse alankhula zabwino kwa mfumu. Nawenso ukalankhule zabwino.”+ 13  Koma Mikaya anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, zimene Mulungu angandiuze nʼzimene ndikanene.”+ 14  Kenako anafika kwa mfumu ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana ndipo mzindawo ukaperekedwa kwa inu mfumu.” 15  Ndiyeno mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti uzindiuza zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?” 16  Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika mʼmapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe mtsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mwamtendere.’” 17  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Paja ndinakuuzani kuti, ‘Sadzalosera zabwino za ine, koma zoipa.’”+ 18  Mikaya anati: “Choncho imvani mawu a Yehova: Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu+ ndipo gulu lonse lakumwamba+ linaimirira kumanja ndi kumanzere kwake.+ 19  Ndiyeno Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu mfumu ya Isiraeli, kuti apite ku Ramoti-giliyadi nʼkukafa?’ Choncho angelo osiyanasiyana ankanena maganizo awo, wina izi, wina izi. 20  Kenako mngelo*+ wina anabwera kudzaima pamaso pa Yehova nʼkunena kuti, ‘Ine ndikamʼpusitsa.’ Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukamʼpusitsa bwanji?’ 21  Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse.’ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukamʼpusitsadi ndipo zikakuyendera bwino. Pita ukachite zimenezo.’ 22  Choncho Yehova waika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anuwa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.” 23  Zedekiya+ mwana wa Kenaana anapita pomwe panali Mikaya+ nʼkumumenya mbama+ ndipo ananena kuti: “Zingatheke bwanji kuti mzimu wa Yehova undidutse nʼkukalankhula ndi iwe?”+ 24  Mikaya anayankha kuti: “Udzadziwa zimenezo tsiku limene udzalowe mʼchipinda chamkati kukabisala.” 25  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Mtengeni Mikaya mupite naye kwa Amoni mkulu wa mzinda ndi Yowasi mwana wa mfumu. 26  Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti: “Mʼtsekereni munthu uyu.+ Muzimʼpatsa chakudya chochepa ndi madzi ochepa mpaka nditabwerako mwamtendere.”’” 27  Koma Mikaya anati: “Mukakabwerakodi mwamtendere ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Ananenanso kuti: “Anthu inu, mawu angawa muwakumbukire.” 28  Zitatero mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 29  Mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha kuti ndisadziwike ndipo ndimenya nawo nkhondo. Koma inuyo muvale zovala zanu zachifumu.” Choncho mfumu ya Isiraeli inadzisintha nʼkuyamba kumenya nawo nkhondo. 30  Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaleta kuti: “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.” 31  Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Mfumu ya Isiraeli ija ndi imeneyi.” Choncho anatembenuka kuti amenyane naye ndipo Yehosafati anayamba kukuwa kuti anthu amuthandize,+ ndipo Yehova anamuthandiza. Nthawi yomweyo Mulungu anawachititsa kuti amusiye. 32  Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaletawo atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, anasiya kumuthamangitsa nʼkubwerera. 33  Koma munthu wina anaponya muvi wake chiponyeponye ndipo unakabaya mfumu ya Isiraeli pamalo olumikizira a chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti: “Bwera udzanditulutse mʼbwalo lankhondoli chifukwa ndavulala kwambiri.”+ 34  Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo ndipo mfumuyo anaiimiritsa mʼgaleta nʼkuitsamiritsa kugaletalo moyangʼanizana ndi Asiriya mpaka madzulo. Mfumuyo inafa pamene dzuwa linkalowa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “popunthira mbewu.”
Kapena kuti, “mzimu.”