2 Mbiri 19:1-11

  • Yehu anadzudzula Yehosafati (1-3)

  • Zinthu zimene Yehosafati anasintha (4-11)

19  Kenako Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera mwamtendere kunyumba kwake*+ ku Yerusalemu. 2  Ndiyeno Yehu+ mwana wa Haneni+ wamasomphenya, anapita kwa Mfumu Yehosafati ndipo anamufunsa kuti: “Kodi muyenera kuthandiza anthu oipa,+ ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana ndi Yehova?+ Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani. 3  Komabe, pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu+ chifukwa mwachotsa mizati yopatulika* mʼdzikoli ndiponso mwakonza mtima wanu kuti mufunefune Mulungu woona.”+ 4  Yehosafati anapitiriza kukhala ku Yerusalemu. Iye anapitanso kwa anthu, kuyambira ku Beere-seba mpaka kudera lamapiri la Efuraimu,+ kuti awabwezere kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.+ 5  Anaikanso oweruza mʼdziko lonselo, mumzinda ndi mzinda, ndipo anachita zimenezi mʼmizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 6  Ndiyeno anauza oweruzawo kuti: “Muzichita zinthu mosamala chifukwa simukuweruzira munthu koma Yehova, ndipo iye ali nanu pa ntchito yoweruzayi.+ 7  Muziopa Yehova+ ndipo muzisamala pochita zinthu, chifukwa Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo+ kapena watsankho,+ ndipo salandira chiphuphu.”+ 8  Ku Yerusalemu nakonso Yehosafati anaikako Alevi ena, ansembe ndi ena mwa atsogoleri a nyumba za makolo a Isiraeli, kuti akhale oweruza mʼmalo mwa Yehova ndipo aziweruza milandu ya anthu a ku Yerusalemu.+ 9  Ndiyeno anawalamula kuti: “Muzichita zotsatirazi moopa Yehova, mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse. 10  Abale anu, amene akukhala mʼmizinda yawo, akabwera ndi mlandu wokhudza kukhetsa magazi+ komanso funso lokhudza malamulo kapena ziweruzo, muziwachenjeza kuti asalakwire Yehova kuopera kuti Mulungu angakukwiyireni kwambiri inuyo ndiponso abale anuwo. Muzichita zimenezi nʼcholinga choti musapalamule mlandu. 11  Ndakupatsani wansembe wamkulu Amariya kuti azisamalira nkhani iliyonse yokhudza Yehova.+ Zebadiya mwana wa Isimaeli, mtsogoleri wa nyumba ya Yuda, aziyangʼanira nkhani iliyonse yokhudza mfumu. Ndakupatsaninso Alevi kuti azikuyangʼanirani. Khalani olimba mtima ndipo gwirani ntchitoyi. Yehova akhale ndi anthu amene azichita zabwino.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kunyumba yachifumu.”