2 Mbiri 22:1-12

  • Ahaziya, mfumu ya Yuda (1-9)

  • Ataliya analanda ufumu (10-12)

22  Kenako anthu a ku Yerusalemu anaveka ufumu Ahaziya mwana wake wamngʼono kwambiri kuti alowe mʼmalo mwake chifukwa gulu la achifwamba limene linabwera ndi Aluya kumsasa linapha ana ake onse akuluakulu.+ Choncho Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.+  Ahaziya anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu* wa Omuri.+  Ahaziya nayenso anayenda mʼnjira za anthu a mʼbanja la Ahabu+ chifukwa amayi ake ndi amene anali mlangizi wake kuti azichita zoipa.  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabu, chifukwa iwowo anakhala alangizi ake pambuyo pa imfa ya bambo ake ndipo anamʼpweteketsa.  Anatsatira malangizo awo ndipo anapita kunkhondo ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, kukamenyana ndi Hazaeli+ mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Kumeneko oponya mivi anavulaza Yehoramu.  Choncho Yehoramu anabwerera nʼkupita ku Yezereeli+ kuti akachire mabala amene anamʼvulaza ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Ahaziya* mwana wa Yehoramu+ mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu+ mwana wa Ahabu chifukwa anali atavulazidwa.*+  Koma Mulungu ndi amene anachititsa kuti Ahaziya apite kwa Yehoramu kuti akaphedwe. Atafika kumeneko, anatengana ndi Yehoramu nʼkupita kukakumana ndi Yehu+ mdzukulu* wa Nimusi, amene Yehova anamudzoza kuti aphe anthu a mʼbanja la Ahabu.+  Yehu atayamba kupereka chiweruzo kwa anthu a mʼbanja la Ahabu, anapeza akalonga a Yuda ndi ana a abale ake a Ahaziya, omwe ankatumikira Ahaziya, ndipo anawapha.+  Kenako iye anayamba kufunafuna Ahaziya ndipo anthu anakamugwira ku Samariya kumene ankabisala nʼkupita naye kwa Yehu. Atatero iwo anamupha nʼkumuika mʼmanda+ popeza anati: “Uyu ndi mdzukulu wa Yehosafati yemwe anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”+ Panalibe aliyense wa mʼbanja la Ahaziya amene akanatha kukhala mfumu ya ufumuwo. 10  Ataliya, mayi ake a Ahaziya+ ataona kuti mwana wake wafa, anapha anthu onse amene anali oyenera kulowa ufumu* wa Yuda.+ 11  Koma Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pagulu la ana aamuna a mfumu amene ankayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi ndi mayi amene ankamusamalira nʼkukamubisa mʼchipinda chamkati chogona. Yehosabati, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu,+ (ameneyu anali mkazi wa wansembe Yehoyada+ komanso mchemwali wake wa Ahaziya) anakwanitsa kubisa mwanayo kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.+ 12  Anakhala naye kwa zaka 6, atamubisa mʼnyumba ya Mulungu woona pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wamkazi.”
Mʼmipukutu ina ya Chiheberi amadziwika kuti Azariya.
Kapena kuti, “ankadwala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wamwamuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zonse za ufumu.”